Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Joel 1:1-3:21
  • Yoweli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yoweli
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Yoweli

YOWELI

1 Yehova analankhula kudzera mwa Yoweli* mwana wa Petueli kuti:

 2 “Tamverani inu akulu,

Ndipo tcherani khutu inu nonse okhala mʼdzikoli.

Kodi zinthu ngati izi zinachitikapo mʼmasiku anu,

Kapena mʼmasiku a makolo anu?+

 3 Fotokozerani ana anu zinthu zimenezi.

Nawonso ana anu adzafotokozere ana awo,

Ndipo ana awowo adzafotokozerenso mʼbadwo wotsatira.

 4 Zinthu zimene ziwala zowononga zinasiya zinadyedwa ndi dzombe lambirimbiri.+

Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe opanda mapiko.

Ndipo zimene ana a dzombe opanda mapiko anasiya zinadyedwa ndi dzombe losakaza.+

 5 Dzukani zidakwa inu+ ndipo lirani.

Fuulani inu nonse okonda vinyo,

Chifukwa vinyo wotsekemera wachotsedwa pakamwa panu.+

 6 Pali mtundu umene walowa mʼdziko langa, wamphamvu ndiponso wa anthu osawerengeka.+

Mano ndiponso nsagwadwa zawo zili ngati za mikango.+

 7 Iwo awononga mtengo wanga wa mpesa ndipo asandutsa mtengo wanga wa mkuyu kukhala chitsa.

Nthambi za mitengoyi azichotsa makungwa nʼkuzitaya.

Mphukira zake azichotsanso makungwa.

 8 Lirani ngati mmene amalirira namwali amene wavala chiguduli,

Polirira mwamuna amene amafuna kumukwatira.

 9 Nsembe zambewu+ ndi nsembe zachakumwa+ sizikupezekanso mʼnyumba ya Yehova.

Ansembe omwe ndi atumiki a Yehova, akulira.

10 Munda wawonongedwa ndipo nthaka ikulira.+

Mbewu zawonongedwa, vinyo watsopano watha ndipo mafuta sakupezekanso.+

11 Alimi asokonezeka ndipo osamalira minda ya mpesa akulira mofuula,

Chifukwa cha tirigu ndi barele.

Popeza zokolola zamʼmunda zawonongeka.

12 Mtengo wa mpesa wauma,

Mtengo wa mkuyu wafota.

Mtengo wa makangaza,* wa kanjedza ndiponso wa maapozi, yonse yauma.

Mitengo yonse yamʼmunda yauma.+

Chifukwa chisangalalo cha anthu chasanduka manyazi.

13 Valani ziguduli ndipo lirani* inu ansembe.

Lirani mofuula, inu atumiki apaguwa lansembe.+

Lowani, valani ziguduli usiku wonse inu atumiki a Mulungu wanga,

Chifukwa nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa+ sizikubweranso mʼnyumba ya Mulungu wanu.

14 Lengezani nthawi yosala kudya. Itanitsani msonkhano wapadera.+

Sonkhanitsani akulu ndi anthu onse okhala mʼdzikoli,

Kuti akumane kunyumba ya Yehova Mulungu wanu+ ndipo alirire Yehova kuti awathandize.

15 Tsikulo lidzakhala lochititsa mantha.

Tsiku la Yehova lili pafupi.+

Lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

16 Kodi chakudya sichinachotsedwe ife tikuona?

Kodi kusangalala sikunachotsedwe mʼnyumba ya Mulungu wathu?

17 Mbewu* zawonongeka mafosholo ali pamwamba pake.

Nyumba zosungiramo zinthu zawonongedwa.

Nkhokwe zapasulidwa chifukwa mbewu zauma.

18 Ngakhale ziweto zikubuula.

Magulu a ngʼombe akuyendayenda mosokonezeka chifukwa palibe msipu.

Ndiponso magulu a nkhosa alangidwa.

19 Ine ndidzaitana inu Yehova,+

Chifukwa moto wawononga malo onse komwe kuli tchire lodyetserako ziweto,

Ndipo malawi amoto atentha mitengo yonse yakutchire.

20 Ngakhale zilombo zakutchire zikufuna kuti muzithandize,

Chifukwa mitsinje ya madzi yauma,

Ndipo moto wawononga malo onse komwe kuli tchire lodyetserako ziweto.”

2 “Lizani lipenga mu Ziyoni.+

Lengezani mʼphiri langa loyera kuti kukubwera nkhondo.

Anthu onse okhala mʼdzikoli anjenjemere,

Chifukwa tsiku la Yehova likubwera+ ndipo lili pafupi.

 2 Limeneli ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,+

Tsiku lamitambo ndi lamdima wandiweyani.+

Tsikuli lili ngati mmene kuwala kwa mʼbandakucha kumaonekera pamwamba pa mapiri.

Pali mtundu wa anthu ambiri ndiponso amphamvu.+

Kuyambira kalekale, palibenso mtundu wina womwe ungafanane nawo,

Ndipo sikudzakhalanso mtundu wina wofanana nawo,

Kumibadwomibadwo.

 3 Kutsogolo kwawo moto ukuwononga,

Ndipo kumbuyo kwawo malawi amoto akusakaza.+

Dziko lomwe lili patsogolo pawo lili ngati munda wa Edeni,+

Koma kumbuyo kwawo kuli chipululu,

Ndipo palibe chilichonse chingapulumuke.

 4 Mtundu wa anthuwo umaoneka ngati mahatchi,*

Ndipo amathamanga ngati mahatchi ankhondo.+

 5 Amadumphadumpha ndipo amachita mkokomo ngati magaleta oyenda pamwamba pa mapiri,+

Ndiponso ngati moto walawilawi umene ukutentha mapesi.

Ali ngati anthu amphamvu omwe ayalana pokonzekera kumenya nkhondo.+

 6 Anthu adzakhala ndi nkhawa chifukwa cha mtunduwo.

Nkhope zawo zonse zidzakhala zamantha.

 7 Amathamanga ngati asilikali.

Amakwera khoma ngati asilikali.

Aliyense amayenda mʼnjira yake,

Ndipo saphonya njira zawo.

 8 Iwo sakankhanakankhana.

Aliyense amayenda mʼnjira yake.

Wina akalasidwa nʼkugwa,

Enawo sabwerera mʼmbuyo.

 9 Iwo amathamangira mʼmizinda ndipo amathamanga pakhoma la mpanda.

Amakwera nyumba ndipo amalowera pawindo ngati mbala.

10 Dzombelo likamayenda, dziko limanjenjemera ndipo kumwamba kumagwedezeka.

Dzuwa ndi mwezi zada,+

Ndipo nyenyezi zasiya kuwala.

11 Yehova adzawalankhula asilikali ake mokweza+ chifukwa anthu amumsasa wake ndi ambiri.+

Amene akukwaniritsa mawu ake ndi wamphamvu.

Tsiku la Yehova ndi lalikulu komanso lochititsa mantha.+

Ndani angalimbe pa tsiku limeneli?”+

12 Yehova wanenanso kuti, “Tsopano bwererani kwa ine ndi mtima wonse.+

Salani kudya,+ lirani momvetsa chisoni ndiponso mokweza.

13 Ngʼambani mitima yanu,+ osati zovala zanu,+

Ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,

Chifukwa iye ndi wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga+ ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.+

Iye adzasintha maganizo okubweretserani tsoka.

14 Ndani akudziwa kuti mwina adzasintha maganizo,+

Ndipo adzakusiyirani madalitso,

Nsembe yambewu ndi nsembe yachakumwa kuti mupereke kwa Yehova Mulungu wanu?

15 Lizani lipenga mu Ziyoni.

Lengezani za nthawi yosala kudya. Itanitsani msonkhano wapadera.+

16 Sonkhanitsani anthu ndipo muyeretse mpingo.+

Sonkhanitsani amuna achikulire,* ana komanso makanda.+

Mkwati atuluke mʼchipinda chake ndipo nayenso mkwatibwi atuluke mʼchipinda chake.

17 Pakati pa khonde ndi guwa la nsembe,+

Ansembe omwe ndi atumiki a Yehova alire nʼkumanena kuti:

‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu,

Ndipo musachititse manyazi cholowa chanu,

Kuti anthu a mitundu ina awalamulire.

Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+

18 Ndiyeno Yehova adzachitira nsanje dziko lake,

Ndipo adzachitira chifundo anthu ake.+

19 Yehova adzayankha anthu ake kuti:

‘Ndikukutumizirani mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta.

Anthu inu mudzakhuta.+

Sindidzachititsanso kuti muzinyozedwa pakati pa anthu a mitundu ina.+

20 Mdani wakumpoto ndidzamuthamangitsira kutali ndi inu.

Ndidzamuthamangitsira kudziko louma komanso lopanda anthu,

Nkhope yake itayangʼana kunyanja yakumʼmawa,*

Nkhongo yake italoza kunyanja yakumadzulo.*

Fungo lake lonunkha lidzamveka,

Ndipo fungo lake loipalo lidzafalikira mʼdziko lonselo,+

Chifukwa Mulungu adzachita zinthu zazikulu.’

21 Usachite mantha iwe dziko.

Sangalala chifukwa Yehova adzachita zinthu zazikulu.

22 Inu zilombo zakutchire musachite mantha,

Chifukwa malo odyetserako ziweto kutchire adzamera msipu wobiriwira.+

Mitengo nayonso idzabereka zipatso.+

Mtengo wa mkuyu ndi mtengo wa mpesa udzabereka zipatso zambiri.+

23 Inu ana aamuna a Ziyoni sangalalani chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+

Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera,

Ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi,

Mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+

24 Malo opunthira mbewu adzadzaza ndi mbewu,

Ndipo malo opangira vinyo komanso mafuta adzasefukira.+

25 Ndidzakubwezerani mbewu za zaka zonse

Zimene dzombe, ana a dzombe opanda mapiko komanso dzombe losakaza zinadya.

Limeneli ndi gulu langa lankhondo limene ndinakutumizirani.+

26 Mudzadya nʼkukhuta,+

Ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,+

Amene wakuchitirani zodabwitsa.

Anthu anga sadzachitanso manyazi mpaka kalekale.+

27 Mudzadziwa kuti ine ndili pakati pa Isiraeli,+

Komanso kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu+ ndipo palibenso wina.

Anthu anga sadzachitanso manyazi mpaka kalekale.

28 Zimenezi zikadzachitika ndidzapereka* mzimu wanga+ kwa chamoyo chilichonse,

Ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosera.

Amuna achikulire adzalota maloto,

Ndipo anyamata adzaona masomphenya.+

29 Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi,

Ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo.

30 Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndi padziko lapansi.

Padzakhala magazi, moto ndi utsi wambiri wokwera mʼmwamba.+

31 Dzuwa lidzasanduka mdima ndipo mwezi udzasanduka magazi,+

Tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova lisanafike.+

32 Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka,+

Chifukwa mʼphiri la Ziyoni ndiponso mu Yerusalemu mudzakhala anthu opulumuka+ ngati mmene Yehova ananenera.

Anthu opulumuka amene Yehova akuwaitana.”

3 “Mʼmasiku amenewo ndiponso pa nthawiyo,

Ndikadzabwezeretsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amene anagwidwa ukapolo,+

 2 Ndidzasonkhanitsanso anthu a mitundu yonse,

Nʼkuwabweretsa mʼchigwa cha Yehosafati.*

Ndipo ndidzawaweruza kumeneko,+

Mʼmalo mwa anthu anga ndiponso cholowa changa, Isiraeli.

Chifukwa anamwaza Aisiraeli pakati pa anthu a mitundu ina,

Ndiponso anagawana dziko langa.+

 3 Ankachitira maere anthu anga.+

Ankagulitsa mnyamata kuti alipire hule,

Ndipo ankagulitsa mtsikana kuti agule vinyo woti amwe.

 4 Komanso kodi ndakulakwira chiyani

Iwe Turo ndi Sidoni ndiponso nonse amʼchigawo cha Filisitiya?

Kodi mukundichitira zimenezi pondibwezera zimene ndinachita?

Ngati mukundibwezera,

Ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+

 5 Chifukwa chakuti mwatenga siliva ndi golide wanga,+

Ndipo mwabweretsa zinthu zanga zabwino kwambiri mu akachisi anu,

 6 Komanso mwagulitsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kwa Agiriki,+

Kuti muwapititse kutali ndi dziko lawo,

 7 Choncho ndiwatenga kuti achoke kumalo amene munawagulitsa,+

Ndipo ndikubwezerani zimene munachita.

 8 Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a ku Yuda.+

Iwo adzawagulitsa kwa anthu a ku Sheba, mtundu wa anthu akutali.

Ine Yehova ndanena zimenezi.

 9 Lengezani kwa anthu a mitundu ina+ kuti:

‘Konzekerani nkhondo! Konzekeretsani amuna amphamvu!

Asilikali onse abwere nʼkuukira!+

10 Sulani makasu anu a pulawo kuti akhale malupanga, ndiponso zida zanu zosadzira mitengo kuti zikhale mikondo.

Munthu wofooka anene kuti: “Ndine wamphamvu.”

11 Inu anthu a mitundu yotizungulira, bwerani mudzathandize ndipo nonse musonkhane.’”+

Inu Yehova, bweretsani asilikali anu kumalo amenewo.

12 “Mitundu ya anthu inyamuke nʼkubwera kuchigwa cha Yehosafati,

Chifukwa ndidzakhala kumeneko kuti ndiweruze anthu a mitundu yozungulira.+

13 Yambani kumweta ndi chikwakwa, chifukwa zokolola zacha.

Bwerani nʼkuyamba kuponda chifukwa moponderamo mphesa mwadzaza.+

Malo ogweramo vinyo asefukira, chifukwa zoipa zawo zachuluka kwambiri.

14 Anthu ambirimbiri ali mʼchigwa choweruzira mlandu,

Chifukwa tsiku la Yehova layandikira mʼchigwa choweruzira mlandu.+

15 Dzuwa ndi mwezi zidzachita mdima,

Ndipo nyenyezi zidzasiya kuwala.

16 Yehova adzabangula kuchokera ku Ziyoni,

Ndipo adzalankhula mokweza ali ku Yerusalemu.

Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka.

Koma Yehova adzakhala malo othawirako a anthu ake,+

Malo achitetezo champhamvu kwa Aisiraeli.

17 Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimakhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika.+

Yerusalemu adzakhala malo opatulika,+

Ndipo anthu achilendo* sadzadutsanso mmenemo.+

18 Nthawi imeneyo mʼmapiri akuluakulu mudzatuluka vinyo wotsekemera.+

Mʼmapiri angʼonoangʼono mudzayenda mkaka.

Ndipo mʼmitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi.

Kasupe adzatuluka mʼnyumba ya Yehova,+

Ndipo adzathirira chigwa cha Mitengo ya Mthethe.

19 Koma Iguputo adzasanduka bwinja,+

Ndipo Edomu adzakhala chipululu chopanda kanthu.+

Chifukwa cha nkhanza zimene anachitira anthu a ku Yuda,+

Ndiponso chifukwa chokhetsa magazi a anthu osalakwa mʼdziko la Yudalo.+

20 Koma ku Yuda kuzidzakhala anthu nthawi zonse,

Ndipo ku Yerusalemu kudzakhala anthu mibadwomibadwo.+

21 Magazi awo amene anali ndi mlandu adzakhala opanda mlandu,+

Ndipo ine Yehova ndizidzakhala ku Ziyoni.”+

Kutanthauza “Yehova ndi Mulungu.”

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.

Kapena kuti, “dzimenyeni pachifuwa.”

Mabaibulo ena amati, “Nkhuyu zouma.”

Ena amati “mahosi.”

Kapena kuti, “akulu.”

Kutanthauza “Nyanja Yakufa.”

Kutanthauza “Nyanja ya Mediterranean.”

Kapena kuti, “ndidzatsanulira.”

Kutanthauza “Yehova ndi Woweruza.”

Kapena kuti, “ochokera kwina.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena