Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Zephaniah 1:1-3:20
  • Zefaniya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zefaniya
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Zefaniya

ZEFANIYA

1 Mʼmasiku a Yosiya+ mwana wa Amoni+ mfumu ya Yuda, Yehova analankhula kudzera mwa Zefaniya* mwana wa Kusa, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya. Iye anati:

 2 “Ine ndidzasesa chilichonse chimene chili panthaka,” watero Yehova.+

 3 “Ndidzasesa anthu ndi nyama.

Ndidzasesa mbalame zamumlengalenga ndiponso nsomba zamʼnyanja.+

Ndidzasesanso zopunthwitsa*+ pamodzi ndi anthu oipa,

Ndipo ndidzawononga anthu onse padziko,” watero Yehova.

 4 “Ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwononga Yuda,

Ndiponso anthu onse okhala mu Yerusalemu.

Ndidzawononga chilichonse chokhudza Baala+ pamalowa.

Ndidzawononganso ansembe komanso dzina la ansembe a mulungu wachilendo.+

 5 Ndidzawononga anthu amene amakwera padenga nʼkumagwadira magulu a zinthu zakumwamba.*+

Komanso amene amagwada ndiponso kulumbira kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+

Koma nʼkumalumbiranso kuti adzakhala okhulupirika kwa Malikamu.+

 6 Ndidzawononga amene asiya kutsatira Yehova,+

Komanso amene sanafunefune Yehova kapena kufunsa malangizo kwa iye.”+

 7 Khalani chete pamaso pa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi,+

Yehova wakonza nsembe ndipo wayeretsa anthu amene wawaitana.

 8 “Pa tsiku limene Yehova adzapereke nsembe, ine ndidzaweruza akalonga,

Ana a mfumu+ ndi onse ovala zovala zachilendo.

 9 Pa tsiku limenelo ndidzaweruza aliyense amene amakwera pamalo omwe pamakhala mpando wachifumu,

Anthu amene adzaza nyumba ya ambuye awo ndi chiwawa ndiponso chinyengo.”

10 Yehova wanena kuti: “Patsiku limenelo,

Ku Geti la Nsomba+ kudzamveka phokoso la anthu,

Ndipo Kumbali Yatsopano ya mzinda kudzamveka kulira mokweza.+

Kumapiri kudzamveka phokoso la chiwonongeko.

11 Lirani mofuula inu anthu okhala ku Makitesi,*

Chifukwa amalonda onse awonongedwa.

Ndipo onse amene amayeza siliva pasikelo aphedwa.*

12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuza ndi nyale mosamala kwambiri mu Yerusalemu,

Ndipo ndidzaweruza anthu amene akukhala mosatekeseka* nʼkumaganiza kuti,

‘Yehova sadzachita zabwino kapena zoipa.’+

13 Chuma chawo chidzatengedwa ndipo nyumba zawo zidzawonongedwa.+

Iwo adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo.

Iwo adzalima minda ya mpesa koma sadzamwa vinyo wake.+

14 Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.+

Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.+

Mkokomo wa tsiku la Yehova ukubwera ndi zowawa.+

Pa tsiku limenelo msilikali adzalira.+

15 Tsiku limenelo ndi tsiku la mkwiyo,+

Tsiku la masautso ndi zowawa,+

Tsiku lowononga ndi la mphepo yamkuntho,

Tsiku la mdima wochititsa mantha,+

Tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani,+

16 Tsiku loliza lipenga ndiponso la mfuu yankhondo,+

Pochenjeza mizinda ya mipanda yolimba komanso nsanja zazitali zamʼmakona.+

17 Ndidzasautsa anthu,

Ndipo adzayenda ngati anthu osaona,+

Chifukwa iwo achimwira Yehova.+

Magazi awo adzakhuthulidwa pansi ngati fumbi,

Ndipo matumbo awo adzakhuthulidwa pansi ngati ndowe.+

18 Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+

Popeza moto wa mkwiyo wake udzawotcheratu dziko lonse lapansi,+

Chifukwa iye adzawononga anthu onse apadziko lapansi.”+

2 Sonkhanani pamodzi, ndithu sonkhanani pamodzi,+

Inu anthu a mtundu wopanda manyazi.+

 2 Lamulo lisanayambe kugwira ntchito,

Tsiku lisanadutse ngati mankhusu,*

Yehova asanakusonyezeni mkwiyo wake woyaka moto,+

Tsiku la mkwiyo wa Yehova lisanakufikireni,

 3 Funafunani Yehova,+ inu nonse ofatsa* apadziko lapansi,

Amene mumatsatira malamulo ake olungama.*

Yesetsani kukhala olungama, yesetsani kukhala ofatsa.*

Mwina mungadzabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+

 4 Gaza adzakhala mzinda wosiyidwa,

Ndipo Asikeloni adzakhala bwinja.+

Anthu a ku Asidodi adzathamangitsidwa dzuwa likuswa mtengo,*

Ndipo Ekironi adzazulidwa.+

 5 “Tsoka kwa anthu okhala mʼmbali mwa nyanja, mtundu wa Akereti.+

Yehova wakudzudzulani.

