Lachinayi, April 16
Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova, . . . ndipo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.—Sal. 18:6.
Mfumu Davide ankadziwa Yehova ndipo ankamudalira. Pamene Mfumu Sauli komanso adani ake ankafuna kumupha, Davide anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Mulungu atayankha pemphero lake n’kumupulumutsa, Davide ananena kuti: “Yehova ndi wamoyo.” (Sal. 18:46) Polankhula mawu amenewa, Davide sankatanthauza kuti ankangodziwa kuti Mulungu aliko. Buku lina linanena kuti Davide ankakhulupirira kuti Yehova “ndi Mulungu wamoyo yemwe nthawi zonse amathandiza anthu ake.” Zimene zinachitika pa moyo wa Davide zinamutsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo ndipo zinamulimbikitsa kuti apitirize kumutumikira komanso kumutamanda. (Sal. 18:28, 29, 49) Kukhulupirira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo kungatithandize kuti tizimutumikira ndi mtima wonse. Tidzapeza mphamvu kuti tizipirira mayesero komanso tizichita zambiri pomutumikira. Tidzakhalanso ofunitsitsa kupitiriza kukhala naye pa ubwenzi. w24.06 25:3-4
Lachisanu, April 17
Musalole kuti aliyense akusocheretseni.—2 Ates. 2:3.
Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a mtumwi Paulo opita kwa Atesalonika? Tikamva zinazake zomwe sizikugwirizana ndi zomwe timaphunzira m’Baibulo kapenanso mphekesera, tiyenera kuchita zinthu mwanzeru. M’dziko lomwe poyamba linkatchedwa Soviet Union, adani athu anafalitsa kalata yooneka ngati ikuchokera kulikulu lathu. Kalatayo inalimbikitsa abale ena kuti apange kagulu kena kapadera koima pakokha. Kalatayo inkaoneka ngati yachokeradi kulikulu lathu. Koma abale okhulupirika sanapusitsidwe. Iwo anazindikira kuti uthenga wa m’kalatayo sunkagwirizana ndi zomwe akhala akuphunzitsidwa. Masiku anonso adani athu amagwiritsa ntchito njira zamakono pofuna kutisokoneza kapena kutichititsa kuti tisamagwirizane. M’malo molola kuti wina aliyense “asinthe maganizo [athu]” omwe ndi olondola, tingadziteteze poganizira mosamala ngati zimene tamva kapena kuwerenga zikugwirizana ndi mfundo za choonadi zomwe tikuzidziwa kale.—2 Ates. 2:2; 1 Yoh. 4:1. w24.07 28:14-15
Loweruka, April 18
Wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza.—1 Yoh. 2:1.
Nkhani yofunika kwambiri imene aliyense afunika kusankha ndi yokhudza kudzipereka kwa Yehova n’kukhala m’banja la anthu amene amamulambira. Yehova amafuna kuti munthu aliyense achite zimenezi. Chifukwa chiyani? Iye amafuna kuti akhale nawo pa ubwenzi komanso apeze moyo wosatha. (Deut. 30:19, 20; Agal. 6:7, 8) Koma Yehova sakakamiza anthu kuti azimutumikira. Amafuna kuti aliyense azisankha yekha zimene akufuna kuchita. Kodi chimachitika n’chiyani ngati Mkhristu wobatizidwa waphwanya lamulo la Mulungu n’kuchita tchimo lalikulu? Ngati sangalape, ayenera kuchotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:13) Komabe ngakhale zili choncho, Yehova amayembekezera kuti munthu amene wachita zoipayo adzabwerera kwa iye. Ndipotu n’chifukwa chake anapereka dipo kuti anthu ochimwa amene alapa azikhululukidwa. Mulungu wathu wachikondi amapempha anthu amene achita tchimo kuti alape.—Zek. 1:3; Aroma 2:4; Yak. 4:8. w24.08 33:1-2