1 MAFUMU
1 Mfumu Davide anakalamba+ ndipo anali ndi zaka zambiri. Ankamufunditsa zofunda koma sankamva kutentha. 2 Choncho atumiki ake anamuuza kuti: “Mbuyathu mfumu, bwanji tikufunireni mtsikana yemwe ndi namwali woti azikusamalirani? Azigona pafupi nanu kuti inu mbuyathu mfumu muzimva kutentha.” 3 Ndiyeno anafufuza mtsikana wokongola mʼdziko lonse la Isiraeli. Kenako anapeza Abisagi+ wa ku Sunemu+ ndipo anabwera naye kwa mfumu. 4 Mtsikanayo anali chiphadzuwa ndipo ankasamalira mfumu. Koma mfumuyo sinagonepo naye.
5 Pa nthawi imeneyi Adoniya+ mwana wa Hagiti anayamba kudzikweza nʼkumanena kuti: “Ineyo ndikhala mfumu!” Iye anapangitsa galeta ndipo anali ndi amuna okwera pamahatchi* komanso amuna 50 oti azithamanga patsogolo pake.+ 6 Koma bambo ake sanamʼdzudzulepo* nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?” Iye analinso wooneka bwino kwambiri ndipo mayi ake anamʼbereka Abisalomu atabadwa kale. 7 Iye anagwirizana ndi Yowabu mwana wa Zeruya komanso wansembe Abiyatara+ ndipo awiriwa anayamba kumutsatira komanso kumuthandiza.+ 8 Koma wansembe Zadoki,+ Benaya+ mwana wa Yehoyada, mneneri Natani,+ Simeyi,+ Reyi ndi amuna amphamvu a Davide+ sanagwirizane ndi Adoniya.
9 Kenako Adoniya anapereka nsembe+ za nkhosa, ngʼombe komanso ana a ngʼombe onenepa pafupi ndi mwala wa Zoheleti womwe uli pafupi ndi Eni-rogeli. Anaitana azichimwene ake onse omwe anali ana a mfumu komanso amuna onse a mu Yuda omwe anali atumiki a mfumu. 10 Koma sanaitane mneneri Natani, Benaya, asilikali amphamvu a Davide ndiponso mchimwene wake Solomo. 11 Kenako Natani+ anauza Bati-seba+ mayi ake a Solomo+ kuti: “Kodi mwamva zoti Adoniya,+ mwana wa Hagiti, wakhala mfumu koma mbuye wathu Davide sakudziwa chilichonse? 12 Tsopano mvetserani malangizo amene ndikufuna kukupatsani, kuti mupulumutse moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomo.+ 13 Mupite kwa Mfumu Davide mukanene kuti, ‘Kodi si inu mbuyanga mfumu amene munalumbirira ine kapolo wanu kuti: “Solomo mwana wako ndi amene adzakhale mfumu pambuyo panga, ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu”?+ Nanga nʼchifukwa chiyani Adoniya wakhala mfumu?’ 14 Inu mukamakalankhula ndi mfumuyo, ineyo ndidzabwera kudzatsimikizira zimene mukunena.”
15 Zitatero, Bati-seba anapita kuchipinda kumene kunali mfumu. Mfumuyo inali yokalamba kwambiri ndipo Abisagi+ wa ku Sunemu ankaisamalira. 16 Bati-seba anagwada nʼkuweramira mfumu ndipo mfumuyo inati: “Ukufuna kupempha chiyani?” 17 Bati-seba anayankha kuti: “Mbuyanga, ndinu amene munalumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wanu kwa ine kapolo wanu kuti, ‘Mwana wako Solomo ndi amene adzakhale mfumu pambuyo panga ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu.’+ 18 Koma tsopano Adoniya wakhala mfumu ndipo inu mbuyanga mfumu simukudziwa chilichonse.+ 19 Iye wapereka nsembe zambiri za ngʼombe zamphongo, nyama zonenepa ndiponso nkhosa. Komanso waitana ana onse a mfumu, wansembe Abiyatara ndi Yowabu mkulu wa asilikali,+ koma mtumiki wanu Solomo sanamuitane.+ 20 Panopa maso a Aisiraeli onse ali pa inu mbuyanga mfumu, kuti muwauze amene akhale pampando wanu wachifumu pambuyo panu. 21 Mukapanda kutero, inuyo mbuyanga mfumu mukadzangogona mʼmanda mofanana ndi makolo anu, ineyo ndi mwana wanga Solomo tidzaonedwa ngati oukira.”
22 Bati-seba akulankhula ndi mfumuyo, mneneri Natani analowa.+ 23 Nthawi yomweyo anthu anauza mfumu kuti: “Kwabwera mneneri Natani!” Kenako Natani anagwada nʼkuweramira mfumuyo mpaka nkhope yake kufika pansi. 24 Ndiyeno Natani anati: “Mbuyanga mfumu, kodi munanena kuti, ‘Adoniya adzakhala mfumu pambuyo panga ndipo ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumuʼ?+ 25 Chifukwatu lero wapita kukapereka nsembe+ zambiri za ngʼombe zamphongo, nyama zonenepa ndi nkhosa. Waitananso ana onse a mfumu, atsogoleri a asilikali komanso wansembe Abiyatara.+ Moti panopa ali kumeneko ndipo akudya ndi kumwa naye nʼkumanena kuti, ‘Mfumu Adoniya ikhale ndi moyo wautali!’ 26 Koma sanaitane ineyo mtumiki wanu, wansembe Zadoki, Benaya+ mwana wa Yehoyada komanso Solomo mtumiki wanu. 27 Kodi inuyo mbuyanga mfumu mwalamula zimenezi osandidziwitsa ine mtumiki wanu, kuti ndi ndani amene adzakhale pampando wanu wachifumu pambuyo panu?”
28 Zitatero Mfumu Davide inati: “Tamuitaneni Bati-seba.” Choncho Bati-seba anabwera nʼkuima pamaso pa mfumu. 29 Mfumuyo inalumbira kuti: “Mʼdzina la Yehova amene anandipulumutsa mʼmasautso onse,+ 30 zimene ndinakulumbirira mʼdzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli kuti, ‘Mwana wako Solomo adzakhala mfumu pambuyo panga ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu mʼmalo mwanga,’ ndi zimene ndichite lero.” 31 Kenako Bati-seba anagwada nʼkuweramira mfumu mpaka nkhope yake kufika pansi ndipo ananena kuti: “Mbuyanga Mfumu Davide, mukhale ndi moyo mpaka kalekale!”
32 Nthawi yomweyo Mfumu Davide inati: “Ndiitanireni wansembe Zadoki, mneneri Natani ndi Benaya+ mwana wa Yehoyada.”+ Ndipo anthuwo anabweradi. 33 Mfumuyo inawauza kuti: “Tengani atumiki a mbuye wanu nʼkukweza Solomo mwana wanga panyulu* yanga,+ ndipo mupite naye ku Gihoni.+ 34 Kumeneko, wansembe Zadoki ndi mneneri Natani akamudzoze+ kukhala mfumu ya Isiraeli. Ndiyeno mukalize lipenga nʼkunena kuti, ‘Mfumu Solomo akhale ndi moyo wautali!’+ 35 Ndiye pobwera muzikamulondola, ndipo adzafike kuno nʼkukhala pampando wanga wachifumu. Iyeyo adzakhala mfumu mʼmalo mwanga ndipo ndidzamuika kukhala mtsogoleri wa Isiraeli ndi Yuda.” 36 Nthawi yomweyo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti: “Ame!* Yehova, Mulungu wa mbuyanga mfumu, atsimikizire zimenezi. 37 Mmene Yehova anakhalira ndi inu mbuyanga mfumu, akhalenso ndi Solomo+ ndipo achititse mpando wake wachifumu kukhala waukulu kuposa mpando wanu wachifumu, mbuyanga Mfumu Davide.”+
38 Kenako wansembe Zadoki, mneneri Natani, Benaya+ mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti+ anapita kukakweza Solomo panyulu ya Mfumu Davide+ nʼkupita naye ku Gihoni.+ 39 Ndiyeno wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta+ mutenti+ nʼkudzoza Solomo.+ Zitatero anthuwo anayamba kuliza lipenga nʼkumafuula kuti: “Mfumu Solomo akhale ndi moyo wautali!” 40 Atatero anthuwo anayamba kumulondola ndipo ankaimba zitoliro akusangalala kwambiri, moti nthaka inangʼambika chifukwa cha phokoso lawo.+
41 Adoniya ndi anthu onse amene anawaitana anamva phokosolo, ndipo anali atangomaliza kudya.+ Yowabu atangomva kulira kwa lipenga anafunsa kuti: “Kodi phokoso likumveka mumzindali ndi la chiyani?” 42 Asanamalize kulankhula, kunabwera Yonatani+ mwana wa wansembe Abiyatara. Ndipo Adoniya anati: “Lowa, iwe ndiwe munthu wabwino ndipo uyenera kuti wabweretsa nkhani yabwino.” 43 Koma Yonatani anayankha Adoniya kuti: “Ayi, si nkhani yabwino! Mbuyathu Mfumu Davide wapatsa Solomo ufumu. 44 Mfumu inatuma wansembe Zadoki, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti ndipo iwo anakweza Solomo panyulu ya mfumu.+ 45 Kenako wansembe Zadoki ndi mneneri Natani anakamudzoza ufumu ku Gihoni. Ndiyeno abwerako akusangalala ndipo mumzinda muli phokoso lokhalokha. Phokoso limenelo ndi limene munamva lija. 46 Panopa, Solomo wakhala pampando wachifumu. 47 Kuwonjezera apo, atumiki a mfumu abwera kudzafunira mafuno abwino mbuye wathu Mfumu Davide kuti: ‘Mulungu wanu akulitse dzina la Solomo kuposa dzina lanu ndiponso akweze ufumu wake kuposa ufumu wanu!’ Kenako mfumuyo inaweramitsa mutu wake ili pabedi. 48 Komanso mfumu inanena kuti, ‘Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene lero wapereka munthu woti akhale pampando wanga wachifumu, ndipo walola kuti maso anga aone zimenezi.’”
49 Anthu onse amene anaitanidwa ndi Adoniya anachita mantha ndipo ananyamuka nʼkumapita. 50 Nayenso Adoniya anachita mantha ndi Solomo. Choncho anapita kukagwira nyanga za guwa lansembe.+ 51 Solomo anauzidwa kuti: “Adoniya akuchita mantha ndi inu Mfumu Solomo moti wakagwira nyanga za guwa lansembe, ndipo wanena kuti, ‘Mfumu Solomo andilumbirire kaye ine mtumiki wake kuti sandipha ndi lupanga.’” 52 Solomo anayankha kuti: “Akamachita zabwino, tsitsi lake ngakhale limodzi silidzagwera pansi, koma akadzapezeka atachita choipa,+ adzaphedwa.” 53 Choncho Mfumu Solomo inatumiza anthu kuti akatenge Adoniya paguwa lansembe nʼkubwera naye. Kenako Adoniya analowa nʼkugwadira Mfumu Solomo. Ndiyeno Solomo anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwako.”
2 Davide atatsala pangʼono kumwalira, anapatsa mwana wake Solomo malangizo awa: 2 “Ine ndatsala pangʼono kufa, choncho iweyo uchite zinthu mwamphamvu+ ndipo ukhale wolimba mtima.+ 3 Uzimvera Yehova Mulungu wako poyenda mʼnjira zake komanso posunga malamulo ake, ziweruzo zake ndiponso zikumbutso zake mogwirizana ndi mmene anazilembera mʼChilamulo cha Mose.+ Ukatero zinthu zidzakuyendera bwino* pa zonse zimene ungachite ndiponso kulikonse kumene ungapite. 4 Komanso Yehova adzakwaniritsa zimene analonjeza zokhudza ineyo zakuti: ‘Ana ako akamadzachita zinthu mosamala komanso kuyenda mokhulupirika* pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse,+ anthu a mʼbanja lako adzapitiriza kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli.’+
5 Iweyo ukudziwa bwino zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, anapha akulu awiri a asilikali a Isiraeli, Abineri+ mwana wa Nera ndi Amasa+ mwana wa Yeteri. Iye anakhetsa magazi+ ankhondo pa nthawi yamtendere. Ndipo anadetsa ndi magazi ankhondo lamba amene anali mʼchiuno mwake ndiponso nsapato zimene zinali kuphazi kwake. 6 Iweyo uchite zinthu mogwirizana ndi nzeru zako ndipo usalole kuti imvi zake zidzapite ku Manda* mwamtendere.+
7 Koma ana a Barizilai+ wa ku Giliyadi uwasonyeze chikondi chokhulupirika. Akhale mʼgulu la anthu amene azidya patebulo lako, chifukwa anandithandiza+ pa nthawi imene ndinkathawa mchimwene wako Abisalomu.+
8 Ndiye palinso Simeyi wa ku Bahurimu, mwana wa Gera wa fuko la Benjamini. Iyeyu anandilankhula mawu onyoza kwambiri+ tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu.+ Koma atabwera kudzakumana nane pa Yorodano, ndinamulumbirira pamaso pa Yehova kuti: ‘Sindidzakupha ndi lupanga.’+ 9 Iweyo usangomusiya, umulange,+ poti ndiwe munthu wanzeru ndipo ukudziwa zimene uyenera kumuchita. Uchite zoti imvi zake zipite ku Manda* zili ndi magazi.”+
10 Kenako Davide anamwalira,* ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide.+ 11 Davide analamulira Isiraeli zaka 40. Ku Heburoni+ analamulira zaka 7, ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.+
12 Ndiyeno Solomo anakhala pampando wachifumu wa Davide bambo ake, ndipo patapita nthawi ufumu wake unakhazikika.+
13 Kenako Adoniya mwana wa Hagiti anapita kwa Bati-seba, amayi ake a Solomo ndipo iwo anamufunsa kuti: “Kodi nʼkwabwino?” Iye anayankha kuti: “Inde, nʼkwabwino.” 14 Kenako iye anati: “Ndili nanu mawu.” Ndiyeno Bati-seba anati: “Lankhulani.” 15 Adoniya anapitiriza kuti: “Inu mukudziwa kuti ufumu unayenera kukhala wanga, ndipo Aisiraeli onse ankayembekezera kuti ineyo ndikhala mfumu.+ Koma ufumuwo unatembenuka nʼkukhala wa mchimwene wanga, chifukwa Yehova ndi amene anamupatsa ufumuwo.+ 16 Koma ndikufuna kupempha chinthu chimodzi. Chonde musandikanire.” Bati-seba anamuyankha kuti: “Lankhulani.” 17 Kenako Adoniya anati: “Chonde, mukapemphe Mfumu Solomo kuti andipatse Abisagi+ wa ku Sunemu kuti akhale mkazi wanga. Ndikudziwa kuti inuyo sakakukanirani.” 18 Bati-seba atamva zimenezi anati: “Chabwino. Ndikakupempherani kwa mfumu.”
19 Choncho Bati-seba anapita kwa Mfumu Solomo kukafotokoza zomwe Adoniya anamutuma. Atangofika, Solomo anaimirira kuti akumane naye ndipo anamuweramira. Kenako anakhala pampando wake wachifumu nʼkuitanitsa mpando wina ndipo anauika kumanja kwake kuti amayi akewo akhalepo. 20 Ndiyeno Bati-seba anati: “Pali chinthu chachingʼono chimodzi chimene ndikufuna kupempha. Chonde musandikanire.” Mfumuyo inati: “Pemphani amayi, sindikukanirani.” 21 Choncho Bati-seba anapitiriza kuti: “Ndimapempha kuti Abisagi wa ku Sunemu mumupereke kwa mchimwene wanu Adoniya kuti akhale mkazi wake.” 22 Mfumu Solomo inayankha mayi akewo kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukupempha kuti Abisagi wa ku Sunemu akhale mkazi wa Adoniya? Ndiyetu mumupempherenso ufumu,+ popeza iye ndi mkulu wanga+ ndipo wansembe Abiyatara ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya+ ali kumbali yake.”
23 Kenako Mfumu Solomo analumbira pamaso pa Yehova kuti: “Mulungu andilange mowirikiza ngati Adoniya sanaike moyo wake pangozi popempha zimenezi. 24 Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, amene anandiika pampando wachifumu wa Davide bambo anga komanso amene anachititsa kuti ufumu wanga ukhazikike+ ndiponso kuti pakhale mzere wa banja lachifumu+ mogwirizana ndi zimene analonjeza, lero Adoniya aphedwa.”+ 25 Nthawi yomweyo Mfumu Solomo anatuma Benaya+ mwana wa Yehoyada kuti akaphe Adoniya ndipo anamuphadi.
26 Mfumuyo inauza wansembe Abiyatara+ kuti: “Pita kuminda yako ku Anatoti.+ Umayenera kufa, koma lero sindikupha chifukwa unanyamula Likasa la Yehova Ambuye Wamkulu Koposa pamaso pa Davide bambo anga+ ndiponso chifukwa chakuti unavutika limodzi ndi bambo anga pa nthawi yonse imene ankavutika.”+ 27 Choncho Solomo anachotsa Abiyatara kuti asatumikirenso monga wansembe wa Yehova ndipo izi zinakwaniritsa mawu amene Yehova analankhula ku Silo+ okhudza nyumba ya Eli.+
28 Yowabu atamva za nkhaniyi, anathawira kuchihema cha Yehova+ nʼkukagwira nyanga za guwa lansembe. Paja Yowabu ankatsatira Adoniya,+ koma sanatsatire Abisalomu.+ 29 Kenako Mfumu Solomo inauzidwa kuti: “Yowabu wathawira kuchihema cha Yehova ndipo ali pambali pa guwa lansembe.” Choncho Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada kuti: “Pita ukamuphe!” 30 Benaya anapitadi kuchihema cha Yehova nʼkukamuuza Yowabu kuti: “Mfumu ikuti utuluke.” Koma iye anati: “Ayi! Ndifera momʼmuno.” Ndiyeno Benaya anakauza mfumu kuti: “Yowabu wanena zimenezi, ndipo wandiyankha choncho.” 31 Mfumuyo inamuuza kuti: “Chita zimene wakuuzazo. Ukamuphe nʼkumuika mʼmanda ndipo undichotsere ineyo komanso nyumba ya bambo anga magazi amene Yowabu anakhetsa popanda chifukwa.+ 32 Yehova adzachititsa kuti magazi ake akhale pamutu pake, chifukwa anapha ndi lupanga anthu awiri olungama komanso abwino kuposa iyeyo. Anachita zimenezi Davide bambo anga osadziwa. Iye anapha Abineri+ mwana wa Nera mkulu wa asilikali a Isiraeli+ ndiponso Amasa+ mwana wa Yeteri mkulu wa asilikali a Yuda.+ 33 Magazi awo adzakhala pamutu pa Yowabu ndi pamutu pa mbadwa zake mpaka kalekale.+ Koma mtendere wochokera kwa Yehova ukhale kwa Davide, mbadwa zake, nyumba yake ndiponso mpando wake wachifumu mpaka kalekale.” 34 Kenako Benaya mwana wa Yehoyada anapita kuchihemako nʼkukapha Yowabu ndipo anaikidwa mʼmanda kunyumba kwake mʼchipululu. 35 Zitatero, mfumu inasankha Benaya+ mwana wa Yehoyada kuti akhale mkulu wa asilikali mʼmalo mwa Yowabu, ndipo inasankha wansembe Zadoki+ kuti alowe mʼmalo mwa Abiyatara.
36 Kenako mfumu inaitanitsa Simeyi+ nʼkumuuza kuti: “Umange nyumba yako ku Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko. Usadzachokeko nʼkupita kwina kulikonse. 37 Tsiku limene udzachoke nʼkudutsa chigwa cha Kidironi,+ udziwiretu kuti udzafa. Mlandu wa magazi ako udzakhala pamutu pako.” 38 Simeyi anayankha mfumu kuti: “Mwanena bwino. Ine mtumiki wanu ndichita zimene mbuyanga mfumu mwanena.” Ndipo Simeyi anakhala ku Yerusalemu masiku ambiri.
39 Koma patatha zaka zitatu, akapolo awiri a Simeyi anathawira kwa Akisi+ mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati. Kenako Simeyi anauzidwa kuti: “Akapolo anutu ali ku Gati.” 40 Nthawi yomweyo, Simeyi anakwera bulu wake nʼkupita ku Gati kwa Akisi kukafunafuna akapolo akewo. Simeyi atabwerako ku Gati ndi akapolo akewo, 41 anthu anauza Solomo kuti: “Simeyi anatuluka mu Yerusalemu kupita ku Gati ndipo wabwerako.” 42 Mfumuyo itamva zimenezi inaitanitsa Simeyi nʼkumufunsa kuti: “Kodi sindinakulumbiritse pamaso pa Yehova nʼkukuchenjeza kuti, ‘Tsiku limene udzatuluke nʼkupita kwina kulikonse, udziwiretu kuti udzafaʼ? Ndipo kodi iwe sunandiuze kuti, ‘Mwanena bwino. Ndichita zimene mwanenaziʼ?+ 43 Ndiye nʼchifukwa chiyani sunasunge lumbiro limene unapanga pamaso pa Yehova komanso lamulo limene ndinakupatsa?” 44 Kenako mfumuyo inauza Simeyi kuti: “Iweyo ukudziwa mumtima mwako zoipa zonse zimene unachitira Davide bambo anga.+ Yehova akubwezera pamutu pako zoipa zimene unachita.+ 45 Koma Mfumu Solomo idzadalitsidwa+ ndipo mpando wachifumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova mpaka kalekale.” 46 Ndiyeno mfumuyo inalamula Benaya mwana wa Yehoyada kuti aphe Simeyi ndipo anamuphadi.+
Choncho ufumu unakhazikika mʼmanja mwa Solomo.+
3 Solomo anachita mgwirizano wa ukwati ndi Farao mfumu ya Iguputo. Anakwatira mwana wamkazi wa Farao+ nʼkubwera naye mu Mzinda wa Davide,+ kuti azikhala kaye kumeneko mpaka iye atamaliza kumanga nyumba yake,+ nyumba ya Yehova+ ndiponso mpanda wa Yerusalemu.+ 2 Koma anthu ankaperekabe nsembe pamalo okwezeka,+ chifukwa pa nthawiyi nyumba ya dzina la Yehova inali isanamangidwe.+ 3 Solomo anapitiriza kukonda Yehova ndipo ankatsatira malamulo a Davide bambo ake, kungoti ankapereka nsembe zopsereza pamalo okwezeka.+
4 Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe, chifukwa kumeneko nʼkumene kunali malo okwezeka otchuka* kwambiri.+ Solomo anapereka nsembe zopsereza zokwana 1,000 paguwa lansembe.+ 5 Ku Gibiyoniko, Yehova Mulungu anaonekera kwa Solomo mʼmaloto usiku ndipo anamuuza kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikupatse.”+ 6 Solomo atamva zimenezi anati: “Inu mwasonyeza kwambiri chikondi chokhulupirika kwa mtumiki wanu Davide bambo anga, chifukwa anali wokhulupirika, wachilungamo komanso wowongoka mtima pamaso panu. Mwapitiriza kumusonyeza chikondi chimenechi mpaka pano pomupatsa mwana kuti akhale pampando wake wachifumu.+ 7 Tsopano Yehova Mulungu wanga, mwandiika ine mtumiki wanu kukhala mfumu mʼmalo mwa Davide bambo anga, ngakhale kuti ndine wamngʼono ndipo sindikudziwa zambiri.+ 8 Ine mtumiki wanu ndili pakati pa anthu anu amene mwawasankha,+ anthu ambirimbiri osatheka kuwawerenga. 9 Mundipatse ine mtumiki wanu mtima womvera kuti ndiweruze anthu anu+ komanso ndizitha kusiyanitsa zabwino ndi zoipa.+ Ndani angathe kuweruza anthu anu ambirimbiriwa?”*
10 Yehova anasangalala ndi zimene Solomo anapemphazi.+ 11 Ndiyeno Mulungu anamuuza kuti: “Popeza wapempha zimenezi ndipo sunapemphe moyo wautali, chuma, kapena kuti adani ako afe, koma wapempha kuti ukhale womvetsa zinthu kuti uzitha kuweruza milandu,+ 12 ndikupatsa zimene wapempha.+ Ndikupatsa mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu+ kuposa anthu onse amene anakhalapo mʼmbuyomu komanso amene adzakhaleko mʼtsogolo.+ 13 Ndikupatsanso zomwe sunapemphe.+ Ndikupatsa chuma ndi ulemerero,+ moti sikudzakhalanso mfumu ngati iwe pa nthawi yonse ya moyo wako.+ 14 Ndipo ukamayenda mʼnjira zanga posunga malangizo ndi malamulo anga ngati mmene Davide bambo ako anachitira,+ ndidzakupatsanso moyo wautali.”+
15 Solomo atadzuka, anazindikira kuti waona masomphenya. Kenako anapita ku Yerusalemu nʼkukaima patsogolo pa likasa la pangano la Yehova. Ndiyeno anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano+ ndipo anakonzera phwando atumiki ake onse.
16 Kenako mahule awiri anapita kwa mfumu nʼkuima patsogolo pa mfumuyo. 17 Mkazi mmodzi anati: “Mbuyanga, ine ndi mayi uyu tikukhala mʼnyumba imodzi. Ndipo ine ndinabereka mwana wamwamuna iyeyu ali mʼnyumba momwemo. 18 Patapita masiku atatu kuchokera tsiku limene ine ndinabereka mwana, nayenso anabereka mwana wamwamuna. Tinali awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe munthu wina aliyense. 19 Usiku mwana wa mayiyu anamwalira chifukwa anamutsamira. 20 Ndiyeno ine kapolo wanu ndili mʼtulo, mayiyu anadzuka pakati pa usiku nʼkutenga mwana wanga amene anali pambali panga nʼkumuika pachifuwa pake. Ndipo anatenga mwana wake wakufayo nʼkumuika pachifuwa panga. 21 Nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga, ndinapeza kuti anali wakufa. Choncho ndinamuyangʼanitsitsa mʼmawa nʼkuona kuti si mwana wanga amene ndinabereka.” 22 Koma mayi winayo anati: “Ayi, mwana wanga ndi wamoyoyu, wako ndi wakufayo!” Ndipo mayi woyamba uja ankanena kuti: “Ayi, mwana wako ndi wakufayu, wanga ndi wamoyoyo.” Iwo anapitiriza kukangana chonchi pamaso pa mfumu.
23 Kenako mfumuyo inati: “Uyu akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu, wako ndi wakufayo!’ Ndipo uyo akuti, ‘Ayi, mwana wako ndi wakufayo, wanga ndi wamoyoyu!’” 24 Ndiyeno mfumuyo inati: “Tabweretsani lupanga.” Choncho anabweretsa lupanga kwa mfumu. 25 Mfumuyo inati: “Dulani mwana wamoyoyu pakati. Mupereke hafu kwa mayi mmodzi, hafu ina kwa mayi winayo.” 26 Nthawi yomweyo mayi yemwe mwana wake anali wamoyoyo anayamba kuchonderera mfumu chifukwa chochitira chifundo mwana wakeyo. Iye anauza mfumuyo kuti: “Chonde mbuyanga, mʼpatseni mayiyu mwana wamoyoyu. Musamuphe.” Koma mayi winayo ankanena kuti: “Mwana ameneyu sakhala wanga kapena wako. Amudule pakati basi!” 27 Mfumuyo itamva zimenezi inati: “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayo. Musamuphe. Mayi ake ndi amenewa.”
28 Aisiraeli onse anamva mmene mfumu inaweruzira nkhaniyo ndipo anachita mantha ndi mfumuyo+ chifukwa anaona kuti Mulungu wamupatsa nzeru kuti aziweruza mwachilungamo.+
4 Mfumu Solomo ankalamulira Isiraeli yense.+ 2 Ndipo anthu amene anali ndi maudindo ndi awa: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe.+ 3 Elihorefi ndi Ahiya ana a Sisa anali alembi,+ ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi anali wolemba zochitika. 4 Benaya+ mwana wa Yehoyada anali mkulu wa asilikali, ndipo Zadoki ndi Abiyatara+ anali ansembe. 5 Azariya mwana wa Natani+ anali mkulu wa nduna, ndipo Zabudu mwana wa Natani anali wansembe komanso mnzake wa mfumu.+ 6 Ahisara anali woyangʼanira banja lachifumu, ndipo Adoniramu+ mwana wa Abada ankayangʼanira anthu olembedwa ntchito yokakamiza.+
7 Solomo anali ndi nduna 12 zomwe zinkayangʼanira Aisiraeli onse ndipo zinkabweretsa chakudya kwa mfumu ndi banja lake. Nduna iliyonse inkabweretsa chakudya kwa mwezi umodzi pachaka.+ 8 Mayina a ndunazo anali awa: Mwana wa Hura, ankayangʼanira kudera lamapiri la Efuraimu. 9 Mwana wa Dekeri, ankayangʼanira ku Makazi, ku Saalibimu,+ ku Beti-semesi ndi ku Eloni-beti-hanani. 10 Mwana wa Hesedi, ankayangʼanira ku Aruboti (dera lake linali Soko ndi dera lonse la Heferi). 11 Mwana wa Abinadabu ankayangʼanira kumapiri onse a Dori (kenako anakwatira Tafati mwana wa Solomo). 12 Baana mwana wa Ahiludi ankayangʼanira ku Taanaki, ku Megido+ ndi ku Beti-seani+ konse, pafupi ndi Zeretani kumunsi kwa Yezereeli, kuchokera ku Beti-seani kukafika ku Abele-mehola mpaka kuchigawo cha Yokimeamu.+ 13 Mwana wa Geberi ankayangʼanira ku Ramoti-giliyadi+ (dera lake linali midzi ingʼonoingʼono ya Yairi+ mwana wa Manase, yomwe ili ku Giliyadi.+ Analinso ndi chigawo cha Arigobi,+ chomwe chili ku Basana.+ Kunali mizinda ikuluikulu 60 yokhala ndi mipanda komanso zotchingira zakopa*). 14 Ahinadabu mwana wa Ido ankayangʼanira ku Mahanaimu.+ 15 Ahimazi ankayangʼanira kudera la Nafitali (anakwatira mwana wina wa Solomo dzina lake Basemati). 16 Baana mwana wa Husai ankayangʼanira kudera la Aseri ndi ku Bealoti. 17 Yehosafati mwana wa Paruwa ankayangʼanira kudera la Isakara. 18 Simeyi+ mwana wa Ela ankayangʼanira kudera la Benjamini.+ 19 Geberi mwana wa Uri ankayangʼanira ku Giliyadi,+ mʼdera la Sihoni+ mfumu ya Aamori ndi la Ogi+ mfumu ya Basana. Panalinso nduna imodzi yomwe inkayangʼanira nduna zonsezi mʼdzikomo.
20 Ayuda ndi Aisiraeli anachuluka kwambiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja+ ndipo ankadya, kumwa komanso kusangalala.+
21 Solomo ankalamulira maufumu onse kuyambira ku Mtsinje*+ mpaka kudziko la Afilisiti nʼkukafika kumalire ndi Iguputo. Maufumuwa ankabweretsa msonkho kwa Solomo komanso kumutumikira kwa moyo wake wonse.+
22 Chakudya cha tsiku lililonse chakunyumba yachifumu ya Solomo chinkakhala ufa wosalala wokwana miyezo 30 ya kori,* ufa wamba wokwana miyezo 60 ya kori, 23 ngʼombe 10 zodyetsera mʼkhola, ngʼombe 20 zodyetsera kutchire, nkhosa 100, mbawala zamphongo, insa, ngondo ndiponso mbalame zoweta. 24 Iye ankalamulira chilichonse kumbali yakumadzulo kwa Mtsinje,*+ kuchokera ku Tifisa mpaka ku Gaza.+ Ankalamulira mafumu onse a mbali yakumadzulo kwa Mtsinje ndipo mʼzigawo zake zonse munali mtendere.+ 25 Ayuda ndi Aisiraeli ankakhala mwamtendere. Aliyense ankakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu, kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba, masiku onse a Solomo.
26 Solomo anali ndi makola 4,000* a mahatchi okoka magaleta ake komanso mahatchi* 12,000.+
27 Nduna zinkapititsa chakudya cha Mfumu Solomo komanso anthu onse amene ankadya ndi mfumuyo. Nduna iliyonse inkapereka chakudya cha mwezi umodzi ndipo inkaonetsetsa kuti ndi chokwanira bwino.+ 28 Ndunazi zinkabweretsanso balere ndi chakudya cha mahatchi okoka magaleta ndiponso cha mahatchi ena. Zinkachipititsa kulikonse komwe chikufunika, aliyense mogwirizana ndi zomwe walamulidwa.
29 Mulungu anapatsa Solomo nzeru, luso lozindikira komanso mtima womvetsa zinthu zambirimbiri ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.+ 30 Nzeru za Solomo zinaposa nzeru za anthu onse a Kumʼmawa komanso nzeru zonse za ku Iguputo.+ 31 Iye anali wanzeru kuposa munthu aliyense. Anali wanzeru kuposa Etani+ mbadwa ya Zera ndiponso Hemani,+ Kalikoli+ ndi Darida ana a Maholi moti anatchuka mʼmitundu yonse yozungulira.+ 32 Anapeka miyambi 3,000+ ndiponso nyimbo zokwana 1,005.+ 33 Ankafotokoza za mitengo, kuyambira mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kamtengo ka hisope+ kamene kamamera pakhoma. Ankafotokozanso za zinyama,+ mbalame,+ nyama zokwawa*+ ndiponso nsomba. 34 Anthu ochokera mʼmitundu yonse ankabwera kudzamva nzeru za Solomo, ngakhalenso mafumu onse apadziko lapansi amene anamva za nzeru zake.+
5 Hiramu, mfumu ya ku Turo,+ atamva kuti Solomo wadzozedwa kukhala mfumu mʼmalo mwa bambo ake, anatuma atumiki ake kuti apite kwa Solomo popeza Hiramuyo anali mnzake wa Davide.+ 2 Kenako Solomo anatumiza uthenga kwa Hiramu wakuti:+ 3 “Inuyo mukudziwa bwino kuti Davide bambo anga sanathe kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo zimene adani ake ankamenyana naye mʼmadera onse omuzungulira, mpaka pamene Yehova anamuthandiza kugonjetsa adani akewo.*+ 4 Koma panopa Yehova Mulungu wanga wandipatsa mpumulo moti adani anga onse ondizungulira sakumenyana nane.+ Palibe aliyense amene akulimbana nane komanso palibe choipa chilichonse chimene chikuchitika.+ 5 Choncho ndikuganiza zomanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga, mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza Davide bambo anga kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamuike pampando wako wachifumu mʼmalo mwa iweyo, ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 6 Ndiye lamulani anthu anu kuti andidulire mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+ Antchito anga azidzagwira ntchito limodzi ndi antchito anu ndipo ndidzalipira antchito anu mogwirizana ndi malipiro amene munganene. Inuyo mukudziwa kuti pakati pathu palibe odziwa kudula mitengo ngati Asidoni.”+
7 Hiramu atamva zimene Solomo ananenazi, anasangalala kwambiri ndipo anati: “Yehova atamandike lero chifukwa wapereka kwa Davide mwana wanzeru woti alamulire anthu ochulukawa.”+ 8 Choncho Hiramu anatumiza uthenga kwa Solomo wakuti: “Ndamva uthenga wanu. Ndichita zonse zimene mukufuna ndipo ndikupatsani mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ya junipa.*+ 9 Antchito anga adzainyamula ku Lebanoni nʼkupita nayo kunyanja, ndipo ndidzaimanga pamodzi ngati phaka nʼkuiyandamitsa panyanja kuti ikafike kumalo kumene mudzandiuze. Kenako akaimasula ndipo inuyo mukaitengera kumeneko. Malipiro ake mudzandipatsa chakudya cha banja langa.”+
10 Choncho Hiramu anapereka kwa Solomo mitengo ya mkungudza ndiponso mitengo ina yofanana ndi mkungudza imene Solomo ankafuna. 11 Ndipo Solomo anapereka kwa Hiramu tirigu wokwana miyezo 20,000 ya kori,* kuti chikhale chakudya cha banja lake, ndiponso mafuta a maolivi oyenga bwino okwana miyezo 20 ya kori. Zinthu zimenezi ndi zomwe Solomo ankapereka kwa Hiramu chaka chilichonse.+ 12 Ndiyeno Yehova anapatsa Solomo nzeru mogwirizana ndi zimene anamulonjeza.+ Pakati pa Hiramu ndi Solomo panali mtendere ndipo awiriwa anachita pangano.
13 Mfumu Solomo inalemba amuna kuchokera ku Isiraeli konse kuti azigwira ntchito yokakamiza, ndipo anthu amene anawalembawo analipo 30,000.+ 14 Inkawatumiza ku Lebanoni mʼmagulu a anthu 10,000 pamwezi. Anthuwo ankakhala mwezi umodzi ku Lebanoni ndipo miyezi iwiri ankakhala kwawo. Adoniramu+ ndi amene ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yokakamizawo. 15 Solomo anali ndi anthu 70,000 onyamula katundu ndiponso anthu 80,000 osema miyala+ kumapiri.+ 16 Solomo analinso ndi nduna 3,300+ zomwe zinkayangʼanira anthu ogwira ntchito. 17 Ndiyeno mfumuyo inalamula kuti aseme miyala ikuluikulu yokwera mtengo,+ kuti akamange maziko+ a nyumbayo ndi miyala yosema.+ 18 Choncho amisiri omanga a Solomo ndi amisiri omanga a Hiramu ndiponso anthu a ku Gebala+ anasema miyalayo, ndipo anadula mitengo komanso kusema miyala pokonzekera kumanga nyumbayo.
6 Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova*+ mʼchaka cha 480 kuchokera pamene Aisiraeli anatuluka mʼdziko la Iguputo,+ mwezi wa Zivi*+ (womwe ndi mwezi wachiwiri). Ichi chinali chaka cha 4 kuchokera pamene Solomoyo anakhala mfumu ya Isiraeli. 2 Nyumba imene Mfumu Solomo inamangira Yehova, inali mikono* 60 mulitali, mikono 20 mulifupi ndiponso mikono 30 kupita mʼmwamba.+ 3 Khonde+ lakutsogolo kwa kachisi* linali mikono 20 mulitali ndipo linkafanana ndi mulifupi mwa nyumbayo. Khondelo linali kutsogolo kwa nyumbayo ndipo linali mikono 10 mulifupi.
4 Mawindo a nyumbayo anali aakulu mkati, aangʼono kunja.+ 5 Komanso anamanga zipinda kuzungulira khoma lonse la nyumbayo, kuzungulira makoma onse akunja a kachisi* ndi chipinda chamkati.+ Anamanganso zipinda zamʼmbali zosanjikizana kuzungulira nyumbayo.+ 6 Chipinda chamʼmbali chapansi chinali mikono 5 mulifupi mwake, chapakati chinali mikono 6 mulifupi mwake ndipo chachitatu chinali mikono 7 mulifupi mwake. Makoma onse akunja a nyumbayo anangowagoba nʼcholinga choti asawaboole.+
7 Nyumbayo anaimanga ndi miyala yosema kale,+ ndipo phokoso la hamala, nkhwangwa kapena zida zilizonse zachitsulo silinkamveka pamene ankaimanga. 8 Khomo lolowera kuchipinda chamʼmbali chapansi linali kumʼmwera* kwa nyumbayo,+ ndipo ankakwera masitepe oyenda mokhotakhota kukafika kuchipinda chapakati, kenako kukafika kuchipinda chachitatu. 9 Anapitiriza kumanga nyumbayo mpaka kuimaliza.+ Denga la nyumbayo analipanga ndi matabwa komanso mitengo ya mkungudza.+ 10 Anamanga zipinda zamʼmbali zosanjikizana kuzungulira nyumbayo+ ndipo chipinda chilichonse chinali chachitali mikono 5. Zipindazo anazilumikiza kunyumbayo ndi matabwa a mkungudza.
11 Pa nthawiyo, Yehova anauza Solomo kuti: 12 “Ponena za nyumba ukumangayi, ukamatsatira malamulo anga ndiponso kusunga ziweruzo zanga zonse,+ inenso ndidzakwaniritsa zimene ndinalonjeza Davide bambo ako.+ 13 Komanso ndidzakhala pakati pa Aisiraeli+ ndipo sindidzasiya Aisiraeli, omwe ndi anthu anga.”+
14 Solomo anapitiriza kumanga nyumbayo mpaka kuimaliza. 15 Makoma a mkati mwa nyumbayo anawamanga ndi matabwa akuluakulu a mkungudza. Mkati mwa nyumbayo, kuchokera pansi mpaka kudenga anakutamo ndi matabwa. Komanso pansi pa nyumbayo anaikapo matabwa akuluakulu a mitengo ya junipa.*+ 16 Anagawanso chipinda cha mikono 20 kumbuyo kwa nyumbayo pogwiritsa ntchito matabwa akuluakulu a mkungudza, kuchokera pansi mpaka kudenga. Ndipo mʼchipindamo anamangamo chipinda chamkati+ chotchedwa Malo Oyera Koposa.+ 17 Komanso kachisi,*+ yemwe anali mbali ya nyumbayi ndipo anali kutsogolo kwake, kutalika kwake kunali mikono 40. 18 Pamatabwa a mkungudza a mkati mwa nyumbayo anajambulapo mochita kugoba zokongoletsera zooneka ngati zipanda+ ndiponso maluwa.+ Mkati monse munali matabwa a mkungudza ndipo simunkaoneka mwala uliwonse.
19 Iye anakonza chipinda chamkati+ cha nyumbayo kuti aikemo likasa la pangano la Yehova.+ 20 Chipinda chamkaticho chinali mikono 20 mulitali, mikono 20 mulifupi ndi mikono 20 kupita mʼmwamba.+ Chipindachi anachikuta ndi golide woyenga bwino, komanso anakuta guwa lansembe+ ndi matabwa a mkungudza. 21 Solomo anakuta mkati mwa nyumba yonseyo ndi golide woyenga bwino.+ Kutsogolo kwa chipinda chamkati+ anaikako matcheni agolide ndipo anakuta chipindacho ndi golide. 22 Nyumba yonseyo anaikuta ndi golide mpaka kuimaliza, ndipo guwa lansembe lonse, lomwe linali pafupi ndi chipinda chamkati, analikuta ndi golide.+
23 Mʼchipinda chamkati Solomo anapangamo akerubi awiri+ pogwiritsa ntchito mtengo wa paini.* Kerubi aliyense anali wamtali mikono 10.+ 24 Phiko limodzi la kerubi linali lalitali mikono 5 ndipo phiko lina, linalinso lalitali mikono 5. Kuchokera kunsonga kwa phiko kukafika kunsonga kwa phiko lina kutalika kwake kunali mikono 10. 25 Kerubi wachiwiri analinso wamtali mikono 10. Akerubiwa anali ofanana kukula kwake ndiponso kapangidwe kake. 26 Kerubi mmodzi anali wamtali mikono 10, chimodzimodzinso winayo. 27 Kenako akerubiwo+ anawaika mʼchipinda chamkati.* Mapiko awo anali otambasula moti phiko la kerubi mmodzi linagunda khoma ndipo phiko la kerubi wina linagundanso khoma lina. Mapiko awo anafika pakati pa nyumbayo, ndipo anagundana. 28 Solomo anakuta akerubiwo ndi golide.
29 Pamakoma onse a nyumbayo a zipinda zonse ziwiri, zomwe ndi Malo Oyera Koposa komanso Malo Oyera, anajambulapo mochita kugoba akerubi,+ mitengo ya kanjedza+ ndi maluwa.+ 30 Pansi pa zipinda ziwirizo anakutapo ndi golide. 31 Pakhomo la chipinda chamkati anaikapo zitseko za mtengo wa paini, zipilala zamʼmbali ndiponso mafelemu, ngati mbali ya 5. 32 Zitseko ziwirizo zinali zamatabwa a mtengo wa paini ndipo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza ndi maluwa. Zitsekozo anazikuta ndi golide. Akerubi ndi mitengo ya kanjedza zomwe anazilemba mochita kugoba pazitsekozo anazikutanso ndi golide. 33 Anapanganso chimodzimodzi ndi khomo la kachisi,* pamafelemu ake a mtengo wa paini omwe anali mbali ya 4. 34 Anapanga zitseko ziwiri zamatabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza. Chitseko choyamba chinali ndi mbali ziwiri ndipo hafu inkatsegukira mbali ina, hafu ina inkatsegukira mbali ina. Chitseko chachiwiri chinalinso ndi mbali ziwiri ndipo hafu inkatsegukira mbali ina, hafu ina inkatsegukira mbali ina.+ 35 Pazitsekopo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza komanso maluwa ndipo anakuta zojambulazo ndi golide.
36 Anamanga bwalo lamkati+ la mizere itatu ya miyala yosema komanso mzere umodzi wa matabwa a mkungudza.+
37 Mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Solomo, mwezi wa Zivi,* anamanga maziko a nyumba ya Yehova.+ 38 Ndipo mʼchaka cha 11, mwezi wa Buli,* (womwe ndi mwezi wa 8), anamaliza zinthu zonse panyumbayo mogwirizana ndi pulani yake.+ Choncho Solomo anamanga nyumbayo zaka 7.
7 Panatenga zaka 13 kuti Solomo amange nyumba* yake+ nʼkuimaliza.+
2 Kenako anamanga nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+ Nyumbayi inali mikono* 100 mulitali, mikono 50 mulifupi ndiponso mikono 30 kupita mʼmwamba. Anaimanga pamwamba pa nsanamira za mtengo wa mkungudza.+ Nsanamirazo zinali mʼmizere 4 ndipo pamwamba pake anaikapo mitengo ya mkungudza. 3 Nyumbayi anaikuta ndi matabwa a mkungudza kuyambira pazitsulo zimene zinali pamwamba pa nsanamira. Zinalipo 45 ndipo pamzere uliwonse panali 15. 4 Nyumbayi inali yosanja kawiri. Nsanjika iliyonse inali ndi mzere wa mawindo. Choncho nyumba yonseyo inali ndi mizere itatu ya mawindo okhala ndi mafelemu. Mawindo a mbali ina anayangʼanizana ndi mawindo a mbali inanso ya nyumbayo. 5 Makomo komanso mafelemu a nyumbayo anali ofanana mbali zonse 4 ndipo ndi mmene zinalilinso ndi mawindo onse amʼmizere itatu ya nyumbayo.
6 Kenako anamanga Khonde la Zipilala. Mulitali mwake linali mikono 50 ndipo mulifupi linali mikono 30. Kutsogolo kwa khondelo kunalinso kakhonde kena kokhala ndi zipilala ndi denga.
7 Anamanganso Bwalo la Mpando Wachifumu,+ kumene ankaweruzira milandu. Bwaloli linkatchedwa Bwalo Loweruzira Milandu.+ Makoma ake anawakuta ndi matabwa a mkungudza kuyambira pansi mpaka kudenga.
8 Kenako Solomo anamanga nyumba* yake yokhalamo chapatali ndi nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu.+ Kamangidwe ka nyumbayi kanali kofanana ndi ka nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu. Solomo anamanganso nyumba ina yofanana ndi Bwaloli ndipo anamangira mwana wamkazi wa Farao amene iye anamʼkwatira.+
9 Nyumba zonsezi, kuyambira pamaziko ake mpaka pamwamba pa khoma, ndiponso kuchokera panja pa nyumbazo mpaka kubwalo lalikulu,+ zinamangidwa ndi miyala yokwera mtengo+ yochita kuyeza ndiponso yocheka ndi macheka a miyala, mkati ndi kunja komwe. 10 Maziko ake anawamanga ndi miyala ikuluikulu yokwera mtengo ndipo miyala ina inali yaikulu mikono 10, ina mikono 8. 11 Pamwamba pa miyala ya mazikoyo panalinso miyala ina yokwera mtengo yochita kuyeza ndiponso yosema. Panalinso matabwa a mkungudza. 12 Bwalo lalikulu linazunguliridwa ndi khoma la miyala yosema lotalika mizere itatu kuchokera pansi ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza pamwamba pake. Ndi mmenenso zinalili ndi bwalo lamkati+ la nyumba ya Yehova komanso khonde la nyumbayo.+
13 Mfumu Solomo anatuma anthu kuti akatenge Hiramu+ ku Turo. 14 Mayi ake anali mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali. Bambo ake anali a ku Turo odziwa kupanga zinthu zakopa.*+ Hiramu anali waluso, womvetsa zinthu+ ndiponso wodziwa bwino ntchito yopanga zinthu zakopa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomo ndipo anamugwirira ntchito yake yonse.
15 Anaumba zipilala ziwiri zakopa.+ Chipilala chilichonse chinali chachitali mikono 18, ndipo kuzungulira chipilala chilichonse inali mikono 12.+ 16 Anapanga mitu iwiri yakopa nʼkuiika pamwamba pa zipilalazo. Mutu umodzi unali wautali mikono 5, ndipo mutu winawo unalinso wautali mikono 5. 17 Pamutu wa chipilala chilichonse anaikapo maukonde opangidwa ndi matcheni opotanapotana.+ Pamutu wina anaikapo ukonde wopangidwa ndi matcheni 7 ndipo pamutu winawo anaikaponso ukonde wopangidwa ndi matcheni 7. 18 Kenako anapanga mizere iwiri ya makangaza* kuzungulira maukonde awiri aja, nʼkuveka mitu imene inali pamwamba pa zipilalazo. Anachita zimenezi pamitu yonse iwiri. 19 Mbali yokwana mikono 4 ya mitu imene inali pamwamba pa zipilala, pafupi ndi khonde, anaipanga ngati maluwa. 20 Mitu iwiriyo inali pamwamba pa zipilala komanso pamwamba pa malo ozungulira amene analumikizira maukonde aja. Kuzungulira mutu uliwonse, panali makangaza 200 amene anali mʼmizere.+
21 Ndiyeno Hiramu anaika zipilala zija pakhonde la kachisi.*+ Chipilala chimodzi anachiika mbali yakumanja* nʼkuchipatsa dzina lakuti Yakini.* Chipilala china anachiika mbali yakumanzere* nʼkuchipatsa dzina lakuti Boazi.*+ 22 Pamwamba pa chipilala chilichonse panali pooneka ngati maluwa. Choncho, anamaliza ntchito yopanga zipilalazo.
23 Kenako iye anapanga thanki yosungira madzi.*+ Thankiyo inali yozungulira ndipo inali mikono 10 kuchokera mbali ina kufika ina, kuyeza modutsa pakati. Thankiyo inali yaitali mikono 5 ndipo kuzungulira thanki yonseyo inali mikono 30.+ 24 Kuzungulira mʼkhosi mwake monse munali zokongoletsera zooneka ngati zipanda.+ Pamalo alionse otalika mkono umodzi ankaikapo zokongoletsera 10. Zokongoletsera zooneka ngati zipandazo zinalipo mizere iwiri, ndipo anaziumbira kumodzi ndi thankiyo. 25 Thankiyo anaikhazika pangʼombe zamphongo 12.+ Ngʼombe zitatu zinayangʼana kumpoto, zitatu zinayangʼana kumadzulo, zitatu zinayangʼana kumʼmwera ndipo zitatu zinayangʼana kumʼmawa. Thankiyo inali pamwamba pa ngʼombezo ndipo mbuyo zonse za ngʼombezo zinaloza pakati. 26 Kuchindikala kwa thankiyo kunali chikhatho* chimodzi. Milomo yake inali ngati kukamwa kwa mphika kapena ngati maluwa. Muthankiyo munkalowa madzi okwana mitsuko* 2,000.
27 Kenako anapanga zotengera 10+ zakopa zokhala ndi mawilo. Chotengera chilichonse chinali mikono 4 mulitali, mikono 4 mulifupi komanso mikono itatu kupita mʼmwamba. 28 Zotengerazo anazipanga chonchi: Mʼmbali mwake zinali zamalata ndipo malatawo anali pakati pa zitsulo zopingasana. 29 Pamalata amene anali pakati pa zitsulo zopingasana anajambulapo mikango,+ ngʼombe zamphongo ndiponso akerubi.+ Pazitsulo zopingasana anajambulaponso zinthu zimenezi. Pamwamba ndi pansi pa mikango ndi ngʼombe zamphongozo, anajambulapo nkhata zamaluwa. 30 Chotengera chilichonse chinali ndi mawilo 4 akopa ndiponso mapaipi akopa olumikiza mawilo. Mʼmakona 4 a chotengeracho munali zogwiriziza mawilo ndi mapaipiwo. Pansi pa beseni panalinso zogwiriziza ndipo anazipangira kumodzi ndi nkhata zamaluwa pafupi ndi chogwiriziza chilichonse. 31 Besenilo linali mkati mwa mbali yapamwamba ya chotengeracho ndipo kuchoka pansi kufika mumkombero linali mkono umodzi. Pakamwa pake panali pozungulira ndipo tikaphatikiza ndi mkomberowo, beseni lonse linali lalitali mkono umodzi ndi hafu. Mʼmbali mwa pakamwa pake anajambulamo zokongoletsera mochita kugoba. Malata amʼmbali mwake anali a mbali 4 zofanana, osati ozungulira. 32 Pansi pa malata a mʼmbaliwo panali mawilo 4. Zogwiriziza za mawilowo anazilumikiza ku chotengeracho ndipo wilo lililonse linali lalitali mkono umodzi ndi hafu. 33 Mawilowo anawapanga ngati mawilo a galeta. Zogwiriziza zake, malimu ake,* masipoko ake ndiponso mahabu ake, zonse zinali zakopa. 34 Chotengera chilichonse chinali ndi makona 4, ndipo pakona iliyonse panali chogwiriziza. Zogwirizizazo anaziumbira kumodzi ndi chotengeracho. 35 Pamwamba pa chotengeracho panali chokhazikapo beseni chozungulira. Chinali chachitali hafu ya mkono. Chokhazikapo besenicho chinali chozungulira, ndipo kutalika kwake kunali hafu ya mkono kuchokera pansi kufika pamwamba. Timafelemu take komanso malata ake amʼmbali anazipangira kumodzi ndi chotengeracho. 36 Patimafelemuto ndiponso pamalata amʼmbaliwo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mikango komanso mitengo ya kanjedza mogwirizana ndi kukula kwa malo ake. Anajambulanso nkhata zamaluwa kuzungulira chokhazikapo besenicho.+ 37 Umu ndi mmene anapangira zotengera 10 zonsezo.+ Zinali zofanana kaumbidwe kake,+ kukula kwake ndiponso maonekedwe ake.
38 Kenako anapanga mabeseni 10 akopa.+ Mʼbeseni lililonse munkalowa madzi okwana mitsuko 40, ndipo linali mikono 4 kuchokera mbali ina kufika mbali ina. Pa zotengera 10 zija, chilichonse chinali ndi beseni lake. 39 Anaika zotengera 5 mbali yakumanja kwa nyumbayo komanso zotengera 5 mbali yakumanzere. Thanki ija anaiika kumanja kwa nyumbayo, kumʼmwera chakumʼmawa.+
40 Hiramu+ anapanganso mabeseni, mafosholo+ ndi mbale zolowa.+
Choncho iye anamaliza ntchito yonse imene ankagwirira Mfumu Solomo yopanga zinthu zotsatirazi panyumba ya Yehova:+ 41 zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yooneka ngati mbale zolowa imene anaiika pamwamba pa zipilala ziwirizo ndi maukonde awiri+ okutira mitu iwiri imene inali pamwamba pa zipilalazo. 42 Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja ndipo panali mizere iwiri ya makangaza pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yooneka ngati mbale zolowa imene inali pazipilala ziwiri zija. 43 Anapanganso zotengera 10,+ mabeseni 10+ oika pazotengerazo, 44 thanki+ imodzi, ngʼombe zamphongo 12 zokhala pansi pa thankiyo, 45 ndowa, mafosholo, mbale zolowa ndi ziwiya zina zonse. Hiramu anapanga zinthu zimenezi ndi kopa wonyezimira kuti Mfumu Solomo aziike mʼnyumba ya Yehova. 46 Mfumuyo inaumba zinthu zimenezi mʼzikombole zadongo mʼchigawo cha Yorodano, pakati pa Sukoti ndi Zeretani.
47 Solomo sanayeze kulemera kwa ziwiya zonse chifukwa zinali zambiri. Kopayo sanadziwike kulemera kwake.+ 48 Solomo anapanga zinthu zonse zapanyumba ya Yehova. Anapanga guwa lansembe+ lagolide komanso tebulo yagolide+ yoikapo mkate wachionetsero. 49 Anapanganso zoikapo nyale+ zagolide woyenga bwino ndipo anaziika pafupi ndi chipinda chamkati, anaika 5 kumanja, 5 kumanzere. Ndiponso anapanga maluwa agolide,+ nyale zagolide, zopanira zagolide zozimitsira nyale,+ 50 mabeseni, zozimitsira nyale,+ mbale zolowa, makapu+ ndiponso zopalira moto.+ Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. Anapanganso molowa miyendo ya zitseko za chipinda chamkati,+ kutanthauza Malo Oyera Koposa ndiponso molowa miyendo ya zitseko za nyumbayo.+ Zonsezi zinali zagolide.
51 Choncho Mfumu Solomo anamaliza ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova imene anayenera kugwira. Kenako Solomo anabweretsa zinthu zimene bambo ake Davide anaziyeretsa.+ Anatenga siliva, golide ndiponso zinthu zina nʼkuziika mosungira chuma chapanyumba ya Yehova.+
8 Pa nthawi imeneyo Solomo anasonkhanitsa+ akulu a Isiraeli, atsogoleri a mafuko ndiponso atsogoleri a nyumba za makolo a Aisiraeli.+ Anabwera kwa Mfumu Solomo ku Yerusalemu kuti akatenge likasa la pangano la Yehova ku Mzinda wa Davide,+ komwe ndi ku Ziyoni.+ 2 Amuna onse a mu Isiraeli anasonkhana kwa Mfumu Solomo pachikondwerero* mʼmwezi wa Etanimu,* womwe ndi mwezi wa 7.+ 3 Choncho Akulu onse a Isiraeli anabwera ndipo ansembe ananyamula Likasa.+ 4 Iwo ananyamula Likasa la Yehova, chihema chokumanako+ komanso zinthu zonse zopatulika zimene zinali mʼchihemacho. Ansembe ndi Alevi anabweretsa zinthuzi. 5 Mfumu Solomo ndi gulu lonse la Aisiraeli amene anawaitana, anasonkhana patsogolo pa Likasa. Iwo anapereka nsembe+ zosawerengeka za nkhosa ndi ngʼombe.
6 Kenako ansembe anabweretsa likasa la pangano la Yehova pamalo ake,+ kuchipinda chamkati cha nyumbayo, chomwe ndi Malo Oyera Koposa, ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+
7 Choncho mapiko a akerubiwo anali pamwamba pa Likasa, moti akerubiwo anatchinga pamwamba pa Likasalo ndi mitengo yake yonyamulira.+ 8 Mitengo yonyamulirayo+ inali yaitali moti nsonga zake zinkaonekera ku Malo Oyera kutsogolo kwa chipinda chamkati, koma sizinkaonekera panja. Mitengoyo idakali pomwepo mpaka lero. 9 Mu Likasalo munalibe chinthu china chilichonse kupatulapo miyala iwiri yosema+ imene Mose anaikamo+ ku Horebe. Anaiikamo pa nthawi imene Yehova anachita pangano+ ndi Aisiraeli, pamene ankachoka mʼdziko la Iguputo.+
10 Ansembe atatuluka mʼmalo oyera, mtambo+ unadzaza nyumba ya Yehova.+ 11 Chifukwa cha mtambowo, ansembewo analephera kutumikira popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehovayo.+ 12 Pa nthawiyo Solomo ananena kuti: “Yehova anati adzakhala mumdima wandiweyani.+ 13 Ine ndakwanitsa kukumangirani nyumba yapamwamba yomwe ndi malo okhazikika oti muzikhalamo mpaka kalekale.”+
14 Kenako mfumu inatembenuka nʼkuyamba kudalitsa gulu lonse la Aisiraeli. Apa nʼkuti Aisiraeli onsewo ataimirira.+ 15 Mfumuyo inati: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene ndi pakamwa pake analonjeza bambo anga Davide ndipo ndi dzanja lake wakwaniritsa zimene ananena zakuti, 16 ‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga Aisiraeli mʼdziko la Iguputo, sindinasankhe mzinda mʼmafuko onse a Isiraeli womangako nyumba ya dzina langa kuti likhale kumeneko.+ Koma ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisiraeli.’ 17 Ndipo bambo anga Davide ankafunitsitsa kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 18 Koma Yehova anauza Davide bambo anga kuti, ‘Unkafunitsitsa kumanga nyumba ya dzina langa ndipo unachita bwino kulakalaka utachita zimenezi. 19 Koma iweyo sumanga nyumbayi, mʼmalomwake mwana wamwamuna amene udzabereke* ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.’+ 20 Yehova wakwaniritsa zimene analonjeza, chifukwa ndalowa mʼmalo mwa bambo anga Davide ndipo ndakhala pampando wachifumu wa Isiraeli, mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza. Komanso ndamanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 21 Ndiponso mʼnyumbamo ndakonzamo malo oika Likasa, lomwe muli pangano+ limene Yehova anapangana ndi makolo athu pamene ankawachotsa mʼdziko la Iguputo.”
22 Kenako Solomo anaimirira pafupi ndi guwa lansembe la Yehova kutsogolo kwa Aisiraeli onse ndipo anakweza manja ake mʼmwamba.+ 23 Atatero anati: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, palibe Mulungu wina wofanana ndi inu+ kumwambako kapena pansi pano. Mumasunga pangano komanso mumasonyeza chikondi chokhulupirika+ kwa anthu amene amakutumikirani ndi mtima wawo wonse.+ 24 Mwakwaniritsa lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga. Munalonjeza ndi pakamwa panu ndipo lero mwakwaniritsa ndi dzanja lanu.+ 25 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, mukwaniritse lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a mʼbanja lako sadzasiya kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli. Chofunika nʼchakuti ana ako asamale mayendedwe awo poyenda mokhulupirika mʼnjira zanga ngati mmene iwe wachitira.’+ 26 Ndiye inu Mulungu wa Isiraeli, zimene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga, zikwaniritsidwe chonde.
27 Koma kodi Mulungu angakhaledi padziko lapansi?+ Kumwamba, ngakhalenso kumwamba kwa kumwamba, simungakwaneko.+ Kuli bwanji nyumba imene ndamangayi?+ 28 Inu Yehova Mulungu wanga, mumvetsere pemphero la mtumiki wanu ndi pempho lake lopempha chifundo. Imvani kulira kwanga kopempha thandizo komanso pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera kwa inu lero. 29 Maso anu akhale akuyangʼana nyumba ino masana komanso usiku. Akhale akuyangʼana malo amene munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala kumeneko,’+ kuti mumvetsere pemphero limene mtumiki wanu angapemphere atayangʼana kumalo ano.+ 30 Mumve pemphero lopempha chifundo la mtumiki wanu komanso la anthu anu Aisiraeli, limene angapemphere atayangʼana malo ano. Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ mumve nʼkukhululuka.+
31 Munthu akachimwira mnzake, wochimwiridwayo nʼkulumbiritsa* wochimwayo pofuna kutsimikiza kuti sanachimwedi, ndiyeno wochimwayo akabwera patsogolo pa guwa lansembe mʼnyumba muno,+ 32 inu mumve muli kumwamba ndipo muchitepo kanthu posonyeza amene ali wolakwa nʼkumubwezera mogwirizana ndi zochita zake komanso musonyeze amene ali wosalakwa nʼkumupatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo chake.+
33 Anthu anu Aisiraeli akagonjetsedwa ndi adani awo chifukwa choti ankakuchimwirani,+ ndiyeno abwerera kwa inu nʼkutamanda dzina lanu+ mʼnyumbayi, kupemphera ndiponso kupempha kuti muwachitire chifundo,+ 34 inuyo mumve muli kumwambako ndipo mukhululuke tchimo la anthu anu Aisiraeli nʼkuwabwezeretsa kudziko limene munapatsa iwowo ndiponso makolo awo.+
35 Kumwamba kukatsekeka, mvula nʼkumakanika kugwa+ chifukwa choti akhala akukuchimwirani,+ ndiyeno iwo nʼkupemphera atayangʼana malo ano, kutamanda dzina lanu ndiponso kusiya machimo awo chifukwa choti mwawapatsa chilango,+ 36 inuyo mumve muli kumwambako ndipo anthu anu Aisiraeli, omwenso ndi atumiki anu, muwakhululukire machimo awo popeza mudzawaphunzitsa+ njira yabwino yoti aziyendamo. Mubweretse mvula mʼdziko lanu+ limene munapatsa anthu anu monga cholowa.
37 Mʼdzikomo mukagwa njala,+ mliri, mphepo yotentha yowononga mbewu, matenda ambewu a chuku,+ dzombe, ziwala zowononga, mliri wamtundu uliwonse, nthenda yamtundu uliwonse komanso adani awo akawaukira mʼmizinda yawo,+ 38 ndiyeno munthu aliyense kapena anthu anu onse Aisiraeli akapereka pemphero lililonse, akapempha kuti muwachitire chifundo+ (chifukwa aliyense akudziwa ululu umene uli mumtima mwake),+ ndiponso akakweza manja awo atayangʼana kunyumbayi, 39 inuyo mumve muli kumwambako, komwe mumakhala+ ndipo mukhululuke+ ndi kuchitapo kanthu. Mupereke mphoto kwa aliyense mogwirizana ndi njira zake zonse,+ chifukwa mukudziwa mtima wake (inu nokha mumadziwa bwino mtima wa munthu aliyense).+ 40 Muchite zimenezi kuti iwo azikuopani masiku onse amene angakhale ndi moyo mʼdziko limene munapatsa makolo athu.
41 Komanso mlendo amene si mmodzi wa anthu anu Aisiraeli, amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina lanu*+ 42 (popeza adzamva za dzina lanu lalikulu,+ dzanja lanu lamphamvu ndiponso mkono wanu wokonzeka kuthandiza*), ndipo wabwera nʼkupemphera atayangʼana nyumbayi, 43 inuyo mumve muli kumwambako, kumene mumakhala,+ ndipo muchite zonse zimene mlendoyo wakupemphani. Muchite zimenezi kuti anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi adziwe dzina lanu ndiponso akuopeni+ ngati mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, komanso adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi.
44 Anthu anu akapita kunkhondo kukamenyana ndi adani awo mmene mwawatumizira,+ ndipo akapemphera+ kwa Yehova atayangʼana kumzinda umene mwasankha+ ndi kunyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 45 inuyo mumve muli kumwambako pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo, ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo.
46 Anthu anu akakuchimwirani (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu nʼkuwakwiyira kwambiri ndiponso kuwapereka kwa adani, adani awowo nʼkuwatenga kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+ 47 ndiyeno iwo nʼkuzindikira kulakwa kwawo mʼdziko limene anawatengeralo+ nʼkulapa,+ ndiponso akapempha chifundo kwa inu mʼdziko la adani awowo+ nʼkunena kuti, ‘Tachimwa, talakwitsa ndiponso tachita zinthu zoipa,’+ 48 nʼkubwerera kwa inu ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse,+ mʼdziko la adani awo amene anawagwira ndiponso akapemphera kwa inu atayangʼana kudziko lawo limene munapatsa makolo awo, mzinda umene mwasankha komanso nyumba ya dzina lanu imene ndamanga,+ 49 inuyo, kumwamba kumene mumakhalako,+ mumve pemphero lawo ndi pempho lawo lopempha chifundo ndipo muonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa iwo. 50 Mukhululukire anthu anu amene anakuchimwirani. Muwakhululukire zimene anakulakwirani. Muchititse kuti adani awo amene anawatenga azikhudzidwa mtima ndipo aziwamvera chisoni,+ 51 (popeza amenewa ndi anthu anu ndi cholowa chanu,+ amene munawatulutsa mu Iguputo,+ kuwachotsa mʼngʼanjo yosungunulira zitsulo).+ 52 Makutu anu amve pempho* la mtumiki wanu lopempha chifundo+ komanso pempho la anthu anu Aisiraeli lopempha chifundo, powamvera zonse zimene angakupempheni.+ 53 Chifukwa munawasankha pakati pa mitundu yonse ya anthu apadziko lapansi+ kuti akhale cholowa chanu ngati mmene munanenera kudzera mwa Mose mtumiki wanu, pamene munkatulutsa makolo athu mu Iguputo, inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.”
54 Solomo atamaliza kupemphera kwa Yehova pemphero lonseli ndiponso kupempha chifundo, anachoka patsogolo pa guwa lansembe la Yehova, chifukwa nthawi yonseyi anali atagwada nʼkukweza manja ake mʼmwamba.+ 55 Kenako anaimirira nʼkuyamba kudalitsa gulu lonse la Aisiraeli ndi mawu okweza kuti: 56 “Atamandike Yehova amene wapatsa anthu ake Aisiraeli malo oti azikhalamo mwamtendere, mogwirizana ndi zimene analonjeza.+ Palibe mawu amene sanakwaniritsidwe pa malonjezo ake onse abwino amene iye analonjeza kudzera mwa Mose mtumiki wake.+ 57 Yehova Mulungu wathu akhale nafe ngati mmene anakhalira ndi makolo athu.+ Asatisiye kapena kutitaya.+ 58 Atipatse mtima wofuna kuyenda mʼnjira zake zonse+ komanso kutsatira malamulo ake, malangizo ake ndi ziweruzo zake zimene analamula makolo athu. 59 Mawu amene ndanenawa popempha chifundo kwa Yehova, Yehova Mulungu wathu aziwakumbukira masana komanso usiku, kuti aonetsetse kuti chilungamo chachitika kwa mtumiki wake ndiponso kwa anthu ake Aisiraeli, mogwirizana ndi zimene zingafunike tsiku lililonse. 60 Achite zimenezi kuti anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi adziwe kuti Yehova ndi Mulungu woona+ ndipo palibenso wina.+ 61 Choncho muzitumikira Yehova Mulungu wathu ndi mtima wathunthu+ potsatira malangizo ake ndi kusunga malamulo ake ngati mmene mukuchitira lero.”
62 Kenako mfumu ndi Aisiraeli onsewo anayamba kupereka nsembe zambiri kwa Yehova.+ 63 Solomo anapereka nsembe zamgwirizano+ kwa Yehova. Anapereka ngʼombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Choncho mfumuyo ndi Aisiraeli onse anatsegulira nyumba ya Yehova.+ 64 Tsiku limenelo, mfumu inapatula pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova chifukwa inkafunika kuperekerapo nsembe zopsereza, nsembe zambewu komanso mafuta a nsembe zamgwirizano. Inachita zimenezi chifukwa guwa lansembe lakopa*+ lapatsogolo pa kachisi wa Yehova linali lalingʼono kwambiri moti nsembe zopsereza, nsembe zambewu ndiponso mafuta+ a nsembe zamgwirizano sizikanakwanapo. 65 Pa nthawiyo Solomo anachita chikondwerero+ pamodzi ndi Aisiraeli onse. Linali gulu lalikulu la anthu amene anachokera ku Lebo-hamati* nʼkutsetsereka mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+ Anachita chikondwererochi pamaso pa Yehova Mulungu wathu masiku 7, ndi masiku enanso 7. Onse pamodzi masiku 14. 66 Tsiku lotsatira,* Solomo anauza anthuwo kuti azipita, ndipo anthuwo anadalitsa mfumuyo nʼkumapita kwawo. Anapita akusangalala, ali ndi chimwemwe mumtima chifukwa cha zabwino zonse+ zimene Yehova anachitira Davide mtumiki wake komanso anthu ake Aisiraeli.
9 Solomo atangomaliza kumanga nyumba ya Yehova, nyumba yachifumu+ ndiponso zinthu zonse zimene anafuna kupanga,+ 2 Yehova anaonekera kwa iye kachiwiri, ngati mmene anachitira ku Gibiyoni.+ 3 Yehova anamuuza kuti: “Ndamva pemphero lako ndi pempho lako lopempha chifundo. Ndayeretsa nyumba imene wamangayi poikamo dzina langa mpaka kalekale+ ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala mmenemo nthawi zonse.+ 4 Iweyo ukayenda mʼnjira zanga ngati mmene bambo ako Davide anachitira,+ yemwe anali ndi mtima wokhulupirika+ komanso ankachita zoyenera,+ ukachita zonse zimene ndinakulamula,+ ndiponso ukamamvera malangizo anga ndi ziweruzo zanga,+ 5 ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu mu Isiraeli mpaka kalekale, ngati mmene ndinalonjezera bambo ako Davide kuti, ‘Munthu wa mʼbanja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+ 6 Koma inuyo ndi ana anu mukadzasiya kunditsatira nʼkusiyanso kutsatira malamulo anga amene ndakupatsani komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira,+ 7 ndidzachotsa Aisiraeli mʼdziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa chifukwa cha dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzatonzedwa ndi kunyozedwa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+ 8 Nyumbayi idzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi adzayangʼana modabwa ndipo adzaimba mluzu nʼkunena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova anachitira zimenezi dzikoli komanso nyumbayi?’+ 9 Ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo mʼdziko la Iguputo ndipo anatenga milungu ina nʼkumaigwadira ndi kuitumikira. Nʼchifukwa chake Yehova anawabweretsera tsoka lonseli.’”+
10 Solomo anamanga nyumba ziwiri, nyumba ya Yehova ndi nyumba yachifumu, ndipo anazimanga kwa zaka 20.+ 11 Hiramu+ mfumu ya Turo anathandiza Solomo ndi matabwa a mkungudza, matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza komanso golide yense amene Mfumu Solomo ankafuna.+ Choncho Mfumu Solomo anapatsa Hiramu mizinda 20 mʼdera la Galileya. 12 Ndiyeno Hiramu anachoka ku Turo nʼkupita kukaona mizinda imene Solomo anamupatsa, koma ataiona sinamusangalatse. 13 Ndipo anati: “Mʼbale wanga, mizinda imene wandipatsayi ubwino wake uli pati?” Choncho mizindayo anaitchula kuti Dziko la Kabulu* mpaka lero. 14 Pa nthawiyo, Hiramu anatumiza kwa mfumuyo golide wokwana matalente* 120.+
15 Mfumu Solomo inagwiritsa ntchito anthu ogwira ntchito yokakamiza+ kuti amange nyumba ya Yehova,+ nyumba* yake, Chimulu cha Dothi,*+ mpanda wa Yerusalemu ndiponso mzinda wa Hazori,+ wa Megido+ ndi wa Gezeri.+ 16 (Mʼmbuyomo, Farao mfumu ya Iguputo anabwera nʼkulanda mzinda wa Gezeri ndipo anautentha ndi moto. Komanso anapha Akanani+ okhala mumzindawo. Kenako anaupereka kwa mwana wake wamkazi+ monga mphatso pamene ankakwatiwa ndi Solomo.) 17 Solomo anamanganso Gezeri, Beti-horoni Wakumunsi,+ 18 Baalati+ ndi Tamara mʼchipululu cha mʼdzikolo. 19 Anamanganso mizinda yake yonse yosungirako zinthu, mizinda yosungirako magaleta,+ mizinda ya amuna okwera pamahatchi ndiponso zilizonse zimene iye anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi mʼmadera onse amene ankalamulira. 20 Panalinso Aamori onse otsala, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ amene sanali Aisiraeli,+ 21 komanso mbadwa zawo zimene zinatsala mʼdzikomo, zomwe Aisiraeli analephera kuzipha. Anthu onsewa Solomo ankawagwiritsa ntchito yaukapolo ndipo akupitiriza kugwira ntchito yaukapoloyi mpaka lero.+ 22 Koma palibe Aisiraeli amene Solomo anawasandutsa akapolo,+ chifukwa iwo anali asilikali ake, atumiki ake, akalonga ake, asilikali othandiza pa magaleta ndiponso atsogoleri a asilikali ake oyendetsa magaleta ndi amuna okwera pamahatchi. 23 Panali akuluakulu oyangʼanira nduna okwana 550 amene ankayangʼanira ntchito ya Solomo. Iwowa ankayangʼanira anthu ogwira ntchito.+
24 Mwana wamkazi+ wa Farao anachoka mu Mzinda wa Davide+ nʼkukakhala kunyumba yake imene Solomo anamʼmangira. Kenako Solomo anamanga Chimulu cha Dothi.*+
25 Katatu pachaka,+ Solomo ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano paguwa lansembe limene anamangira Yehova.+ Ankaperekanso nsembe zautsi paguwa lansembe lomwe linali pamaso pa Yehova. Choncho anamaliza kumanga nyumbayo.+
26 Mfumu Solomo inapanganso zombo ku Ezioni-geberi+ pafupi ndi Eloti, pagombe la Nyanja Yofiira, mʼdziko la Edomu.+ 27 Mʼzombomo, Hiramu ankatumizamo antchito ake odziwa bwino zapanyanja+ kuti akagwire ntchito limodzi ndi antchito a Solomo. 28 Iwo ankapita ku Ofiri+ nʼkukatenga golide wokwana matalente 420 nʼkubwera naye kwa Mfumu Solomo.
10 Mfumukazi ya ku Sheba inamva za Solomo, zoti anatchuka chifukwa cha dzina la Yehova.+ Choncho inabwera kuti idzamuyese pomufunsa mafunso ovuta.+ 2 Mfumukaziyo inafika ku Yerusalemu ndi anthu ambiri oiperekeza.+ Inabwera ndi ngamila zitanyamula mafuta a basamu,+ golide wambiri ndi miyala yamtengo wapatali. Inafika kwa Solomo nʼkuyamba kulankhula naye zonse zimene zinali mumtima mwake. 3 Solomo anayankha mafunso ake onse. Panalibe chimene mfumuyo inalephera kumufotokozera.
4 Mfumukazi ya ku Sheba itaona nzeru zonse za Solomo,+ nyumba imene anamanga,+ 5 chakudya chapatebulo pake,+ operekera zakumwa, mmene atumiki ake ankakhalira pa nthawi ya chakudya, mmene operekera zakudya ankachitira komanso zovala zawo ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse, inasowa chonena. 6 Choncho inauza mfumuyo kuti: “Nkhani zimene ndinamva kudziko langa zokhudza zimene mwakwanitsa kuchita komanso nzeru zanu ndi zoona. 7 Koma sindinakhulupirire zimene ndinauzidwa mpaka pamene ndabwera nʼkuona ndi maso anga. Panopa ndaona kuti zimene ndinauzidwa zinali hafu chabe. Nzeru zanu ndi ulemerero wanu zaposa kwambiri zinthu zimene ndinamva. 8 Anthu anu komanso atumiki anu amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse nʼkumamva nzeru zanu, ndi osangalala.+ 9 Atamandike Yehova Mulungu wanu,+ amene wasangalala nanu nʼkukuikani pampando wachifumu wa Isiraeli. Chifukwa Yehova adzakonda Isiraeli mpaka kalekale, wakuikani kuti mukhale mfumu kuti muziweruza anthu ndi kuchita chilungamo.”
10 Kenako mfumukaziyo inapatsa mfumuyo golide wokwana matalente* 120, mafuta a basamu+ ochuluka kwambiri ndiponso miyala yamtengo wapatali.+ Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka choncho.
11 Zombo za Hiramu zimene zinkanyamula golide kuchokera ku Ofiri+ zinkabweretsanso matabwa a mtengo wa mʼbawa+ ochuluka kwambiri ndiponso miyala yamtengo wapatali.+ 12 Mfumuyo inagwiritsa ntchito matabwa a mʼbawawo popanga zochirikizira nyumba ya Yehova komanso nyumba* ya mfumu. Inagwiritsanso ntchito matabwawo kupanga azeze ndi zoimbira za zingwe za oimba.+ Matabwa a mʼbawa otere sanabwereponso kapena kuoneka mpaka lero.
13 Nayonso Mfumu Solomo inapatsa mfumukazi ya ku Sheba chilichonse chimene inkafuna komanso chimene inapempha, kuwonjezera pa zimene Mfumu Solomo inamʼpatsa chifukwa cha kuwolowa manja kwake. Kenako mfumukaziyo inanyamuka nʼkumapita kwawo limodzi ndi antchito ake.+
14 Golide amene ankabwera kwa Solomo pa chaka, anali wolemera matalente 666,+ 15 osawerengera golide wochokera kwa amalonda oyendayenda, phindu lochokera kwa amalonda komanso golide wochokera kwa mafumu onse a Aluya ndi kwa abwanamkubwa amʼdzikolo.
16 Mfumu Solomo anapanga zishango 200 zikuluzikulu za golide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chilichonse anachikuta ndi golide wolemera masekeli* 600.)+ 17 Anapanganso zishango 300 zingʼonozingʼono* za golide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.) Kenako mfumuyo inaika zishangozi mʼnyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+
18 Mfumuyo inapanganso mpando wachifumu waukulu waminyanga ya njovu+ nʼkuukuta ndi golide woyenga bwino.+ 19 Panali masitepe 6 okafika kumpando wachifumuwo. Pamwamba pa mpandowo panali kanthu kozungulira kokhala ngati denga. Mpandowo unali ndi moika manja mbali zonse ziwiri. Mʼmbali mwake munali zifaniziro ziwiri za mikango+ itaimirira. 20 Pamasitepe 6 aja, panali zifaniziro 12 za mikango itaimirira. Kumapeto kwa sitepe iliyonse kunali mkango umodzi. Panalibenso ufumu womwe unali ndi mpando wachifumu ngati umenewo.
21 Makapu onse a Mfumu Solomo anali agolide, ndipo ziwiya zonse zamʼnyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni+ zinali zagolide yekhayekha. Panalibe chiwiya chasiliva chifukwa siliva sankaoneka ngati kanthu mʼmasiku a Solomo.+ 22 Zinali choncho chifukwa mfumuyo inali ndi zombo za ku Tarisi+ zomwe zinkayenda panyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu. Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombozo zinkabweretsa golide, siliva, minyanga ya njovu,+ anyani ndi mbalame zotchedwa pikoko.
23 Choncho Mfumu Solomo anali wolemera kwambiri+ ndiponso wanzeru+ kuposa mafumu ena onse a padziko lapansi. 24 Anthu onse apadziko lapansi ankafuna kuonana ndi Solomo kuti amve nzeru zake zimene Mulungu anaika mumtima mwake.+ 25 Anthuwo ankabweretsa mphatso monga zinthu zasiliva, zinthu zagolide, zovala, zida zankhondo, mafuta a basamu, mahatchi komanso nyulu* ndipo zimenezi zinkachitika chaka chilichonse.
26 Solomo anasonkhanitsa magaleta ndi mahatchi,* moti anali ndi magaleta 1,400 komanso mahatchi* 12,000.+ Zonsezi ankazisunga mʼmizinda yosungiramo magaleta ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu.+
27 Mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu kukhale siliva wambiri ngati miyala ndiponso kuti matabwa a mkungudza akhale ambiri ngati mitengo ya mkuyu ya ku Sefela.+
28 Mahatchi a Solomo ankawagula kuchokera ku Iguputo ndipo gulu la amalonda a mfumu linkagula mahatchiwo mʼmagulumagulu.*+ 29 Galeta lililonse lochokera ku Iguputo mtengo wake unali ndalama zasiliva 600 pomwe mtengo wa hatchi unali ndalama zasiliva 150. Ndipo iwo ankagulitsa zinthuzi kwa mafumu onse a Ahiti+ ndi mafumu a ku Siriya.
11 Mfumu Solomo inakondanso akazi ena ambiri a mitundu ina+ kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao.+ Inakonda akazi a Chimowabu,+ a Chiamoni,+ a Chiedomu, a Chisidoni+ ndi a Chihiti.+ 2 Akaziwa anali ochokera mʼmitundu imene Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Musamakwatirane nawo komanso musamacheze nawo, chifukwa adzapotoza mitima yanu kuti muzitsatira milungu yawo.”+ Koma Solomo ankakonda anthu amenewa ndipo sanafune kuwasiya. 3 Iye anali ndi akazi olemekezeka 700 komanso akazi ena apambali 300 ndipo patapita nthawi, akaziwo anapotoza mtima wa Solomo.* 4 Iye atakalamba,+ akazi akewa anapotoza mtima wake moti Solomo ankatsatira milungu ina+ ndipo sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu ngati mmene anachitira bambo ake Davide. 5 Solomo anayamba kutsatira Asitoreti,+ mulungu wamkazi wa Asidoni ndi Milikomu,+ mulungu wonyansa wa Aamoni. 6 Solomo anachita zinthu zoipa pamaso pa Yehova ndipo sanatsatire Yehova ndi mtima wonse ngati mmene bambo ake Davide anachitira.+
7 Pa nthawiyi mʼpamene Solomo anamangira Kemosi malo okwezeka.+ Kemosi anali mulungu wonyansa wa Amowabu ndipo anamʼmangira malowo paphiri lomwe linali pafupi ndi Yerusalemu. Anamangiranso Moleki,+ mulungu wonyansa wa Aamoni,+ malo okwezeka. 8 Izi nʼzimene anachitira akazi ake onse a mitundu ina amene ankapereka nsembe zautsi ndi nsembe zina kwa milungu yawo.
9 Yehova anamukwiyira kwambiri Solomo chifukwa mtima wake unapatuka ndipo anasiya kutsatira Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene anaonekera kwa iye kawiri konse+ 10 komanso anamuchenjeza za nkhani imeneyi, kuti asatsatire milungu ina.+ Koma iye sanamvere zimene Yehova analamula. 11 Ndiyeno Yehova anauza Solomo kuti: “Chifukwa chakuti wachita zimenezi ndipo sunasunge pangano langa ndi malamulo amene ndinakupatsa, ndithu ndidzangʼamba ufumuwu kuuchotsa kwa iwe nʼkuupereka kwa mtumiki wako.+ 12 Komabe, chifukwa cha bambo ako Davide, sindichita zimenezi iwe uli moyo. Ufumuwu ndidzaungʼamba nʼkuuchotsa mʼmanja mwa mwana wako,+ 13 koma sindidzauchotsa wonse.+ Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wako+ chifukwa cha Davide mtumiki wanga ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu umene ndausankha.”+
14 Kenako Yehova anabweretsa munthu woti azilimbana ndi Solomo.+ Munthuyo anali Hadadi wa ku Edomu ndipo anali wa mʼbanja lachifumu ku Edomuko.+ 15 Pa nthawi imene Davide anagonjetsa Edomu,+ Yowabu, mkulu wa asilikali, anapita kukakwirira anthu amene anaphedwa. Kumeneko anayambanso kupha mwamuna aliyense wa ku Edomu. 16 (Yowabu ndi Aisiraeli onse anakhala kumeneko miyezi 6, mpaka pamene anapha mwamuna aliyense mu Edomu.) 17 Koma Hadadi ndi Aedomu ena omwe anali atumiki a bambo ake, anathawira ku Iguputo. Pa nthawiyi nʼkuti Hadadi ali kamnyamata. 18 Iwo ananyamuka ku Midiyani nʼkupita ku Parana.+ Kumeneko anatenga anthu ena nʼkukafika ku Iguputo kwa Farao mfumu ya Iguputo. Faraoyo anapatsa Hadadi nyumba ndi malo komanso ankamupatsa chakudya. 19 Farao ankamukonda kwambiri Hadadi moti mpaka anamʼpatsa mkazi. Mkaziyo anali mngʼono wake wa Tapenesi, mkazi wa Farao. 20 Patapita nthawi, mngʼono wake wa Tapenesi anaberekera Hadadi mwana wamwamuna dzina lake Genubati. Tapenesi anamutenga* nʼkumamulera mʼnyumba ya Farao ndipo Genubati ankakhala mʼnyumba ya Farao pamodzi ndi ana a Farao.
21 Hadadi ali ku Iguputo, anamva kuti Davide, mofanana ndi makolo ake, anamwalira+ ndiponso kuti Yowabu mkulu wa asilikali anamwaliranso.+ Choncho Hadadi anapempha Farao kuti: “Kodi mungandilole kuti ndizipita kwathu?” 22 Koma Farao anamufunsa kuti: “Kodi ukusowa chiyani kuno kuti uzifuna kupita kwanu?” Hadadi anayankha kuti: “Palibe chimene ndikusowa, koma chonde ndiloleni ndizipita.”
23 Mulungu anabweretsa munthu winanso woti azilimbana ndi Solomo.+ Munthuyo anali Rezoni mwana wa Eliyada, yemwe anathawa kwa mbuye wake Hadadezeri,+ mfumu ya Zoba. 24 Davide atagonjetsa* anthu a ku Zoba, Rezoni anasonkhanitsa anthu ndipo anakhala mtsogoleri wa gulu la achifwamba.+ Choncho iye ndi gulu lakelo anapita kukakhala ku Damasiko+ nʼkuyamba kulamulira kumeneko. 25 Rezoni ankalimbana ndi Aisiraeli masiku onse a Solomo, ndipo ankawachitira zoipa kuwonjezera pa zoipa zimene Hadadi ankawachitira. Rezoni ankadana kwambiri ndi Aisiraeli pa nthawi imene iye ankalamulira ku Siriya.
26 Panalinso Yerobowamu,+ mwana wa Nebati, wa fuko la Efuraimu, wa ku Zereda. Iye anali mtumiki wa Solomo.+ Mayi ake anali mkazi wamasiye dzina lake Zeruwa. Nayenso Yerobowamu anayamba kuukira mfumu.+ 27 Iye anaukira mfumu chifukwa chakuti: Solomo anamanga Chimulu cha Dothi*+ ndiponso anatseka mpata umene unali pampanda wa Mzinda wa bambo ake Davide.+ 28 Yerobowamu anali munthu waluso. Ndiyeno Solomo ataona kuti mnyamatayo ndi wolimbikira ntchito, anamʼpatsa udindo woyangʼanira+ anthu ogwira ntchito yokakamiza kunyumba ya Yosefe. 29 Pa nthawiyo, Yerobowamu anatuluka mu Yerusalemu ndipo Ahiya+ wa ku Silo, yemwe anali mneneri, anamʼpeza panjira. Ahiya anali atavala chovala chatsopano ndipo awiriwo anali okhaokha kumeneko. 30 Ndiyeno Ahiya anavula chovala chatsopano chimene anavalacho nʼkuchingʼamba mapisi okwana 12. 31 Atatero, anauza Yerobowamu kuti:
“Tengapo mapisi 10, chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikungʼamba ufumuwu kuuchotsa mʼmanja mwa Solomo ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko 10.+ 32 Koma fuko limodzi lipitiriza kukhala lake+ chifukwa cha mtumiki wanga Davide+ ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli.+ 33 Ndichita zimenezi chifukwa iwo andisiya+ nʼkuyamba kugwadira Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndi Milikomu mulungu wa Aamoni. Iwo sanayende mʼnjira zanga, sanachite zoyenera pamaso panga ndipo sanatsatire malamulo anga ndi ziweruzo zanga ngati mmene anachitira Davide bambo a Solomo. 34 Koma sindidzachotsa ufumu wonse mʼmanja mwake. Ndidzamulola kukhalabe mtsogoleri masiku onse a moyo wake chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene ndinamusankha,+ popeza Davide anasunga malamulo anga. 35 Koma ndidzachotsa ufumuwu mʼmanja mwa mwana wake nʼkuupereka kwa iwe ndipo ndidzakupatsa mafuko 10.+ 36 Mwana wake ndidzamʼpatsa fuko limodzi kuti mtumiki wanga Davide apitirize kukhala ndi nyale pamaso panga mumzinda wa Yerusalemu+ umene ndausankha kuti ukhale ndi dzina langa. 37 Ndidzakutenga ndipo udzalamulira zonse zimene umalakalaka. Udzakhaladi mfumu ya Isiraeli. 38 Ukamvera malamulo anga onse, kuyenda mʼnjira zanga ndiponso kuchita zoyenera pamaso panga posunga malamulo anga ngati mmene anachitira mtumiki wanga Davide,+ inenso ndidzakhala nawe. Ana ako adzalamulira kwa nthawi yaitali mofanana ndi ana a Davide,+ ndipo ndidzakupatsa Isiraeli. 39 Ndidzachititsa manyazi ana a Davide chifukwa cha zoipa zimene anachita,+ koma osati nthawi zonse.’”+
40 Solomo ankafuna kupha Yerobowamu koma Yerobowamu anathawira ku Iguputo kwa Sisaki,+ mfumu ya Iguputo.+ Anakhala ku Iguputoko mpaka Solomo atamwalira.
41 Nkhani zina zokhudza Solomo, zonse zimene anachita ndiponso nzeru zake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya Solomo.+ 42 Solomo analamulira Isiraeli yense ku Yerusalemu kwa zaka 40. 43 Kenako Solomo anamwalira* ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide bambo ake. Ndiyeno mwana wake Rehobowamu,+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.
12 Rehobowamu anapita ku Sekemu+ chifukwa Aisiraeli onse anapita kumeneko kuti akamuveke ufumu.+ 2 Yerobowamu mwana wa Nebati anamva zimenezi ali ku Iguputo, (iye anali ku Iguputo chifukwa anathawa Mfumu Solomo nʼkukakhala kumeneko),+ 3 ndipo anthu anatumiza uthenga womuitana. Kenako Yerobowamu ndi gulu lonse la Aisiraeli anabwera kwa Rehobowamu nʼkumuuza kuti: 4 “Bambo anu anachititsa kuti goli lathu likhale lowawa.+ Koma inuyo mukatifewetsera ntchito yowawa ya bambo anu komanso goli lolemera limene ankatisenzetsa, tizikutumikirani.”
5 Rehobowamu atamva zimenezi anauza anthuwo kuti: “Pitani kaye ndipo mukabwerenso pakatha masiku atatu.” Choncho anthuwo anapitadi.+ 6 Ndiyeno Mfumu Rehobowamu anafunsa nzeru kwa anthu achikulire* amene ankatumikira bambo ake Solomo pamene anali moyo. Anawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti anthuwa ndiwayankhe bwanji?” 7 Iwo anamuuza kuti: “Ngati lero mungakhale mtumiki wa anthuwa, kumvera zimene apempha ndiponso kuwayankha bwino, iwo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”
8 Koma iye sanamvere malangizo amene anthu achikulirewo* anamupatsa, ndipo anapita kukafunsira malangizo kwa achinyamata amene anakulira naye limodzi, omwe ankamutumikira.+ 9 Iye anawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti tiwayankhe bwanji anthuwa, amene andiuza kuti, ‘Mutifewetsere goli limene bambo anu anatisenzetsaʼ?” 10 Achinyamata amene anakulira naye limodziwo anamuuza kuti: “Anthu amene akuuzani kuti, ‘Bambo anu anatisenzetsa goli lolemera, koma inuyo mutipeputsirekoʼ mukawauze kuti, ‘Chala changa chachingʼono chidzakhala chachikulu kuposa chiuno cha bambo anga. 11 Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera koma ineyo ndiwonjezera goli lanulo. Bambo anga ankakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndizikukwapulani ndi zikoti zaminga.’”
12 Pa tsiku lachitatu, Yerobowamu ndi anthu onse anapita kwa Rehobowamu, mogwirizana ndi zimene mfumuyo inanena kuti: “Mukabwerenso pakatha masiku atatu.”+ 13 Koma mfumuyo inayankha anthuwo mwaukali ndipo sinamvere malangizo a anthu achikulire* aja. 14 Inayankha anthuwo motsatira malangizo a achinyamata aja. Inati: “Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera koma ineyo ndiwonjezera goli lanulo. Bambo anga ankakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndizikukwapulani ndi zikoti zaminga.” 15 Choncho mfumu sinamvere anthuwo. Yehova ndi amene anachititsa kuti zinthu zikhale chonchi,+ kuti akwaniritse mawu amene Yehovayo analankhula kwa Yerobowamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya+ wa ku Silo.
16 Aisiraeli onse ataona kuti mfumuyo yakana kuwamvera, anayankha kuti: “Ife Davide tilibe naye ntchito ndipo sitingapatsidwe cholowa kuchokera kwa mwana wa Jese. Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu yake! Tsopano iwe Davide, uziyangʼanira nyumba yako yokha.” Aisiraeliwo atatero, aliyense anabwerera kunyumba* kwawo.+ 17 Koma Rehobowamu anapitiriza kulamulira Aisiraeli amene ankakhala mʼmizinda ya ku Yuda.+
18 Kenako Mfumu Rehobowamu inatumiza Adoramu+ amene ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yokakamiza, koma Aisiraeli onse anamugenda ndi miyala nʼkumupha. Komabe, Mfumu Rehobowamu inatha kukwera galeta lake nʼkuthawira ku Yerusalemu.+ 19 Ndipo Aisiraeli akupitiriza kuukira+ nyumba ya Davide mpaka lero.
20 Aisiraeli onse atangomva kuti Yerobowamu wabwera, anatumiza uthenga womuitanira kumene anasonkhana, ndipo anamuika kukhala mfumu ya Aisiraeli onse.+ Palibenso amene ankatsatira nyumba ya Davide kupatulapo fuko la Yuda.+
21 Rehobowamu atangofika ku Yerusalemu, anasonkhanitsa asilikali ophunzitsidwa bwino* okwana 180,000 a nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini. Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi nyumba ya Isiraeli pofuna kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu mwana wa Solomo.+ 22 Kenako Semaya,+ munthu wa Mulungu woona, anamva mawu ochokera kwa Mulungu woona kuti: 23 “Ukauze Rehobowamu mwana wa Solomo, mfumu ya Yuda, komanso nyumba yonse ya Yuda ndi Benjamini ndiponso anthu ena onse kuti, 24 ‘Yehova wanena kuti: “Musapite kukamenyana ndi abale anu, Aisiraeli. Aliyense abwerere kunyumba chifukwa ine ndi amene ndachititsa zimenezi.”’”+ Choncho anthuwo anamvera mawu a Yehova nʼkubwerera kwawo ngati mmene Yehova ananenera.
25 Yerobowamu anamanga* mzinda wa Sekemu+ mʼdera lamapiri la Efuraimu nʼkumakhala kumeneko. Kenako anachoka nʼkupita kukamanga* mzinda wa Penueli.+ 26 Yerobowamu anaganiza kuti: “Tsopano ufumuwu ubwerera kunyumba ya Davide.+ 27 Anthuwa akapitiriza kupita kukapereka nsembe kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu,+ mtima wawo udzabwerera kwa mbuye wawo Rehobowamu mfumu ya Yuda. Akatero adzandipha nʼkubwerera kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda.” 28 Mfumuyo itakambirana ndi anthu ena inapanga ana awiri a ngʼombe agolide,+ kenako inauza anthu onse kuti: “Ndikuona kuti mukuvutika kwambiri kupita ku Yerusalemu. Ndiye ndakupangirani Mulungu uyu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo+ Aisiraeli inu.” 29 Choncho mwana wa ngʼombe wina anamuika ku Beteli+ ndipo wina anakamuika ku Dani.+ 30 Zimenezi zinachititsa kuti anthuwo achimwe+ ndipo iwo ankakafika mpaka ku Dani kukalambira mwana wa ngʼombeyo.
31 Yerobowamu anamanga nyumba zolambiriramo mʼmalo okwezeka. Ndipo anasankha anthu wamba, anthu amene sanali ana a Levi, kuti akhale ansembe.+ 32 Yerobowamu anakhazikitsa chikondwerero chofanana ndi cha ku Yuda pa tsiku la 15 la mwezi wa 8.+ Paguwa la nsembe limene analimanga ku Beteli,+ anaperekapo nsembe kwa ana a ngʼombe amene anawapanga aja ndipo ku Beteliko anasankha ansembe kuti azitumikira mʼmalo okwezeka amene anapanga. 33 Yerobowamu anapereka nsembe pa tsiku la 15 la mwezi wa 8 womwe anausankha yekha. Anapereka nsembezo paguwa limene anamanga ku Beteli. Iye anayambitsa chikondwerero choti Aisiraeli azichita ndipo anakwera paguwa kukapereka nsembe zautsi komanso nsembe zina.
13 Panali munthu wa Mulungu+ amene anatumidwa ndi Yehova kuchokera ku Yuda kupita ku Beteli. Kumeneko iye anapeza Yerobowamu ataimirira pambali pa guwa lansembe+ kuti apereke nsembe yautsi. 2 Ndiyeno anafuula mawu ochokera kwa Yehova otemberera guwalo, kuti: “Guwa lansembe iwe! Guwa lansembe iwe! Yehova wanena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa mʼnyumba ya Davide, dzina lake Yosiya.+ Iye adzatenga ansembe a malo okwezeka amene akupereka nsembe yautsi pa iwe nʼkuwapereka nsembe pa iwe. Ndipo adzawotcha mafupa a anthu pa iwe.’”+ 3 Kenako munthu wa Mulunguyo anapereka chizindikiro. Iye anati: “Chizindikiro chimene Yehova wapereka ndi ichi: Guwa lansembeli lingʼambika pakati ndipo phulusa* limene lili paguwali litayika.”
4 Mfumu Yerobowamu atangomva mawu otemberera guwa lansembe la ku Beteli amene munthu wa Mulunguyo ananena, anasiya zimene ankachita paguwa lansembe nʼkumuloza ndipo ananena kuti: “Mʼgwireni uyu!”+ Nthawi yomweyo, dzanja limene analozera munthu wa Mulunguyo linauma ndipo sanathe kulibweza.+ 5 Kenako guwa lansembelo linangʼambika ndipo phulusa linatayika mogwirizana ndi chizindikiro chimene munthu wa Mulungu woonayo anapereka, malinga ndi mawu a Yehova.
6 Mfumuyo inauza munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Chonde, pemphani Yehova Mulungu wanu kuti andichitire chifundo ndipo mundipempherere kuti dzanja langa libwerere mwakale.”+ Choncho munthu wa Mulungu woonayo anapempha Yehova kuti achitire chifundo mfumuyo, moti dzanjalo linabwerera mwakale. 7 Kenako mfumuyo inauza munthuyo kuti: “Tiyeni kunyumba mukadye chakudya komanso ndikakupatseni mphatso.” 8 Koma munthu wa Mulungu woonayo anayankha mfumuyo kuti: “Ngakhale mutandipatsa hafu ya nyumba yanu sindingapite nanu ndipo sindingadye chakudya kapena kumwa madzi kuno. 9 Chifukwa Yehova anandilamula kuti: ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi ndipo pobwerera usakadzere njira imene udutse popita.’” 10 Choncho iye ananyamuka nʼkudutsa njira ina. Sanadutse njira imene anadzera popita ku Beteliko.
11 Ndiyeno panali mneneri wina wokalamba yemwe ankakhala ku Beteli. Ana ake anabwera nʼkumufotokozera zonse zimene munthu wa Mulungu woona uja anachita ku Beteli komanso zomwe anauza mfumu. Atamufotokozera zimenezi, 12 bamboyo anafunsa anawo kuti: “Munthuyo wadzera njira iti?” Anawo analozera bamboyo njira imene munthu wa Mulungu woona wochokera ku Yuda uja anadzera. 13 Kenako bamboyo anauza anawo kuti: “Ndimangireni chishalo pabulu.” Anawo anamangiradi bambo awowo chishalo ndipo iwo anakwera buluyo.
14 Atatero, anatsatira munthu wa Mulungu woona uja ndipo anamʼpeza atakhala pansi pa mtengo waukulu. Ndiyeno anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu woona amene wachokera ku Yuda?”+ Munthuyo anayankha kuti: “Inde, ndi ineyo.” 15 Kenako anamuuza kuti: “Tiye kunyumba ukadye chakudya.” 16 Koma munthuyo anati: “Sindingabwerere nanu kapena kuchita zomwe mwandiuzazi ndipo sindingadye nanu chakudya kapena kumwa madzi kuno. 17 Chifukwa Yehova anandiuza kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko ndipo pobwerera usakadzere njira imene udutse popita.’” 18 Mneneri wokalambayo atamva zimenezi anati: “Inenso ndine mneneri ngati iweyo. Mngelo wandiuza mawu ochokera kwa Yehova akuti, ‘Kamʼbweze upite naye kunyumba kwako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’” (Anamunamiza.) 19 Choncho anabwerera naye kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi kunyumba kwake.
20 Akudya patebulo, mawu a Yehova anafika kwa mneneri yemwe anabweza munthu wa ku Yuda uja. 21 Ndiyeno anauza munthu wa Mulungu woona wochokera ku Yuda uja kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti sunamvere zimene Yehova anakulamula ndipo sunatsatire lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa, 22 koma wabwerera kuti udye chakudya ndi kumwa madzi kumalo amene iye anakuuza kuti: “Usakadye chakudya kapena kumwa madzi,” mtembo wako sudzaikidwa mʼmanda a makolo ako.’”+
23 Munthu wa Mulungu woona uja atamaliza kudya ndi kumwa, mneneri wokalambayo anamanga chishalo pabulu kuti mneneri wa ku Yuda, yemwe anamʼbwezayo akwerepo. 24 Kenako mneneri wa ku Yudayo ananyamuka nʼkumapita. Koma mkango unamupeza panjira nʼkumupha,+ ndipo mtembo wake unali pamsewu. Bulu ndi mkangowo zinaima pambali pa mtembowo. 25 Anthu ena amene ankadutsa, anaona mtembowo uli pamsewupo, mkango utaima pambali pake. Anthuwo atafika mumzinda womwe mneneri wokalamba uja ankakhala, anafotokoza zomwe anaonazo.
26 Mneneri amene anakabweza munthu uja atamva nkhaniyi, nthawi yomweyo anati: “Ndi munthu wa Mulungu woona amene sanamvere lamulo la Yehova uja.+ Choncho Yehova wamupereka kwa mkango kuti umugwire nʼkumupha, mogwirizana ndi mawu amene Yehova anamuuza.”+ 27 Ndiyeno anauza ana ake kuti: “Ndimangireni chishalo pabulu.” Ndipo anamʼmangiradi. 28 Mneneri wokalambayo ananyamuka nʼkukapeza mtembo wa munthu uja uli pamsewu, bulu ndi mkango zitaima pambali pake. Mkangowo sunadye mtembowo kapena kupha buluyo. 29 Ndiyeno mneneriyo ananyamula mtembo wa munthu wa Mulungu woonayo nʼkuukweza pabulu ndipo anabwerera nawo mumzinda wa mneneri wokalambayo kuti akamulire ndi kumuika mʼmanda. 30 Mneneri wokalambayo anakaika mtembowo mʼmanda ake. Ndipo anthu ankamulira kuti: “Mayo ine, mʼbale wanga!” 31 Atamuika mʼmanda, mneneri wokalambayo anauza ana ake kuti: “Ndikadzamwalira mudzandiike mʼmanda amene taika munthu wa Mulungu woonayu. Mudzaike mafupa anga pambali pa mafupa ake.+ 32 Mawu a Yehova amene munthu wa Mulunguyu ananena otemberera guwa lansembe limene lili ku Beteli ndiponso akachisi onse amʼmalo okwezeka+ amene ali mʼmizinda ya ku Samariya, adzakwaniritsidwa ndithu.”+
33 Ngakhale kuti zimenezi zinachitika, Yerobowamu sanasiye kuchita zoipa. Iye anapitiriza kuika anthu wamba kuti akhale ansembe a malo okwezeka.+ Aliyense wofuna unsembewo, iye ankamʼpatsa ponena kuti: “Uyu akhale wansembe wa malo okwezeka.”+ 34 Tchimo la nyumba ya Yerobowamuli,+ linachititsa kuti anthu onse amʼnyumba yake awonongedwe nʼkufafanizidwa padziko lapansi.+
14 Pa nthawiyo, Abiya mwana wamwamuna wa Yerobowamu anadwala. 2 Choncho Yerobowamu anauza mkazi wake kuti: “Nyamuka upite ku Silo ndipo udzisinthe kuti anthu asadziwe kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu. Mneneri Ahiya ali kumeneko. Iye ndi amene anandiuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthuwa.+ 3 Utenge mikate 10, makeke ndi botolo la uchi, upite kwa iyeyo ndipo akakuuza zimene zichitikire mnyamatayu.”
4 Mkazi wa Yerobowamu anachitadi zimenezo. Ananyamuka kupita ku Silo+ nʼkukafika kunyumba kwa Ahiya. Ahiyayo sankatha kuona chifukwa maso ake anali atachita khungu ndi ukalamba.
5 Koma Yehova anali atauza Ahiya kuti: “Kukubwera mkazi wa Yerobowamu kudzakufunsa za mwana wake chifukwa mwanayo akudwala. Ndikuuza zoti umuuze.* Akafika adzisintha kuti asadziwike.”
6 Ahiya atangomva phokoso la mapazi a mkazi wa Yerobowamu pamene ankafika pakhomo anati: “Lowa mkazi wa Yerobowamu. Nʼchifukwa chiyani ukudzisintha kuti usadziwike? Ine ndatumidwa kuti ndikuuze uthenga wopweteka. 7 Pita ukauze Yerobowamu kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndinakukweza pakati pa anthu a mtundu wako kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+ 8 Kenako ndinangʼamba ufumu kuuchotsa kunyumba ya Davide nʼkukupatsa.+ Koma iwe sunakhale ngati Davide mtumiki wanga amene anasunga malamulo anga, kunditsatira ndi mtima wake wonse ndiponso kuchita zinthu zoyenera zokhazokha pamaso panga.+ 9 Koma wachita zinthu zoipa kwambiri kuposa onse amene anakhalapo iwe usanakhale. Unadzipangiranso mulungu wina komanso zifaniziro zachitsulo kuti undikwiyitse+ ndipo wandisiya.+ 10 Pa chifukwa chimenechi, ndikubweretsa tsoka panyumba ya Yerobowamu ndipo ndidzapha mwamuna* aliyense wamʼnyumba ya Yerobowamu, ngakhale ooneka onyozeka ndi ofooka mu Isiraeli. Komanso ndidzaseseratu nyumba ya Yerobowamu+ ngati mmene munthu amasesera ndowe mpaka zonse zitachoka. 11 Munthu wa mʼbanja la Yerobowamu wofera mumzinda, agalu adzamudya ndipo wofera kutchire, mbalame zidzamudya chifukwa Yehova wanena zimenezi.”’
12 Iweyo nyamuka, uzipita kunyumba kwanu ndipo mapazi ako akakangoponda mumzinda, mwanayo akamwalira. 13 Aisiraeli onse akamulira nʼkumuika mʼmanda ndipo mʼbanja lonse la Yerobowamu, uyu yekha ndi amene adzaikidwe mʼmanda chifukwa mʼnyumba yonse ya Yerobowamu, Yehova Mulungu wa Isiraeli wapeza chinachake chabwino mwa yekhayu. 14 Yehova adzaika yekha mfumu ina yolamulira Isiraeli, yomwe idzafafanize nyumba ya Yerobowamu+ kuyambira tsiku limenelo, ndipo akhoza kuchitanso zimenezi pompano. 15 Yehova adzawononga Isiraeli ngati bango limene likugwedezeka mʼmadzi ndipo adzazula Aisiraeli mʼdziko labwinoli limene anapatsa makolo awo.+ Ndiyeno adzawabalalitsira kutsidya lina la Mtsinje,*+ chifukwa anapanga mizati* yawo yopatulika+ nʼkukwiyitsa Yehova. 16 Iye adzasiya Aisiraeli chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita ndiponso amene Aisiraeli anachita chifukwa cha iyeyo.”+
17 Atamva zimenezi, mkazi wa Yerobowamu ananyamuka nʼkumapita ndipo anafika ku Tiriza. Atangofika pakhomo la nyumba yawo, mnyamatayo anamwalira. 18 Choncho anamuika mʼmanda ndipo Aisiraeli onse anamulira, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya.
19 Nkhani zina zokhudza Yerobowamu, mmene anamenyera nkhondo+ ndiponso ulamuliro wake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 20 Yerobowamu analamulira zaka 22, kenako mofanana ndi makolo ake anamwalira.+ Ndiyeno mwana wake, dzina lake Nadabu, anayamba kulamulira mʼmalo mwake.+
21 Pa nthawiyi, Rehobowamu mwana wa Solomo anali mfumu ku Yuda. Rehobowamu anali ndi zaka 41 pamene ankayamba kulamulira, ndipo analamulira kwa zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anasankha+ pa mafuko onse a Isiraeli kuti aikeko dzina lake.+ Mayi ake anali Naama, mbadwa ya Amoni.+ 22 Ayuda ankachita zoipa pamaso pa Yehova+ ndipo anamukwiyitsa kwambiri ndi machimo awo kuposa mmene makolo awo anachitira.+ 23 Nawonso anapitiriza kumanga malo okwezeka, zipilala zopatulika ndi mizati yopatulika*+ pamwamba pa phiri lililonse lalitali+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira.+ 24 Mʼdzikomo munkapezekanso mahule aamuna apakachisi.+ Anthuwo anachita zinthu zonse zonyansa zimene ankachita anthu a mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa Aisiraeli.
25 Mʼchaka cha 5 cha Mfumu Rehobowamu, Sisaki mfumu ya Iguputo+ anaukira Yerusalemu.+ 26 Iye anatenga chuma chamʼnyumba ya Yehova ndi chuma chamʼnyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse kuphatikizapo zishango zonse zagolide zimene Solomo anapanga.+ 27 Choncho Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zakopa* mʼmalomwake ndipo anazipereka kwa akulu a asilikali* olondera pakhomo la nyumba ya mfumu kuti aziziyangʼanira. 28 Nthawi iliyonse imene mfumuyo ikupita kunyumba ya Yehova, asilikaliwo ankanyamula zishangozo ndipo kenako ankazibwezera kuchipinda cha alonda.
29 Nkhani zina zokhudza Rehobowamu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda.+ 30 Pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu pankachitika nkhondo nthawi zonse.+ 31 Kenako Rehobowamu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ Mayi ake anali Naama ndipo anali a Chiamoni.+ Kenako Abiyamu*+ mwana wa Rehobowamu anayamba kulamulira mʼmalo mwake.
15 Mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yerobowamu+ mwana wa Nebati, Abiyamu anakhala mfumu ya Yuda.+ 2 Iye analamulira zaka zitatu ku Yerusalemu. Mayi ake anali Maaka,+ mdzukulu wa Abishalomu. 3 Abiyamu anapitiriza kuchita machimo onse amene bambo ake anachita. Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wonse ngati mmene anachitira Davide kholo lake. 4 Komabe, chifukwa cha kukhulupirika kwa Davide,+ Yehova Mulungu wake anamʼpatsa nyale mu Yerusalemu+ pokweza mwana wake pambuyo pake ndiponso pochititsa kuti Yerusalemu akhalepobe. 5 Anatero popeza Davide anachita zoyenera pamaso pa Yehova, ndipo anatsatira chilichonse chimene Mulungu anamulamula masiku onse a moyo wake, kupatulapo pa nkhani ya Uriya Muhiti.+ 6 Masiku onse a Rehobowamu, pankachitika nkhondo pakati pa iyeyo ndi Yerobowamu.+
7 Nkhani zina zokhudza Abiyamu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda.+ Pakati pa Abiyamu ndi Yerobowamu, panachitikanso nkhondo.+ 8 Kenako Abiyamu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. Ndiyeno mwana wake Asa+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.+
9 Mʼchaka cha 20 cha Yerobowamu mfumu ya Isiraeli, Asa anayamba kulamulira ku Yuda. 10 Analamulira ku Yerusalemu zaka 41. Agogo ake aakazi dzina lawo linali Maaka,+ mdzukulu wa Abishalomu. 11 Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova+ ngati mmene anachitira Davide kholo lake. 12 Iye anachotsa mahule aamuna apakachisi mʼdzikolo+ komanso mafano onse onyansa* amene makolo ake anapanga.+ 13 Anachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu, chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri lolambirira mzati wopatulika.* Asa anagwetsa fanolo+ nʼkukalitentha mʼchigwa cha Kidironi.+ 14 Koma sanachotse malo okwezeka.+ Ngakhale zinali choncho, Asa anatumikira Yehova ndi mtima wonse kwa moyo wake wonse. 15 Iye anabweretsa kunyumba ya Yehova zinthu zimene bambo ake komanso iyeyo anaziyeretsa. Zinthuzo zinali siliva, golide ndiponso ziwiya zina zosiyanasiyana.+
16 Pakati pa Asa ndi Basa+ mfumu ya Isiraeli pankachitika nkhondo. 17 Choncho Basa mfumu ya Isiraeli anapita kukaukira Yuda ndipo anayamba kumanganso mzinda wa Rama+ kuti ukhale wolimba. Anachita zimenezi kuti anthu asamalowe kapena kutuluka mʼdera la Asa mfumu ya Yuda.+ 18 Zitatero, Asa anatenga siliva ndi golide yense amene anatsala pa chuma chamʼnyumba ya Yehova ndi pa chuma chamʼnyumba ya mfumu nʼkumupereka kwa atumiki ake. Kenako Mfumu Asa anatumiza atumiki akewo kwa Beni-hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Hezioni, mfumu ya Siriya,+ amene ankakhala ku Damasiko. Anawatuma kuti akamuuze Beni-hadadi kuti: 19 “Pali pangano pakati pa ine ndi iwe ndiponso pakati pa bambo anga ndi bambo ako. Ndakutumizira mphatso ya siliva ndi golide. Bwera udzaphwanye pangano lako ndi Basa mfumu ya Isiraeli kuti achoke mʼdera langa.” 20 Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a asilikali ake kuti akamenyane ndi anthu amʼmizinda ya Isiraeli. Iwo analanda Iyoni,+ Dani,+ Abele-beti-maaka ndi Kinereti yense komanso dera lonse la Nafitali. 21 Basa atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama* ndipo anapitiriza kukhala ku Tiriza.+ 22 Ndiyeno Mfumu Asa inaitanitsa Ayuda onse moti palibe amene anatsala, ndipo iwo anatenga miyala ndi matabwa za ku Rama zimene Basa ankamangira. Mfumu Asa anatenga zinthu zimenezi nʼkukamangira mzinda wa Geba+ ku Benjamini ndi wa Mizipa+ kuti mizindayi ikhale yolimba.
23 Nkhani zina zonse zokhudza Asa, mphamvu zake, mizinda imene anamanga* ndiponso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. Koma atakalamba anadwala matenda akumapazi.+ 24 Kenako Asa, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide kholo lake. Ndiyeno mwana wake Yehosafati+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.
25 Nadabu+ mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 26 Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anatsatira njira ya bambo ake+ komanso machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha bambo akewo.+ 27 Ndiyeno Basa mwana wa Ahiya wa nyumba ya Isakara, anakonzera chiwembu Nadabu ndipo anamupha mumzinda wa Gibitoni,+ womwe unali mʼmanja mwa Afilisiti. Anamupha pa nthawi imene Nadabuyo ndi Aisiraeli onse ankaukira Gibitoni. 28 Basa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda ndipo anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 29 Basa atangokhala mfumu, anapha anthu onse a mʼnyumba ya Yerobowamu. Sanasiye munthu aliyense wa mʼbanja la Yerobowamu ali ndi moyo. Anapha onse mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo.+ 30 Izi zinachitika chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita, machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha iye komanso chifukwa choti Yerobowamuyo anakwiyitsa kwambiri Yehova Mulungu wa Isiraeli. 31 Nkhani zina zokhudza Nadabu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 32 Pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Isiraeli pankachitika nkhondo.+
33 Mʼchaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Basa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Isiraeli yense ku Tiriza ndipo analamulira kwa zaka 24.+ 34 Koma iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo ankayenda mʼnjira ya Yerobowamu ndiponso mʼmachimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha Yerobowamuyo.+
16 Yehova analankhula mawu otsutsa Basa+ kudzera mwa Yehu,+ mwana wa Haneni kuti: 2 “Ndinakukweza kukuchotsa pafumbi kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+ Koma iwe wakhala ukuyenda mʼnjira ya Yerobowamu nʼkuchimwitsa anthu anga Aisiraeli ndipo andikwiyitsa ndi machimo awo.+ 3 Choncho ndidzaseseratu Basa ndi nyumba yake ndipo ndidzachititsa nyumba yake kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati. 4 Munthu aliyense wa mʼbanja la Basa amene adzafere mumzinda, agalu adzamudya ndipo amene adzafere kutchire, mbalame zidzamudya.”
5 Nkhani zina zokhudza Basa ndi zimene anachita ndiponso mphamvu zake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 6 Kenako Basa, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda ku Tiriza.+ Ndiyeno mwana wake Ela anakhala mfumu mʼmalo mwake. 7 Komanso Yehova analankhula mawu otsutsa Basa ndi nyumba yake kudzera mwa mneneri Yehu mwana wa Haneni. Anamutsutsa chifukwa cha zoipa zonse zimene Basayo anachita pamaso pa Yehova pomukwiyitsa ndi ntchito ya manja ake ngati mmene anthu a mʼnyumba ya Yerobowamu anachitira ndiponso chifukwa chakuti iye anapha Nadabu.+
8 Mʼchaka cha 26 cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Basa anakhala mfumu ya Isiraeli ku Tiriza ndipo analamulira zaka ziwiri. 9 Kenako mtumiki wake Zimiri, amene ankayangʼanira hafu ya asilikali oyenda pa magaleta, anamukonzera chiwembu pamene Ela ankamwa mowa mpaka kuledzera kunyumba ya Ariza ku Tiriza. Ariza anali woyangʼanira banja la mfumu ku Tirizako. 10 Ndiyeno Zimiri anafika nʼkupha Ela+ ndipo zimenezi zinachitika mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda. Kenako Zimiri anakhala mfumu mʼmalo mwake. 11 Iye atangokhala pampando wachifumu nʼkuyamba kulamulira, anapha anthu onse a mʼnyumba ya Basa. Sanasiye ndi moyo mwamuna* aliyense wa mʼbanja la Basa, kaya wachibale* wake kapena mnzake. 12 Choncho Zimiri anapha anthu onse a mʼnyumba ya Basa, mogwirizana ndi mawu a Yehova otsutsa Basa amene analankhula kudzera mwa mneneri Yehu.+ 13 Anawapha onse chifukwa cha machimo onse amene Basa ndi mwana wake Ela anachita, komanso machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha iwo nʼkukwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mafano awo opanda pake.+ 14 Nkhani zina zokhudza Ela ndiponso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli.
15 Mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda, Zimiri anakhala mfumu ku Tiriza ndipo analamulira masiku 7. Pa nthawiyo nʼkuti asilikali atamanga msasa pafupi ndi mzinda wa Gibitoni,+ umene unali wa Afilisiti, kuti amenyane ndi anthu amumzindawo. 16 Patapita nthawi, asilikali a mumsasawo anamva kuti: “Zimiri anakonzera chiwembu mfumu ndipo waipha.” Choncho tsiku limenelo, Aisiraeli onse omwe anali kumsasako anaveka ufumu Omuri,+ mkulu wa asilikali, kuti akhale mfumu ya Isiraeli. 17 Kenako Omuri ndi Aisiraeli onse amene anali naye, anachoka ku Gibitoni nʼkupita kukaukira mzinda wa Tiriza. 18 Zimiri ataona kuti mzindawo walandidwa, anakalowa munsanja yomwe inali panyumba ya mfumu nʼkuyatsa nyumbayo iye ali momwemo, moti anafa.+ 19 Anafa chifukwa cha machimo ake popeza anachita zoipa pamaso pa Yehova, anayenda mʼnjira ya Yerobowamu komanso chifukwa cha machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha iyeyo.+ 20 Nkhani zina zokhudza Zimiri ndi chiwembu chimene anakonza, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli.
21 Pa nthawi imeneyi mʼpamene anthu a ku Isiraeli anagawikana mʼmagulu awiri. Gulu lina linkatsatira Tibini mwana wa Ginati ndipo linkafuna kumuveka ufumu ndipo gulu linalo linkatsatira Omuri. 22 Koma anthu amene ankatsatira Omuri anagonjetsa amene ankatsatira Tibini mwana wa Ginati. Choncho Tibini anafa ndipo Omuri anakhala mfumu.
23 Omuri anakhala mfumu ya Isiraeli mʼchaka cha 31 cha Asa mfumu ya Yuda ndipo analamulira zaka 12. Ku Tiriza analamulirako zaka 6. 24 Iye anagula phiri la Samariya kwa Semeri ndi matalente* awiri asiliva ndipo anamanga mzinda paphiripo. Mzindawo anaupatsa dzina lakuti Samariya*+ lomwe linali dzina la Semeri, mwiniwake* wa phirilo. 25 Omuri anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ndipo anachita zoipa kwambiri kuposa mafumu onse amene anakhalapo iye asanakhale mfumu.+ 26 Iye anayenda mʼnjira zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati komanso mʼmachimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha iye pokwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mafano awo opanda pake.+ 27 Nkhani zina zokhudza Omuri, zimene anachita ndiponso mphamvu zake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 28 Kenako Omuri, mofanana ndi makolo ake, anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda ku Samariya ndipo mwana wake Ahabu+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.
29 Ahabu mwana wa Omuri anakhala mfumu ya Isiraeli mʼchaka cha 38 cha Asa mfumu ya Yuda. Iye analamulira Isiraeli ku Samariya+ kwa zaka 22. 30 Ahabu mwana wa Omuri anachita zoipa kwambiri pamaso pa Yehova kuposa mafumu onse amene anakhalapo iye asanakhale mfumu.+ 31 Ngati kuti kuyenda mʼmachimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati kunali kosakwanira, Ahabu anakwatira Yezebeli+ mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni,+ ndipo anayamba kutumikira Baala+ nʼkumamugwadira. 32 Kuwonjezera pamenepo, anamanga guwa lansembe la Baala mʼkachisi wa Baala+ amene iye anamanga ku Samariya. 33 Ahabu anaimikanso mzati wopatulika.*+ Iye anachita zinthu zambiri zokwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli kuposa mafumu onse a Isiraeli amene anakhalapo iye asanakhale mfumu.
34 Mʼmasiku ake, Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko. Atangoyala maziko ake, Abiramu mwana wake woyamba anafa, ndipo atangoika zitseko zake zapageti, Segubu mwana wake womaliza anafa. Izi zinachitika mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.+
17 Eliya*+ wa ku Tisibe, wochokera ku Giliyadi anauza Ahabu+ kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli amene ndimamʼtumikira, sikubwera mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”+
2 Kenako Eliya anamva mawu a Yehova akuti: 3 “Uchoke kuno nʼkulowera chakumʼmawa ndipo ukabisale mʼchigwa* cha Keriti chimene chili kumʼmawa kwa Yorodano. 4 Uzikamwa madzi mumtsinje umene uli mʼchigwacho ndipo ndidzalamula akhwangwala kuti azikakupatsa chakudya.”+ 5 Nthawi yomweyo, Eliya anachita zimene Yehova ananena. Anapita kukakhala mʼmbali mwa chigwa cha Keriti, chakumʼmawa kwa Yorodano. 6 Akhwangwala ankamubweretsera mkate ndi nyama mʼmawa ndi madzulo, ndipo iye ankamwa madzi mumtsinje umene unali mʼchigwacho.+ 7 Koma patapita masiku angapo,+ mtsinjewo unauma chifukwa mʼdzikomo simunkagwa mvula.
8 Kenako anamva mawu a Yehova akuti: 9 “Nyamuka, upite ku Zarefati mʼdziko la Sidoni ukakhale kumeneko. Ine ndikalamula mayi wamasiye kuti azikakupatsa chakudya.”+ 10 Choncho Eliya ananyamuka nʼkupita ku Zarefati. Atafika pageti la mzindawo anaona mayi wamasiye akutola nkhuni. Ndiyeno anamuitana nʼkumuuza kuti: “Mundipatseko madzi pangʼono mʼkapu kuti ndimwe.”+ 11 Atanyamuka kuti akatenge madziwo, anamuitananso nʼkumuuza kuti: “Mundibweretserekonso kamkate pangʼono.” 12 Atamva zimenezi mayiyo anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wanu wamoyo, ndilibe mkate, koma ufa pangʼono mumtsuko waukulu ndi mafuta pangʼono mumtsuko waungʼono.+ Panopa ndikutola tinkhuni kuti ndipite kukaphika chakudya choti ineyo ndi mwana wanga tidye. Tikadya, tiziyembekezera kufa.”
13 Ndiyeno Eliya anamuuza kuti: “Musaope. Pitani mukachite zimene mwanenazo. Koma pa zimene muli nazozo, mukayambe mwakonza kaye kamkate kozungulira nʼkundibweretsera. Kenako mukakonze chakudya chanu ndi mwana wanu. 14 Chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ufa umene uli mumtsuko waukulu suutha ndipo mafuta amene ali mumtsuko waungʼono saatha, mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula.’”+ 15 Choncho mayiyo anapita nʼkukachita zimene Eliya ananena. Ndipo iye, banja lake komanso Eliyayo anadya kwa masiku ambiri.+ 16 Ufa umene unali mumtsuko waukulu sunathe, ndipo mafuta amene anali mumtsuko waungʼono sanathe, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena kudzera mwa Eliya.
17 Kenako mwana wamwamuna wa mayiyo anadwala. Matenda ake anakula kwambiri mpaka anamwalira.+ 18 Zitatero, mayiyo anauza Eliya kuti: “Ndakulakwirani chiyani inu munthu wa Mulungu woona? Kodi mwabwera kudzandikumbutsa zimene ndinalakwitsa komanso kudzapha mwana wanga?”+ 19 Koma Eliya anamuuza kuti: “Bweretsani mwana wanuyo.” Ndiyeno anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayi ake nʼkupita naye kuchipinda chapadenga chimene Eliyayo ankakhala, ndipo anamugoneka pabedi lake.+ 20 Kenako anafuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga,+ kodi mukuchitiranso zoipa mayi wamasiye amene ndikukhala nayeyu pomuphera mwana wake?” 21 Ndiyeno anakumbatira mwanayo katatu ali pabedipo nʼkufuulira Yehova kuti: “Inu Yehova Mulungu wanga, chonde chititsani kuti moyo wa mwanayu ubwerere.” 22 Yehova anamva pemphero la Eliya+ ndipo moyo wa mwanayo unabwerera moti anakhalanso wamoyo.+ 23 Eliya anatenga mwanayo nʼkutsika naye kuchokera mʼchipinda chapadenga chija ndipo anapita naye kwa mayi ake. Ndiyeno anati: “Mwana wanu uja tsopano ali moyo.”+ 24 Mayiyo ataona zimenezi anauza Eliya kuti: “Tsopano ndadziwa kuti ndinudi munthu wa Mulungu+ ndipo mawu a Yehova amene mwanena ndi oona.”
18 Patapita nthawi, mʼchaka chachitatu,+ Eliya anamva mawu a Yehova akuti: “Pita ukaonekere kwa Ahabu, chifukwa ndikufuna kubweretsa mvula mʼdzikoli.”+ 2 Choncho Eliya anapita kukaonekera kwa Ahabu. Pa nthawiyi nʼkuti njala itafika poipa kwambiri+ ku Samariya.
3 Ahabu anaitana Obadiya, yemwe anali woyangʼanira banja la Ahabuyo. (Obadiya anali munthu woopa Yehova kwambiri. 4 Ndipo pamene Yezebeli+ ankapha aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri 100 nʼkuwagawa mʼmagulu awiri, gulu lililonse aneneri 50. Atatero anakawabisa kuphanga nʼkumawapatsa chakudya ndi madzi.) 5 Ndiyeno Ahabu anauza Obadiya kuti: “Pita mʼdzikoli, ukayendere akasupe onse a madzi ndi zigwa* zonse. Mwina tikhoza kupeza udzu wobiriwira woti tizidyetsa mahatchi ndi nyulu,* kuti ziweto zathuzi zisafe zonse.” 6 Choncho anagawana kopita. Ahabu analowera mbali ina ndipo Obadiya analowera mbali ina.
7 Obadiya akuyenda, anangoona Eliya akubwera kudzakumana naye. Nthawi yomweyo anamuzindikira ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi. Kenako ananena kuti: “Kodi ndinu mbuyanga Eliya?”+ 8 Iye anamuyankha kuti: “Inde ndi ineyo. Pita ukauze abwana ako kuti, ‘Eliya wabwera.’” 9 Koma Obadiya anati: “Kodi ine mtumiki wanu ndalakwa chiyani kuti mundipereke kwa Ahabu kuti andiphe? 10 Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wanu wamoyo, palibe mtundu kapena ufumu kumene abwana anga sanatumizeko anthu kuti akakufufuzeni. Akanena kuti, ‘Kuno kulibe,’ ankauza ufumuwo ndiponso mtunduwo kuti ulumbire kuti walepheradi kukupezani.+ 11 Ndiye mukundiuza kuti, ‘Pita ukauze abwana ako kuti: “Eliya wabwera”’? 12 Tikasiyana pano, mzimu wa Yehova ubwera nʼkukutengani+ kupita nanu kumalo amene ine sindingawadziwe. Ndiye ndikakauza Ahabu koma iyeyo osakupezani, adzandipha ndithu. Komatu ine mtumiki wanu ndakhala ndikuopa Yehova kuyambira ndili mwana. 13 Kodi inu mbuye wanga simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova? Ndinabisa aneneri 100 a Yehova mʼphanga. Ndinawagawa mʼmagulu awiri a aneneri 50 gulu lililonse ndipo ndinkawapatsa chakudya ndi madzi.+ 14 Ndiye pano mukunena kuti, ‘Pita, ukauze abwana ako kuti: “Eliya wabwera”’? Ndithu akandipha.” 15 Koma Eliya anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wamoyo amene ndimamʼtumikira, lero ndionekera kwa Ahabu.”
16 Choncho Obadiya anapita kwa Ahabu kukamuuza zimenezi ndipo Ahabuyo anapita kukakumana ndi Eliya.
17 Ahabu atangoona Eliya, anati: “Kodi ndiwe eti? Iwe ndi amene wabweretsa mavuto ambiri mu Isiraeli.”
18 Eliya anayankha kuti: “Ine sindinabweretse mavuto mu Isiraeli, koma inuyo ndi nyumba ya bambo anu. Chifukwa mwasiya kutsatira malamulo a Yehova nʼkuyamba kutsatira Abaala.+ 19 Tsopano sonkhanitsani Aisiraeli onse kuti ndikakumane nawo paphiri la Karimeli.+ Musonkhanitsenso aneneri 450 a Baala ndi aneneri 400 a mzati wopatulika,*+ amene amadya patebulo la Yezebeli.” 20 Choncho Ahabu anatumiza uthenga kwa Aisiraeli onse nʼkusonkhanitsanso aneneri paphiri la Karimeli.
21 Kenako Eliya anayandikira anthu onsewo nʼkunena kuti: “Kodi mukayikakayika mpaka liti?+ Ngati Yehova ali Mulungu woona mʼtsatireni,+ koma ngati Mulungu woona ndi Baala tsatirani ameneyo.” Koma anthuwo sanamuyankhe chilichonse. 22 Ndiyeno Eliya anauza anthuwo kuti: “Ndilipo ndekha mneneri wa Yehova amene watsala+ koma aneneri a Baala alipo 450. 23 Iwowo apeze ngʼombe zamphongo ziwiri zingʼonozingʼono. Asankhepo ngʼombe imodzi nʼkuiduladula. Ndiyeno aiike pankhuni koma asayatsepo moto. Ineyo ndikonza ngʼombe inayo nʼkuiika pankhuni, ndipo nanenso sindiyatsapo moto. 24 Kenako muitane dzina la mulungu wanu.+ Inenso ndiitana dzina la Yehova, ndipo Mulungu amene ayankhe potumiza moto asonyeza kuti ndi Mulungu woona.”+ Anthu onsewo atamva zimenezi anayankha kuti: “Zili bwino.”
25 Eliya anauza aneneri a Baala kuti: “Yambani ndinu kusankha ngʼombe imodzi nʼkuikonza chifukwa mulipo ambiri. Kenako muitane dzina la mulungu wanu koma musayatse moto.” 26 Choncho anatenga ngʼombe yaingʼono imene anapatsidwa nʼkuikonza ndipo kenako anayamba kuitana dzina la Baala kuyambira mʼmawa mpaka masana. Ankaitana kuti: “Inu a Baala, tiyankheni!” Koma sipanamveke mawu alionse ndipo palibe anayankha.+ Iwo anapitiriza kudumphadumpha uku akuzungulira guwa lansembe limene anamanga. 27 Pofika masana, Eliya anayamba kuwaseka nʼkumanena kuti: “Muitaneni mokuwa kwambiri chifukwa iye ndi mulungu.+ Mwina akuganizira zinazake kapena wapita kuchimbudzi.* Mwinanso wagona ndipo akufunika kumudzutsa.” 28 Iwo anayamba kuitana mokuwa kwambiri nʼkumadzichekacheka ndi mipeni ndi mikondo ingʼonoingʼono mogwirizana ndi mwambo wawo, mpaka magazi anayamba kuyenderera pamatupi awo. 29 Iwo anapitiriza kuchita ngati amisala* mpaka dzuwa linapendeka. Anapitirizabe mpaka nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo. Koma sipanamveke mawu alionse ndiponso palibe amene anayankha kapena kuwamvera.+
30 Patapita nthawi, Eliya anauza anthu onsewo kuti: “Bwerani pafupi.” Anthu onsewo anamuyandikira. Kenako iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linagumuka.+ 31 Eliya anatenga miyala 12 mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a ana a Yakobo, yemwe Yehova anamuuza kuti: “Dzina lako lidzakhala Isiraeli.”+ 32 Eliya anagwiritsa ntchito miyalayo nʼkumanga guwa lansembe+ kuti dzina la Yehova lilemekezedwe. Kenako anakumba ngalande kuzungulira guwa lansembe lonselo. Ngalandeyo kukula kwake inali ngati malo amene angafesepo mbewu zokwana miyezo iwiri ya seya.* 33 Atatero anayalapo nkhuni ndipo anaduladula ngʼombe yaingʼono yamphongo ija nʼkuiika pamwamba pa nkhunizo.+ Kenako anati: “Tungani madzi odzaza mitsuko 4 ikuluikulu ndipo muwathire pansembe yopserezayo ndiponso pankhunizo.” 34 Atatero anati: “Thirani madzi ena.” Anthuwo anathiradi. Anawauzanso kuti: “Thiraninso kachitatu.” Choncho anthuwo anathiranso kachitatu. 35 Madziwo anayenderera pansi ponse pa guwa lansembelo. Iye anathiranso madzi mʼngalande muja mpaka kudzaza.
36 Ndiyeno pa nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo,+ mneneri Eliya anayandikira guwa lansembelo nʼkunena kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu,+ Isaki+ ndi Isiraeli, lero zidziwike kuti inu ndinu Mulungu mu Isiraeli ndiponso kuti ine ndine mtumiki wanu, komanso kuti ndachita zonsezi potsatira mawu anu.+ 37 Ndiyankheni Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe kuti inu Yehova ndinu Mulungu woona ndiponso kuti mukubweza mitima yawo kuti abwerere kwa inu.”+
38 Atatero, moto wa Yehova unatsika nʼkutentha nsembe yopsereza ija,+ nkhuni, miyala ndi fumbi lomwe. Unaumitsanso madzi amene anali mʼngalande aja.+ 39 Anthu onsewo ataona zimenezo, nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi, ndipo ananena kuti: “Mulungu woona ndi Yehova! Mulungu woona ndi Yehova!” 40 Ndiyeno Eliya anauza anthuwo kuti: “Gwirani aneneri a Baala! Muonetsetse kuti pasapezeke wothawa!” Nthawi yomweyo anawagwira ndipo Eliya anatsetserekera nawo kumtsinje* wa Kisoni+ nʼkukawapha kumeneko.+
41 Kenako Eliya anauza Ahabu kuti: “Pitani mukadye ndi kumwa, chifukwa kukumveka mkokomo wa chimvula.”+ 42 Ahabu anapitadi kukadya ndiponso kukamwa. Koma Eliya anapita pamwamba pa phiri la Karimeli ndipo anagwada nʼkuika nkhope yake pakati pa mawondo ake.+ 43 Kenako anauza mtumiki wake kuti: “Pita ukayangʼane mbali yakunyanja.” Mtumikiyo anapita nʼkukayangʼanadi, ndiyeno anati: “Kulibe kalikonse.” Koma Eliya anamubweza nʼkumuuza kuti, “Pita ukayangʼanenso.” Anachita zimenezi mpaka maulendo 7. 44 Pa ulendo wa 7 mtumikiyo anati: “Ndaona kamtambo kakangʼono ngati dzanja la munthu ndipo kakukwera mʼmwamba kuchokera mʼnyanja.” Ndiyeno Eliya anauza mtumiki wakeyo kuti: “Pita ukauze Ahabu kuti, ‘Mangirirani mahatchi kugaleta ndipo munyamuke muzipita kuti chimvula chisakutsekerezeni.’” 45 Pa nthawiyi kumwamba kunachita mdima wa mitambo ndipo kunja kunayamba kuwomba mphepo. Kenako kunayamba kugwa chimvula chambiri.+ Ahabu anapitiriza ulendo wake pagaleta wopita ku Yezereeli.+ 46 Koma dzanja la Yehova linapatsa Eliya mphamvu, moti anakokera chovala chake nʼkuchimanga mʼchiuno ndipo anayamba kuthamanga nʼkupitirira Ahabu mpaka kukafika ku Yezereeli.
19 Kenako Ahabu+ anauza Yezebeli+ zonse zimene Eliya anachita ndiponso mmene anaphera aneneri onse ndi lupanga.+ 2 Yezebeli atamva zimenezo, anatuma munthu kwa Eliya kukamuuza kuti: “Milungu yanga indilange mowirikiza, ngati pofika nthawi ino mawa sindidzakhala nditakupha ngati mmene waphera aneneriwo.” 3 Choncho Eliya anachita mantha moti ananyamuka nʼkuyamba kuthawa kuti apulumutse moyo wake.+ Atafika ku Beere-seba+ wa ku Yuda,+ anasiya mtumiki wake kumeneko. 4 Ndipo iyeyo analowa mʼchipululu nʼkuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Kenako anafika pa kamtengo kenakake nʼkukhala pansi pake. Ndiyeno anapempha kuti afe ponena kuti: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga Yehova,+ chifukwa siine woposa makolo anga.”
5 Kenako anagona pansi pa kamtengo kaja mpaka tulo tinamʼpeza. Mwadzidzidzi kunabwera mngelo ndipo anamukhudza+ nʼkumuuza kuti: “Dzuka udye.”+ 6 Atayangʼana, anaona kuti kumutu kwake kuli mkate wozungulira pamiyala yotentha komanso jagi* ya madzi. Eliya anadya nʼkumwa ndipo anagonanso. 7 Patapita kanthawi, mngelo wa Yehova uja anabweranso nʼkumukhudza ndipo anamuuza kuti: “Dzuka udye, popeza ulendowu ukhala wautali.” 8 Choncho anadzuka ndipo anadya ndi kumwa. Atatero, anapeza mphamvu zokwanira moti anayenda masiku 40, masana ndi usiku, mpaka anakafika kuphiri la Mulungu woona la Horebe.+
9 Atafika kumeneko, analowa mʼphanga+ nʼkugona mmenemo usiku wonse. Kenako anamva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Ukudzatani kuno Eliya?” 10 Iye anayankha kuti: “Ine ndakutumikirani modzipereka kwambiri inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,+ koma Aisiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe ndipo apha aneneri anu ndi lupanga,+ moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+ 11 Koma Mulungu anati: “Tuluka, kaime paphiri pamaso pa Yehova.” Kenako Yehova anadutsa,+ ndipo kunawomba chimphepo champhamvu chomwe chinkangʼamba mapiri ndi kuphwanya matanthwe pamaso pa Yehova+ koma Yehova sanali mumphepoyo. Mphepoyo itatha kunachita chivomerezi,+ koma Yehova sanali mʼchivomerezicho. 12 Chivomerezicho chitatha kunabuka moto,+ koma Yehova sanali mʼmotowo. Motowo utatha, panamveka mawu achifatse apansipansi.+ 13 Eliya atangomva mawuwo, anaphimba nkhope yake ndi chovala chake+ ndipo anatuluka nʼkukaima pakhomo la phangalo. Kenako anamva mawu akuti: “Ukudzatani kuno Eliya?” 14 Iye anayankha kuti: “Ine ndakutumikirani modzipereka kwambiri inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, koma Aisiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe ndipo apha aneneri anu ndi lupanga, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+
15 Kenako Yehova anamuuza kuti: “Bwerera ndipo upite kuchipululu cha Damasiko. Ukakafika ukadzoze Hazaeli+ kuti akhale mfumu ya Siriya. 16 Ukadzozenso Yehu+ mdzukulu wa Nimusi kuti akhale mfumu ya Isiraeli ndipo Elisa,* mwana wa Safati wa ku Abele-mehola, ukamudzoze kuti adzakhale mneneri mʼmalo mwako.+ 17 Aliyense wothawa lupanga la Hazaeli,+ adzaphedwa ndi Yehu+ ndipo wothawa lupanga la Yehu, adzaphedwa ndi Elisa.+ 18 Ine ndasiya anthu 7,000 mu Isiraeli,+ amene mawondo awo sanagwadirepo Baala+ ndipo pakamwa pawo sipanakisepo Baala.”+
19 Choncho Eliya anachoka kumeneko nʼkupita kwa Elisa mwana wa Safati, ndipo anamʼpeza akulima ndi pulawo yokokedwa ndi ngʼombe ziwiri zamphongo. Panali mapulawo 12 ndipo pulawo yake inali kumbuyo. Choncho Eliya anapita pamene panali Elisa nʼkumuponyera chovala chake chauneneri.+ 20 Zitatero, Elisa anasiya ngʼombe zamphongozo nʼkuthamangira Eliya ndipo anamuuza kuti: “Ndiloleni ndipite ndikakise kaye bambo anga ndi mayi anga, kenako ndidzakutsatirani.” Eliya anamuyankha kuti: “Pita, sindingakuletse.” 21 Choncho anabwerera nʼkutenga ngʼombe zamphongo ziwiri zija nʼkuzipha.* Anatenga mitengo ya pulawoyo nʼkuphikira nyama ya ngʼombezo. Kenako anapatsa anthu kuti adye. Atatero, iye ananyamuka nʼkutsatira Eliya ndipo anayamba kumʼtumikira.+
20 Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya+ anasonkhanitsa asilikali ake onse. Atatero ananyamuka pamodzi ndi mafumu ena 32 ndi mahatchi komanso magaleta awo ndipo anapita kukazungulira mzinda+ wa Samariya+ nʼkuyamba kumenyana nawo. 2 Kenako anatumiza anthu mumzindawo kwa Ahabu+ mfumu ya Isiraeli, kuti akamuuze kuti: “Beni-hadadi wanena kuti, 3 ‘Siliva ndi golide wako akhala wanga ndipo akazi ako ndi ana ako aamuna abwino kwambiri, akhala anga.’” 4 Mfumu ya Isiraeli inayankha kuti: “Mogwirizana ndi mawu anu mbuyanga mfumu, ine ndi zanga zonse tili mʼmanja mwanu.”+
5 Kenako anthu aja anabweranso nʼkudzanena kuti: “Beni-hadadi wanena kuti, ‘Ndinakutumizira uthenga wakuti, “Undipatse siliva wako, golide wako, akazi ako ndi ana ako aamuna. 6 Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatumiza atumiki anga. Iwo adzafufuza paliponse mʼnyumba mwako ndi mʼnyumba za atumiki ako ndipo adzatenga zinthu zanu zonse zamtengo wapatali.”’”
7 Mfumu ya Isiraeli itamva mawu amenewa, inaitanitsa akulu onse amʼdzikolo nʼkuwauza kuti: “Munthuyu watsimikiza mtima kuti atibweretsere tsoka. Ananditumizira uthenga woti akufuna akazi anga, ana anga aamuna, siliva wanga ndi golide wanga, ndipo ine sindinamukanize.” 8 Koma akulu onsewo komanso anthu onse anauza mfumuyo kuti: “Musamvere zimenezo ndipo musalole.” 9 Choncho Ahabu anauza anthu amene anatumidwa ndi Beni-hadadi aja kuti: “Mukauze mbuyanga mfumu kuti, ‘Zonse zimene munandiuza poyamba, ine mtumiki wanu ndichita. Koma zimene mwanena kachiwirizi, sindingachite.’” Zitatero, anthuwo ananyamuka nʼkukapereka uthengawo kwa mfumu yawo.
10 Ndiyeno Beni-hadadi anatumizira Ahabu uthenga wakuti: “Milungu yanga indilange mowirikiza, ngati fumbi la ku Samariya lidzakwanire kuti anthu onse onditsatira apatsidwe lodzaza mʼmanja.” 11 Mfumu ya Isiraeli inayankha kuti: “Mukamuuze kuti, ‘Musayambe kudzitama nkhondo isanayambe ngati kuti mwapambana kale nkhondoyo.’”+ 12 Beni-hadadi anamva mawu amenewa pamene iye ndi mafumu amene anali naye ankamwa mowa mʼmatenti. Nthawi yomweyo, anauza antchito ake kuti: “Konzekerani nkhondo!” Choncho iwo anakonzekera kukamenyana ndi anthu amumzindawo.
13 Koma mneneri wina anapita kwa Ahabu+ mfumu ya Isiraeli nʼkumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Kodi waona chigulu chonsechi? Anthu onsewa ndiwapereka mʼmanja mwako lero ndipo udziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+ 14 Ahabu anafunsa kuti: “Adzagwiritsa ntchito ndani?” Mneneriyo anayankha kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndidzagwiritsa ntchito atumiki a akalonga oyangʼanira zigawo.’” Kenako Ahabu anafunsa kuti: “Ndani akayambitse nkhondoyo?” Mneneriyo anayankha kuti: “Inuyo.”
15 Ahabu anawerenga atumiki a akalonga oyangʼanira zigawo ndipo anakwana 232. Atamaliza, anawerenganso asilikali onse a Isiraeli ndipo analipo 7,000. 16 Iwo ananyamuka masana ndipo pa nthawiyo nʼkuti Beni-hadadi ndi mafumu ena 32 amene ankamuthandiza aja, akumwa mpaka kuledzera mʼmatenti. 17 Atumiki a akalonga oyangʼanira zigawo ndi amene anatsogola. Atangofika, Beni-hadadi anatumizako anthu ndipo anthuwo atabwerera anamuuza kuti: “Kwabwera anthu ochokera ku Samariya.” 18 Iye atamva anati: “Kaya abwerera mtendere kapena nkhondo, abweretseni amoyo.” 19 Koma atumiki a akalonga oyangʼanira zigawo komanso asilikali amene ankabwera mʼmbuyo mwawo atangotuluka mumzinda, 20 aliyense anayamba kupha mdani wake. Asiriyawo anayamba kuthawa+ ndipo Aisiraeli anawathamangitsa. Koma Beni-hadadi mfumu ya Siriya anathawa atakwera hatchi, pamodzi ndi amuna ena okwera pamahatchi. 21 Mfumu ya Isiraeli inapitiriza kuwatsatira nʼkumapha mahatchi ndi kuwononga magaleta awo ndipo inapha Asiriya ambiri.
22 Kenako mneneri uja+ anapita kwa mfumu ya Isiraeli nʼkunena kuti: “Pitani, kalimbitseni asilikali anu ankhondo ndi kuganizira zomwe mudzachite,+ chifukwa kumayambiriro kwa chaka chamawa mfumu ya Siriya idzabweranso kudzamenyana nanu.”+
23 Atumiki a mfumu ya Siriya anauza mfumuyo kuti: “Mulungu wawo ndi Mulungu wa mapiri, nʼchifukwa chake anatigonjetsa. Koma ngati titamenyana nawo pamalo afulati tikhoza kuwagonjetsa. 24 Komanso muchite izi: Muchotse mafumu onse+ pa maudindo awo ndipo muike abwanamkubwa mʼmalo mwawo. 25 Kenako musonkhanitse asilikali ndipo chiwerengero chawo chikhale chofanana ndi cha asilikali amene anafa aja. Chiwerengero cha mahatchi ndi magaleta chikhalenso chofanana ndi choyamba chija. Tikatero tikamenyane nawo pamalo afulati ndipo ndithu tikawagonjetsa.” Choncho mfumuyo inamvera malangizo awo ndipo inachitadi zimenezo.
26 Kumayambiriro kwa chaka, Beni-hadadi anasonkhanitsa Asiriya nʼkupita ku Afeki+ kuti akamenyane ndi Aisiraeli. 27 Nawonso Aisiraeli anasonkhana pamodzi ndipo anatenga zonse zofunikira nʼkupita kukakumana nawo. Aisiraeliwo atamanga msasa kutsogolo kwa Asiriya ankangooneka ngati timagulu tiwiri ta mbuzi, pamene Asiriyawo anadzaza dera lonselo.+ 28 Kenako munthu wa Mulungu woona uja anapita kwa mfumu ya Isiraeli nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Popeza Asiriya anena kuti: “Yehova ndi Mulungu wa mapiri, osati Mulungu wa zigwa,” ndipereka chigulu chonsechi mʼmanja mwako+ ndipo anthu inu mudziwadi kuti ine ndine Yehova.’”+
29 Magulu awiriwa anakhala moyangʼanizana mʼmisasa kwa masiku 7. Pa tsiku la 7 nkhondo inayambika ndipo Aisiraeli anapha asilikali oyenda pansi a Asiriya okwana 100,000 tsiku limodzi. 30 Asilikali otsalawo anathawira mumzinda wa Afeki+ ndipo khoma linagwera 27,000 mwa asilikali amenewa. Nayenso Beni-hadadi anathawa nʼkukafika mumzindawo ndipo anakabisala mʼchipinda chamkati.
31 Ndiyeno atumiki ake anamuuza kuti: “Tamva kuti mafumu a nyumba ya Isiraeli amakhala achifundo.* Tiyeni tivale ziguduli mʼchiuno nʼkumanga zingwe kumutu ndipo tipite kwa mfumu ya Isiraeli. Mwina sikakuphani.”+ 32 Choncho anavala ziguduli mʼchiuno nʼkumanga zingwe kumutu kwawo. Atatero anapita kwa mfumu ya Isiraeli nʼkunena kuti: “Kapolo wanu Beni-hadadi akupempha kuti, ‘Chonde musandiphe.’” Ahabu anati: “Kodi adakali ndi moyo? Amene ujatu ndi mʼbale wanga.” 33 Anthuwo anaona kuti chimenechi ndi chizindikiro choti zinthu zikhala bwino, ndipo nthawi yomweyo anaona kuti mfumuyo ikunenadi zochokera mumtima. Choncho anati: “Beni-hadadi ndi mʼbale wanu.” Ahabu atamva zimenezi anati: “Pitani mukamutenge.” Choncho Beni-hadadi anabwera kwa Ahabu ndipo Ahabu anauza anthu kuti akweze Beni-hadadi mʼgaleta.
34 Beni-hadadi anauza Ahabu kuti: “Ndibweza mizinda imene bambo anga analanda bambo anu ndipo mukhoza kukhazikitsa misika* ku Damasiko ngati mmene bambo anga anachitira ku Samariya.”
Ahabu anayankha kuti: “Tikapanga pangano loti zikhaladi chonchi, ndikusiya kuti uzipita kwanu.”
Atatero anachita naye pangano ndipo anamusiya kuti azipita.
35 Munthu wina yemwe anali mmodzi wa ana a aneneri,*+ pomvera mawu a Yehova anauza mnzake kuti: “Ndimenye!” Koma mnzakeyo anakana. 36 Choncho mneneriyo anauza mnzakeyo kuti: “Chifukwa sunamvere mawu a Yehova, tikasiyana mkango ukupha.” Atasiyana, mkango unabwera nʼkumupha mnzakeyo.
37 Ndiyeno anapita kwa munthu wina nʼkumuuza kuti: “Ndimenye!” Munthuyo anamʼmenyadi mpaka kumuvulaza.
38 Kenako mneneriyo anakaima mʼmbali mwa msewu nʼkumadikirira mfumu ija ndipo anali atadzimanga kansalu kumaso kuti asadziwike. 39 Pamene mfumu inkadutsa, mneneriyo anauza mfumuyo kuti: “Ine mtumiki wanu ndinapita pakatikati pa nkhondo. Kenako munthu wina anabwera nʼkundisungitsa munthu ndipo anandiuza kuti, ‘Uyangʼanire munthu uyu. Akangosowa, moyo wako ulowa mʼmalo mwa moyo wake,+ apo ayi ulipira siliva wolemera talente* imodzi.’ 40 Koma ine mtumiki wanu nditatanganidwa ndi zina, mwadzidzidzi munthu uja anasowa.” Pamenepo mfumu ya Isiraeliyo inamuuza kuti: “Chiweruzo chako nʼchomwecho. Wagamula wekha.” 41 Nthawi yomweyo, mneneriyo anachotsa kansalu kamene kanali kumaso kwake kaja, ndipo mfumu ya Isiraeliyo inamuzindikira kuti anali mmodzi wa aneneri.+ 42 Mneneriyo anauza mfumuyo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Chifukwa sunaphe munthu amene ndinanena kuti ayenera kuphedwa,+ moyo wako ulowa mʼmalo mwa moyo wake+ ndipo anthu ako alowa mʼmalo mwa anthu ake.’”+ 43 Mfumu ya Isiraeliyo itamva zimenezi, inanyamuka nʼkumapita kunyumba kwake ku Samariya+ ili yachisoni ndiponso yokhumudwa.
21 Kenako panachitika nkhani yokhudza munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezereeli. Mundawu unali ku Yezereeli,+ pafupi ndi nyumba yachifumu ya Ahabu mfumu ya Samariya. 2 Ahabu anauza Naboti kuti: “Ndipatse munda wako wa mpesawu kuti ndizilimamo masamba, chifukwa uli pafupi ndi nyumba yanga. Mʼmalo mwa munda wakowu ndikupatsa munda wina wa mpesa, wabwino kuposa umenewu. Kapena ngati ungafune, ndiugula ndi ndalama.” 3 Koma Naboti anayankha Ahabu kuti: “Ndikaiona nkhaniyi mmene Yehova akuionera, nʼkosayenera kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga.”+ 4 Choncho Ahabu analowa mʼnyumba mwake ali wachisoni ndiponso wokhumudwa chifukwa cha zimene Naboti wa ku Yezereeli anamuuza kuti: “Sindikupatsani cholowa cha makolo anga.” Ndiyeno anakagona pabedi lake nʼkuyangʼana kukhoma ndipo anakana kudya.
5 Kenako mkazi wake Yezebeli+ anabwera nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani simukusangalala komanso mukukana kudya?” 6 Ahabu anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chakuti ndinauza Naboti wa ku Yezereeli kuti, ‘Ndigulitse munda wako wa mpesa. Kapena ngati ukufuna, ndikupatsa munda wina wa mpesa mʼmalo mwa umenewu.’ Koma wandiyankha kuti, ‘Sindingakupatseni munda wanga wa mpesawu.’” 7 Ndiyeno Yezebeli anamuuza kuti: “Kodi siinu amene mukulamulira Aisiraeli? Dzukani mudye ndipo musangalale. Ineyo ndikupatsani munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezereeli.”+ 8 Choncho Yezebeli analemba makalata mʼdzina la Ahabu nʼkuwadinda ndi chidindo cha Ahabu.+ Kenako anatumiza makalatawo kwa akulu+ ndi anthu olemekezeka amumzinda umene Naboti ankakhala. 9 Mʼmakalatawo analembamo kuti: “Uzani anthu kuti asale kudya ndipo Naboti mumuike kutsogolo kwa anthu onse. 10 Ndiyeno mupeze anthu awiri opanda pake adzakhale kutsogolo kwake nʼkupereka umboni wotsutsana naye.+ Adzanene kuti, ‘Iwe wanyoza Mulungu ndi mfumu!’+ Kenako mukamutulutse kunja nʼkumuponya miyala kuti afe.”+
11 Choncho amuna a mumzinda umene Naboti ankakhala, akulu ndi anthu olemekezeka amumzindawo, anachita mogwirizana ndi zimene zinali mʼmakalata amene Yezebeli anawatumizira. 12 Iwo anauza anthu kuti asale kudya ndipo anaika Naboti kutsogolo kwa anthuwo. 13 Kenako amuna awiri opanda pake anabwera nʼkukhala kutsogolo kwa Naboti. Ndiyeno anayamba kupereka umboni wotsutsana ndi Naboti pamaso pa anthuwo. Iwo ananena kuti: “Naboti wanyoza Mulungu ndi mfumu!”+ Atatero anapita naye kunja kwa mzindawo nʼkukamuponya miyala mpaka kufa.+ 14 Kenako anatumiza uthenga kwa Yezebeli wakuti: “Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa.”+
15 Yezebeli atangomva kuti Naboti waponyedwa miyala ndipo wafa, anauza Ahabu kuti: “Pitani mukatenge munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezereeli+ umene anakana kukugulitsani uja, chifukwa Naboti panopa wafa.” 16 Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, anapita kukatenga munda wa mpesa wa Naboti wa ku Yezereeli kuti ukhale wake.
17 Koma Yehova anauza Eliya+ wa ku Tisibe kuti: 18 “Pita ku Samariya+ ukakumane ndi Ahabu mfumu ya Isiraeli. Iye ali mʼmunda wa mpesa wa Naboti ndipo akufuna kutenga mundawo kuti ukhale wake. 19 Ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi wapha munthu+ nʼkutenganso munda wake?”’+ Ukamuuzenso kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pamalo amene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo omwewo agalu adzanyambitanso magazi ako.”’”+
20 Ndiyeno Ahabu anafunsa Eliya kuti: “Wandipeza kodi mdani wanga?”+ Eliya anayankha kuti: “Inde ndakupezani. Mulungu wanena kuti, ‘Chifukwa watsimikiza mtima kuti uchite zoipa pamaso pa Yehova,+ 21 ndikubweretsera tsoka ndipo ndidzaseseratu nyumba yako ndi kupha mwamuna* aliyense wa mʼbanja la Ahabu,+ ngakhalenso ooneka onyozeka ndi ofooka mu Isiraeli.+ 22 Komanso ndidzachititsa nyumba yako kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati ndiponso nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya, chifukwa chakuti wandikwiyitsa ndiponso wachititsa kuti Aisiraeli achimwe.’ 23 Komanso ponena za Yezebeli, Yehova wanena kuti, ‘Agalu adzamudya Yezebeli mʼmunda wa ku Yezereeli.+ 24 Munthu aliyense wa mʼbanja la Ahabu wofera mumzinda, agalu adzamudya ndipo wofera kutchire, mbalame zidzamudya.+ 25 Palibenso munthu wina amene anatsimikiza mumtima mwake kuchita zoipa pamaso pa Yehova ngati Ahabu.+ Mkazi wake Yezebeli anamulimbikitsa kuchita zimenezo.+ 26 Ahabu anachita zinthu zonyansa kwambiri polambira mafano onyansa* ngati mmene Aamori onse anachitira, amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa Aisiraeli.’”+
27 Ahabu atangomva mawu amenewa, anangʼamba zovala zake nʼkuvala chiguduli. Iye anayamba kusala kudya, kugona pachiguduli ndipo ankayenda mwachisoni. 28 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Eliya wa ku Tisibe kuti: 29 “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga?+ Chifukwa wadzichepetsa pamaso panga, sindidzabweretsa tsokali iye adakali moyo. Mʼmalomwake, ndidzalibweretsa kwa anthu a mʼnyumba yake mʼnthawi ya mwana wake.”+
22 Kwa zaka zitatu, panalibe nkhondo pakati pa Siriya ndi Isiraeli. 2 Mʼchaka chachitatucho, Yehosafati+ mfumu ya Yuda anapita kwa mfumu ya Isiraeli.+ 3 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inafunsa atumiki ake kuti: “Kodi mukudziwa kuti mzinda wa Ramoti-giliyadi+ ndi wathu? Koma tikuzengereza kuulanda mʼmanja mwa mfumu ya Siriya.” 4 Kenako inafunsa Yehosafati kuti: “Kodi tipita limodzi kunkhondo ku Ramoti-giliyadi?” Yehosafati anayankha mfumu ya Isiraeliyo kuti: “Inu ndi ine ndife amodzi. Anthu anga ndi anthu anu ndi amodzi ndipo mahatchi anga nʼchimodzimodzi ndi mahatchi anu.”+
5 Koma Yehosafati anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Choyamba, mufunsire kaye+ kwa Yehova.”+ 6 Choncho mfumu ya Isiraeli inasonkhanitsa aneneri. Analipo amuna pafupifupi 400 ndipo inawafunsa kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena ndisapite?” Iwo anayankha kuti: “Pitani ndipo Yehova akapereka mzindawo kwa inu mfumu.”
7 Kenako Yehosafati anati: “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova? Ngati alipo, tiyeni tifunsirenso kwa Mulungu kudzera mwa iyeyo.”+ 8 Mfumu ya Isiraeli inayankha Yehosafati kuti: “Patsala munthu mmodzi amene tingathe kufunsira kwa Yehova+ kudzera mwa iye, koma ndimadana naye kwambiri,+ chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa zokhazokha.+ Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Koma Yehosafati anati: “Mfumu siyenera kulankhula choncho.”
9 Choncho mfumu ya Isiraeli inaitana nduna yapanyumba ya mfumu nʼkuiuza kuti: “Kamutenge Mikaya mwana wa Imula, ndipo ubwere naye mwamsanga.”+ 10 Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala pabwalo* lapageti lolowera mumzinda wa Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu atavala zovala zachifumu ndipo aneneri onse ankalosera pamaso pawo.+ 11 Ndiyeno Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndi nyanga izi mudzagunda Asiriya mpaka kuwapha onse.’” 12 Aneneri ena onse ankaloseranso zofanana ndi zimenezi. Ankanena kuti: “Pitani ku Ramoti-giliyadi ndipo mukapambana. Yehova akapereka mzindawo kwa inu mfumu.”
13 Munthu amene anatumidwa kukaitana Mikaya anauza Mikayayo kuti: “Aneneri onse alankhula zabwino kwa mfumu. Nawenso ukalankhule zabwino.”+ 14 Koma Mikaya anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, zimene Yehova angandiuze nʼzimene ndikanene.” 15 Kenako anafika kwa mfumu ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana ndipo Yehova akapereka mzindawo kwa inu mfumu.” 16 Ndiyeno mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti uzindiuza zoona zokhazokha mʼdzina la Yehova?” 17 Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika mʼmapiri+ ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe mtsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mwamtendere.’”
18 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Paja ndinakuuzani kuti, ‘Sadzalosera zabwino za ine, koma zoipa.’”+
19 Mikaya anati: “Choncho imvani mawu a Yehova: Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu+ ndipo gulu lonse lakumwamba linaimirira kumanja ndi kumanzere kwake.+ 20 Ndiyeno Yehova anati, ‘Ndani akapusitse Ahabu, kuti apite ku Ramoti-giliyadi nʼkukafa?’ Choncho angelo osiyanasiyana ankanena maganizo awo, wina izi, wina izi. 21 Kenako mngelo*+ wina anabwera kudzaima pamaso pa Yehova nʼkunena kuti, ‘Ine ndikamʼpusitsa.’ Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukamʼpusitsa bwanji?’ 22 Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse.’+ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukamʼpusitsadi ndipo zikakuyendera bwino. Pita ukachite zimenezo.’ 23 Choncho Yehova waika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anu onsewa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.”+
24 Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pomwe panali Mikaya nʼkumumenya mbama ndipo ananena kuti: “Zingatheke bwanji kuti mzimu wa Yehova undidutse nʼkukalankhula ndi iwe?”+ 25 Mikaya anayankha kuti: “Udzadziwa zimenezo tsiku limene udzalowe mʼchipinda chamkati kukabisala.” 26 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inati: “Mtengeni Mikaya mupite naye kwa Amoni mkulu wa mzinda ndi Yowasi mwana wa mfumu. 27 Mukawauze kuti, ‘Mfumu yanena kuti: “Mʼtsekereni munthu uyu.+ Muzimʼpatsa chakudya chochepa ndi madzi ochepa, mpaka nditabwerako mwamtendere.”’” 28 Koma Mikaya anati: “Mukakabwerakodi mwamtendere ndiye kuti Yehova sanalankhule nane.”+ Ananenanso kuti: “Anthu inu, mawu angawa muwakumbukire.”
29 Choncho mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.+ 30 Mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha kuti ndisadziwike ndipo ndimenya nawo nkhondo. Koma inuyo muvale zovala zanu zachifumu.” Choncho mfumu ya Isiraeli inadzisintha+ nʼkuyamba kumenya nawo nkhondo. 31 Mfumu ya Siriya inali italamula akuluakulu 32 oyangʼanira asilikali okwera magaleta kuti:+ “Musakamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya Isiraeli yokha basi.” 32 Akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Mfumu ya Isiraeli ija ndi imeneyi.” Choncho anatembenuka kuti amenyane naye ndipo Yehosafati anayamba kukuwa kuti anthu amuthandize. 33 Akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaletawo atangozindikira kuti si mfumu ya Isiraeli, anasiya kumuthamangitsa nʼkubwerera.
34 Koma munthu wina anaponya muvi wake chiponyeponye ndipo unakabaya mfumu ya Isiraeli pamalo olumikizira a chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti: “Bwera udzanditulutse mʼbwalo lankhondoli chifukwa ndavulala kwambiri.”+ 35 Nkhondoyo inafika poopsa tsiku limenelo ndipo mfumuyo anaiimiritsa mʼgaleta nʼkuitsamiritsa kugaletalo moyangʼanizana ndi Asiriya. Magazi ochokera pamene anaibaya paja ankayenderera mʼgaletamo ndipo kenako inafa madzulo.+ 36 Dzuwa litatsala pangʼono kulowa, mumsasamo analengeza kuti: “Aliyense azipita mumzinda wake ndi kudziko lake!”+ 37 Choncho mfumuyo inafa ndipo anaibweretsa ku Samariya nʼkuiika mʼmanda ku Samariyako. 38 Atayamba kutsuka galeta lankhondolo padziwe la ku Samariya, lomwe mahule ankasambapo, agalu anayamba kunyambita magazi a mfumuyo mogwirizana ndi mawu amene Yehova ananena.+
39 Nkhani zina zokhudza Ahabu, zonse zimene anachita, nyumba yaminyanga ya njovu+ imene anamanga komanso mizinda yonse imene anamanga, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 40 Choncho Ahabu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira+ ndipo mwana wake Ahaziya+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.
41 Yehosafati+ mwana wa Asa anakhala mfumu ya Yuda mʼchaka cha 4 cha Ahabu mfumu ya Isiraeli. 42 Yehosafati anali ndi zaka 35 pamene ankakhala mfumu ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Mayi ake dzina lawo linali Azuba mwana wa Sili. 43 Yehosafati anapitiriza kuyenda mʼnjira zonse za Asa,+ bambo ake. Sanasiye kuyenda mʼnjirazo ndipo anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Koma sanachotse malo okwezeka ndipo anthu ankaperekabe nsembe zautsi komanso nsembe zina mʼmalo okwezekawo.+ 44 Yehosafati ankakhala mwamtendere ndi mfumu ya Isiraeli.+ 45 Nkhani zina zokhudza Yehosafati, mphamvu zake ndiponso mmene anamenyera nkhondo, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 46 Yehosafati anachotsanso mʼdzikolo mahule aamuna apakachisi+ amene anatsala pa nthawi ya Asa bambo ake.+
47 Pa nthawiyo ku Edomu+ kunalibe mfumu. Nduna ndi imene inkalamulira ngati mfumu.+
48 Yehosafati anapanga zombo* za ku Tarisi kuti zizipita ku Ofiri kukatenga golide.+ Koma sizinapite chifukwa zinasweka ku Ezioni-geberi.+ 49 Pa nthawi imeneyi mʼpamene Ahaziya mwana wa Ahabu anapempha Yehosafati kuti: “Bwanji antchito anga apite limodzi ndi antchito anu mʼzombozo?” Koma Yehosafati anakana.
50 Kenako Yehosafati, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake+ mu Mzinda wa Davide kholo lake. Ndiyeno mwana wake Yehoramu+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.
51 Ahaziya+ mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya Yuda ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 52 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira ya bambo ake+ ndi mayi ake+ ndiponso mʼnjira ya Yerobowamu mwana wa Nebati, amene anachititsa kuti Aisiraeli achimwe.+ 53 Ahaziya anapitiriza kutumikira Baala+ komanso kumugwadira. Anapitiriza kukwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli+ ngati mmene anachitira bambo ake.
Ena amati “mahosi.”
Kapena kuti, “sanafune kumukhumudwitsa.”
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
Kapena kuti, “Zikhale momwemo!”
Kapena kuti, “Ukatero udzachita zinthu mwanzeru.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchoonadi.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anagona limodzi ndi makolo ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aakulu.”
Mabaibulo ena amati, “ovutawa.” Mʼchilankhulo choyambirira, “olemerawa.”
Kapena kuti, “zotchingira zamkuwa.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Nambalayi imapezeka mʼmipukutu ina komanso munkhani zina. Koma mipukutu ina imati 40,000.
Kapena kuti, “komanso amuna okwera pamahatchi.”
Nʼkutheka kuti zikuphatikizaponso tizilombo touluka.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anaika adani akewo pansi pa mapazi ake.”
Mitengo ya junipa ndi yofanana ndi mitengo ya mkungudza.
Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B8.
Onani Zakumapeto B15.
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira,“kachisi wa nyumba.”
Apa akunena za Malo Oyera.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanja.”
Mitengo ya junipa ndi yofanana ndi mitengo ya mkungudza.
Amenewa ndi Malo Oyera amene anali kutsogolo kwa Malo Oyera Koposa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtengo wa mafuta.”
Amenewa anali Malo Oyera Koposa.
Apa akunena za Malo Oyera.
Onani Zakumapeto B15.
Onani Zakumapeto B15.
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Kapena kuti, “zamkuwa.”
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Apa akunena za Malo Oyera.
Kapena kuti, “yakumʼmwera.”
Kutanthauza “Iye [Yehova] Akhazikitse.”
Kapena kuti, “yakumpoto.”
Nʼkutheka kuti dzinali likutanthauza “Mu Mphamvu.”
Kapena kuti, “anapanga nyanja yachitsulo chosungunula.”
Pafupifupi masentimita 7.4. Onani Zakumapeto B14.
Mtsuko umodzi unkakwana malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “zingelengele zake.”
Chimenechi ndi Chikondwerero cha Misasa.
Onani Zakumapeto B15.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wotuluka mʼchiuno mwako.”
Kapena kuti, “nʼkutemberera.” Limeneli ndi lumbiro limene linkachititsa kuti munthu atembereredwe ngati walumbira monama kapena ngati sanakwaniritse zomwe walumbirazo.
Kapena kuti, “mbiri yanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkono wanu wotambasula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Maso anu aone pempho.”
Kapena kuti, “lamkuwa.”
Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “la 8.” Limeneli linali tsiku la 8, atatha masiku 7 achiwiri aja.
Mabaibulo ena amati, “Dziko Lopanda Pake.”
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Kapena kuti, “Milo.” Amenewa ndi mawu a Chiheberi otanthauza “kudzaza.”
Kapena kuti, “Milo.” Amenewa ndi mawu a Chiheberi otanthauza “kudzaza.”
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Nthawi zambiri amene ankanyamula zishango zimenezi anali oponya mivi.
“Mina” yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi inkalemera magalamu 570. Onani Zakumapeto B14.
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
Kapena kuti, “amuna okwera pamahatchi.”
Kapena kuti, “amuna okwera pamahatchi.”
Mabaibulo ena amati, “kuchokera ku Iguputo ndi ku Kuwe. Amalonda a mfumu ankawagula ku Kuwe,” mwina kutanthauza ku Kilikiya.
Kapena kuti, “akazi akewo ankamusokoneza kwambiri.”
Mabaibulo ena amati: “anamusiyitsa kuyamwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “atapha.”
Kapena kuti, “Milo.” Amenewa ndi mawu a Chiheberi otanthauza “kudzaza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anagona limodzi ndi makolo ake.”
Kapena kuti, “akulu.”
Kapena kuti, “akuluwo.”
Kapena kuti, “malangizo a akulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumatenti.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ochita kusankhidwa.”
Kapena kuti, “analimbitsa mpanda wa.”
Kapena kuti, “nʼkupita kukalimbitsa mpanda wa.”
Kapena kuti, “phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.”
Kapena kuti, “Umuuze zakutizakuti.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wokodzera khoma.” Amenewa ndi mawu onyoza a Chiheberi otanthauza mwamuna.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “zamkuwa.”
Kapena kuti, “asilikali othamanga.”
Ankadziwikanso kuti Abiya.
Mawu ake a Chiheberi amatanthauzanso “ndowe,” ndipo amagwiritsidwa ntchito ngati mawu onyoza.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kumanganso mzinda wa Rama kuti ukhale wolimba.”
Kapena kuti, “imene anaimanganso kuti ikhale yolimba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wokodzera khoma.” Amenewa ndi mawu onyoza a Chiheberi otanthauza mwamuna.
Kapena kuti, “kaya amene akanatha kubwezera magazi ake.”
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Kutanthauza, “La Banja la Semeri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbuye.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza “Mulungu wanga ndi Yehova.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “kapena wachokapo.”
Kapena kuti, “kuchita ngati aneneri.”
Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita 7.33. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “kuchigwa.”
Kapena kuti, “chikho.”
Kutanthauza “Mulungu Ndi Chipulumutso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuzipereka nsembe.”
Kapena kuti, “amakhala ndi chikondi chokhulupirika.”
Kapena kuti, “kukhazikitsa misewu.”
Mawu akuti “ana a aneneri” mwina akutanthauza sukulu yopereka malangizo kwa aneneri, kapena kagulu ka aneneri.
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wokodzera khoma.” Amenewa ndi mawu onyoza a Chiheberi otanthauza mwamuna.
Mawu ake a Chiheberi amatanthauzanso “ndowe,” ndipo amagwiritsidwa ntchito ngati mawu onyoza.
Mʼchilankhulo choyambirira, “popunthira mbewu.”
Kapena kuti, “mzimu.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.