Iwe Kanani, dziko la Afilisiti, ndidzakuwononga,

Moti mʼdziko lako simudzatsala munthu aliyense.

 6 Malo amʼmbali mwa nyanja adzakhala odyetserako ziweto,

Mudzakhala zitsime za abusa ndiponso makola a nkhosa amiyala.

 7 Chigawo chimenecho chidzakhala cha anthu otsala a mʼnyumba ya Yuda.+

Ndipo iwo adzadya kumeneko.

Madzulo iwo adzagona mʼnyumba za ku Asikeloni.

Chifukwa Yehova Mulungu wawo adzawakumbukira.*

Ndipo adzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu omwe anapita ku ukapolo.”+

 8 “Ndamva kunyoza kwa Mowabu+ ndi mawu achipongwe a Aamoni,+

Amene ankanenera anthu anga nʼkumadzitama kuti alanda dziko lawo.”+

 9 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,

Mowabu adzakhala ngati Sodomu,+

Ndipo Amoni adzakhala ngati Gomora,+

Malo okhala ndi zomera zoyabwa, dothi lamchere ndiponso malo abwinja mpaka kalekale.+

Anthu anga amene adzatsale adzatenga zinthu za anthu amenewa,

Ndipo anthu amtundu wanga amene adzatsale, adzawalanda anthuwa zinthu zawo.

10 Anthu amenewo adzaona zimenezi chifukwa cha kunyada kwawo,+

Chifukwa ankanyoza anthu a Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndipo ankadzikweza pamaso pawo.

11 Yehova adzawachititsa mantha,

Chifukwa adzawononga milungu yonse yapadziko lapansi.

Ndipo zilumba zonse za anthu a mitundu ina zidzamugwadira,*+

Chilichonse pamalo ake.

12 Inunso Aitiyopiya mudzaphedwa ndi lupanga langa.+

13 Iye adzaloza dzanja lake kumpoto ndipo adzawononga Asuri.

Adzachititsa Nineve kukhala bwinja,+ kukhala dziko louma ngati chipululu.

14 Magulu a nyama kapena kuti nyama zakutchire za mitundu yonse zidzagona mumzindawo.

Nungu ndiponso mbalame ya vuwo zidzagona usiku wonse pamitu ya zipilala zamzindawo.

Pawindo padzamveka nyimbo.

Pamakomo a nyumba padzakhala zibulumwa za nyumba zakugwa,

Chifukwa iye adzachititsa kuti matabwa oyalidwa kukhoma akhale pamtunda.

15 Mzinda uwu unali wodzikuza ndipo unkakhala mosatekeseka.

Mumtima mwake unkanena kuti, ‘Ndine ndekha ndipo palibe wondiposa.’

Koma tsopano wakhala chinthu chodabwitsa,

Malo amene nyama zakutchire zimagonamo.

Aliyense wodutsa pafupi ndi mzindawu adzaimba mluzu ndipo adzapukusa mutu.”+

3 Tsoka kwa mzinda wogalukira, woipitsidwa komanso wopondereza anthu ake.+

 2 Mzindawo sunamvere+ ndipo sunalole kulangizidwa,+

Sunakhulupirire Yehova+ komanso sunayandikire Mulungu wake.+

 3 Akalonga ake ali ngati mikango yobangula.+

Oweruza ake ali ngati mimbulu imene ikuyenda usiku.

Imene pofika mʼmawa imadya chilichonse osasiya ngakhale fupa.

 4 Aneneri ake ndi amwano ndiponso achinyengo.+

Ansembe ake amaipitsa zinthu zopatulika,+

Ndipo amaphwanya malamulo.+

 5 Yehova ndi wolungama mumzindawo+ ndipo salakwitsa.

Mʼmawa uliwonse iye amadziwitsa anthu chilungamo chake,+

Moti mofanana ndi kuwala, chilungamocho sichisowa.

Koma wosalungama sachita manyazi.+

 6 “Ine ndinawononga mitundu ya anthu ndi kusakaza nsanja zawo zamʼmakona.

Ndinawononga misewu yawo moti simunkayendanso anthu.

Mizinda yawo inakhala mabwinja ndipo simunatsale munthu aliyense.+

 7 Ndiyeno ndinati, ‘Mosakayikira udzandiopa ndipo udzalola kulangizidwa,’+

Kuti iye* asawonongedwe.+

Ndidzamuimba mlandu wa zonsezi.*

Koma mʼpamene ankafunitsitsa kwambiri kuchita zoipa.+

 8 Yehova wanena kuti: ‘Choncho pitirizani kundiyembekezera,*+

Mpaka tsiku limene ndidzanyamuke kuti ndikatenge zinthu za anthu omwe ndawagonjetsa.*

Chiweruzo changa ndi choti ndisonkhanitse mitundu ya anthu, ndisonkhanitse maufumu,

Kuti ndiwasonyeze mkwiyo wanga, ndithu mkwiyo wanga wonse woyaka moto,+

Chifukwa moto wa mkwiyo wanga udzawotcheratu dziko lonse lapansi.+

 9 Pa nthawiyo ndidzasintha chilankhulo cha anthu kuti chikhale chilankhulo choyera,

Kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova,

Nʼkumamutumikira mogwirizana.’*+

10 Kuchokera kuchigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya,

Anthu amene akundichonderera, anthu anga obalalitsidwa, adzandibweretsera mphatso.+

11 Pa tsiku limenelo, sudzachita manyazi

Chifukwa cha zinthu zonse zimene unachita pondigalukira,+

Popeza ndidzachotsa anthu odzikweza pakati panu.

Ndipo sudzakhalanso wodzikweza mʼphiri langa lopatulika.+

12 Ndidzasiya anthu odzichepetsa ndi ofatsa kuti akhalebe pakati panu,+

Ndipo iwo adzapeza chitetezo mʼdzina la Yehova.

13 Aisiraeli otsala+ sadzachita zinthu zosalungama.+

Sadzalankhula bodza kapena kukhala ndi lilime lachinyengo.

Iwo adzadya ndi kugona ndipo sipadzakhala wowaopseza.”+

14 Fuula mosangalala, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni!*

Fuula chifukwa chopambana, iwe Isiraeli!+

Sangalala ndiponso kondwera ndi mtima wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!*+

15 Yehova wakuchotsera ziweruzo zake.+

Wabweza mdani wako.+

Yehova, Mfumu ya Isiraeli, ali pakati panu.+

Ndipo sudzaopanso kuti tsoka likugwera.+

16 Tsiku limenelo Yerusalemu adzauzidwa kuti:

“Usaope iwe Ziyoni,+

Ndipo manja ako asafooke.

17 Yehova Mulungu wako ali pakati panu+

Ndipo adzakupulumutsa chifukwa ndi wamphamvu.

Iye adzakondwera nawe.+

Adzakhala phee chifukwa chokhutira ndi chikondi chimene akukusonyeza,

Ndipo adzafuula mosangalala chifukwa chokondwera nawe.

18 Ndidzasonkhanitsa anthu amene akumva chisoni chifukwa chosapezeka pazikondwerero zako.+

Iwo sanali ndi iwe chifukwa anali ku ukapolo kumene ankanyozedwa.+

19 Pa nthawiyo ndidzalanga onse amene akukupondereza,+

Ndipo ndidzapulumutsa wotsimphina.+

Ndidzasonkhanitsa anthu amene anabalalitsidwa.+

Ndidzachititsa kuti akhale otchuka* komanso azitamandidwa,

Mʼdziko lonse limene anachititsidwa manyazi.

20 Pa nthawiyo ndidzakubweretsani,

Ndidzachita zimenezi pa nthawi imene ndidzakusonkhanitseni.

Ndikadzabwezeretsa iwe ukuona, anthu a mtundu wako amene anatengedwa kupita ku ukapolo,+

Ndidzachititsa kuti ukhale wotchuka* komanso uzitamandidwa,+ pakati pa anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi,” watero Yehova.

Kutanthauza “Yehova Wasunga (Kusungidwa).”

Ayenera kuti akunena zinthu zokhudza kulambira mafano.

Nʼkutheka kuti akunena za dzuwa, mwezi ndi nyenyezi.

Zikuoneka kuti imeneyi inali mbali ina ya Yerusalemu pafupi ndi Geti la Nsomba.

Mʼchilankhulo choyambirira, “awakhalitsa chete.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene adikha pansi ngati nsenga,” mkapu ya vinyo.

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.

Kapena kuti, “odzichepetsa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chiweruzo chake.”

Kapena kuti, “odzichepetsa.”

Kapena kuti, “lili paliwombo.”

Kapena kuti, “adzawasamalira.”

Kapena kuti, “zidzamulambira.”

Kutanthauza Yerusalemu.

Kapena kuti, “Ndidzamulanga chifukwa cha zonsezi.”

Kapena kuti, “kundidikirira moleza mtima.”

Mabaibulo ena amati, “ndidzanyamuke ngati mboni.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “phewa ndi phewa.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzina.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzina.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena